Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 6:51

[1] Ndipo Mose ndi Aisraeli anayimbira Yehova nyimbo iyi: “Ine ndidzayimbira Yehova pakuti wakwezeka mʼchigonjetso. Kavalo ndi wokwera wake, Iye wawaponya mʼnyanja.

[2] Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; ndiye chipulumutso changa. Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamutamanda, Mulungu wa makolo anga, ine ndidzamukweza.

[3] Yehova ndi wankhondo; Yehova ndilo dzina lake.

[4] Magaleta a Farao ndi asilikali ake ankhondo Iye wawaponya mʼnyanja. Akatswiri ankhondo amphamvu a Farao amizidwa mʼNyanja Yofiira.

[5] Nyanja yakuya inawaphimba; Iwo anamira pansi ngati mwala.”

[6] Yehova, dzanja lanu lamanja ndi laulemerero chifukwa cha mphamvu zake. Ndithu Yehova, dzanja lanu lamanja linaphwanya mdani.

[7] Ndi ulemerero wanu waukulu, munagonjetsa okutsutsani. Inu munatumiza mkwiyo wanu waukulu; ndipo unawapsereza ngati udzu.

[8] Ndi mpweya wotuluka mʼmphuno mwanu madzi anawunjikana pamodzi. Nyanja yakuya ija inasanduka madzi owuma gwaa kufika pansi.

[9] Mdaniyo anati, “Ine ndidzawalondola, ndipo ndidzawagwira. Ndidzagawa chuma chawo; ndiye chokhumba changa chidzakwaniritsidwa. Ine ndidzasolola lupanga langa, ndi mkono wanga ndidzawawononga.”

[10] Koma Inu munawuzira mphepo yanu, ndipo nyanja inawaphimba. Iwo anamira ngati chitsulo mʼmadzi amphamvu.

[11] Ndithu Yehova, pakati pa milungu, ndani afanana nanu? Inu amene muli woyera, ndiponso wotamandika wolemekezeka, chifukwa cha ntchito zanu, zazikulu ndi zodabwitsa?

[12] Munatambasula dzanja lanu lamanja ndipo dziko linawameza.

[13] Ndi chikondi chanu chosasinthika mudzatsogolera anthu amene munawawombola. Ndi mphamvu zanu munawatsogolera ku malo anu woyera.

[14] Anthu amitundu ina anamva za mbiriyi ndipo ananjenjemera ndi mantha, mantha woopsa agwira anthu a dziko la Filisiti.

[15] Tsopano mafumu a ku Edomu agwidwa ndi mantha aakulu, otsogolera a dziko la Mowabu akunjenjemera ndi mantha, ndipo anthu a ku Kanaani asungunuka ndi mantha.

[16] Onse agwidwa ndi mantha woopsa. Popeza anaona mphamvu zanu zazikulu, iwo ayima chilili ngati mwala mpaka anthu anu, Inu Yehova atadutsa; inde mpaka atadutsa anthu amene munawagula.

[17] Inu mudzawalowetsa ndi kuwakhazikitsa pa phiri lanu. Pa malo pamene Inu Yehova munawapanga kuti muzikhalapo; malo wopatulika amene Inu Ambuye munawakonza ndi manja anu.

[18] “Yehova adzalamula mpaka muyaya.”

[19] Akavalo a Farao, magaleta ndi oyendetsa akavalo atalowa mʼnyanja, Yehova anawabwezera madziwo mʼnyanja ndi kuwamiza, koma Aisraeli anawoloka nyanjayo powuma.

[20] Ndipo Miriamu mneneri wamkazi, mlongo wa Aaroni anatenga zoyimbira ndipo akazi onse anamutsatira pambuyo, akuyimba ndi zoyimbira ndi kuvina.

[21] Miriamu anawayimbira nyimbo iyi: “Imbirani Yehova, chifukwa iye wapambana. Kavalo ndi wokwerapo wake Iye wawamiza mʼnyanja.”

[22] Ndipo Mose anatsogolera Israeli kuchoka ku nyanja yofiira ndi kupita ku chipululu cha Suri. Anayenda mʼchipululu masiku atatu wosapeza madzi.

[23] Ndipo anafika ku Mara. Koma sanathe kumwa madzi akumeneko chifukwa anali owawa. (Ndi chifukwa chake malowo amatchedwa Mara).

[24] Tsono anthu aja anadandaulira Mose ndi kumufunsa kuti, “Kodi tikumwa chiyani?”

[25] Ndipo Mose anapemphera kwa Yehova, ndipo Yehova anamuonetsa kamtengo. Iye anakaponya mʼmadzimo ndipo madzi anakhala abwino. Kumeneko Yehova anawayikira lamulo ndi maweruziro. Kumenekonso Yehova anawayesa.

[26] Yehova anati, “Ngati inu mudzamvetsa bwino mawu anga, kuchita zolungama, kumvera malamulo anga ndi kusamalitsa zimene ndikukuwuzani ndiye kuti Ine sindidzayika pa inu matenda amene ndinayika pa anthu a ku Igupto popeza ndine Yehova amene ndimakuchiritsani.”

[27] Kenaka anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe khumi ndi awiri ndi mitengo ya migwalangwa makumi asanu ndi awiri, ndipo anamanga misasa yawo kumeneko pafupi ndi madzi.

Eksodo — Chapters