[1] Kenaka Yehova anati kwa Mose,
[2] “Imika chihema, tenti ya msonkhano, tsiku loyamba la mwezi.
[3] Uyikemo bokosi la umboni ndipo uphimbe bokosilo ndi katani.
[4] Ulowetsemo tebulo ndi kuyika zimene zimakhala pamenepo. Kenaka ulowetse choyikapo nyale ndipo uyikepo nyale zake.
[5] Uyike guwa lofukiza la golide patsogolo pa bokosi la umboni ndipo uyike katani ya pa chipata cha chihema.
[6] “Uyike guwa lansembe yopsereza patsogolo pa chipata cha chihema, tenti ya msonkhano.
[7] Uyike beseni pakati pa tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe ndipo uyikemo madzi.
[8] Upange bwalo lozungulira chihemacho ndipo uyike katani ya pa chipata cha bwalolo.
[9] “Utenge mafuta wodzozera ndipo udzoze chihema ndi chilichonse chili mʼmenemo ndipo zidzakhala zoyeretsedwa.
[10] Kenaka udzoze guwa lansembe lopsereza ndi ziwiya zake zonse. Ulipatule guwalo ndipo lidzakhala loyera kwambiri.
[11] Udzoze beseni ndi miyendo yake ndipo uzipatule.
[12] “Ubwere ndi Aaroni ndi ana ake pa chipata cha tenti ya msonkhano ndipo uwasambitse ndi madzi.
[13] Kenaka umuveke Aaroni zovala zopatulika, umudzoze ndi kumupatula kotero kuti athe kunditumikira monga wansembe.
[14] Ubweretse ana ake ndipo uwaveke minjiro.
[15] Uwadzoze monga momwe unadzozera abambo awo, kotero kuti anditumikire monga ansembe. Kudzozedwako kudzakhala unsembe wawo pa mibado ndi mibado”
[16] Mose anachita zonse monga Yehova anamulamulira.
[17] Kotero anayimika chihema tsiku loyamba la mwezi woyamba mʼchaka chachiwiri.
[18] Nthawi imene Mose anayimika chihema, anayika matsinde mʼmalo ake, kuyimitsa maferemu, kulowetsa mitanda ndi kuyika nsichi.
[19] Kenaka anayika tenti pamwamba pa chihema ndipo anayika chophimba pa tenti monga momwe Yehova analamulira Mose.
[20] Iye anatenga miyala ya umboni nayika mʼbokosi lija ndi kuyika chivundikiro pamwamba pake.
[21] Kenaka analowetsa bokosilo mʼchihema ndipo anapachika katani ndi kubisa bokosi la umboni monga momwe Yehova analamulira iye.
[22] Mose anayika tebulo mu tenti ya msonkhano kumpoto kwa chihema, kunja kwa katani,
[23] ndipo anayikapo buledi pamaso pa Yehova, monga momwe Yehova analamulira Mose.
[24] Iye anayikanso choyikapo nyale mu tenti ya msonkhano moyangʼanana ndi tebulo mbali yakummwera kwa chihema.
[25] Ndipo anayikapo nyale zija pamaso pa Yehova, monga Yehova analamulira Mose.
[26] Mose anayika guwa la golide mu tenti ya msonkhano patsogolo pa katani
[27] ndipo anapserezapo lubani wonunkhira monga Yehova anamulamulira.
[28] Kenaka anayika katani ya pa chipata cha chihema.
[29] Iye anayika guwa lansembe yopsereza pafupi ndi chipata cha chihema, tenti ya msonkhano, ndipo anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe ya ufa monga Yehova anamulamulira.
[30] Iye anayika beseni pakati pa tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe ndipo anathiramo madzi wosamba,
[31] ndipo Mose, Aaroni ndi ana ake amasamba manja ndi mapazi awo.
[32] Iwo amasamba nthawi zonse akamalowa mu tenti ya msonkhano kapena kuyandikira guwa lansembe monga Yehova analamulira Mose.
[33] Kenaka Mose anamanga bwalo kuzungulira chihema ndi guwa lansembe ndipo anayika katani ya pa chipata cha bwalo. Kotero Mose anamaliza ntchito.
[34] Kenaka mtambo unaphimba tenti ya msonkhano, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho.
[35] Mose sanathe kulowa mu tenti ya msonkhano chifukwa mtambo unali utakhazikika pa chihemacho, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho.
[36] Pa maulendo awo onse, mtambo ukachoka pamwamba pa chihema, Aisraeli ankasamukanso pamene analipo.
[37] Koma ngati mtambo sunachoke, iwo sankasamukanso mpaka tsiku limene udzachoke.
[38] Kotero mtambo wa Yehova unkakhala pamwamba pa chihema usana, ndi mtambo wamoto umakhala usiku, pamaso pa nyumba yonse ya Israeli pa masiku onse aulendo wawo.