Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 6:47

[1] Yetero wansembe wa ku Midiyani amenenso anali mpongozi wa Mose, anamva zonse zimene Mulungu anachitira Mose ndi anthu ake a Aisraeli ndi mmene Yehova anawatulutsira mʼdziko la Igupto.

[2] Mose atamubweza Zipora, mkazi wake, Yetero, mpongozi wake anamulandira

[3] mwana wake wamkaziyo pamodzi ndi ana ake aamuna awiri. Mose anamupatsa mwana wachisamba dzina loti Geresomu popeza anati, “Ndakhala mlendo mʼdziko lachilendo.”

[4] Ndipo mwana wake wachiwiri anamupatsa dzina loti Eliezara, pakuti anati, “Mulungu wa makolo anga anali thandizo langa. Iye anandipulumutsa ku lupanga la Farao.”

[5] Yetero, mpongozi wa Mose pamodzi ndi ana a Mose aamuna awiri ndi mkazi wake anabwera kwa Mose ku chipululu pa phiri la Mulungu kumene Mose anamanga misasa.

[6] Yetero anali atatumiza uthenga kwa Mose kuti, “Ine Yetero, mpongozi wako, ndikubwera ndi mkazi wako ndi ana ake awiri.”

[7] Kotero Mose anatuluka kukakumana ndi mpongozi wake ndipo anawerama ndi kupsompsona. Atalonjerana anakalowa mu tenti

[8] Mose anafotokozera mpongozi wake zonse zimene Yehova anamuchita Farao ndi Aigupto chifukwa cha Israeli komanso zowawa zonse anakumana nazo mʼnjira. Mose anafotokozanso momwe Yehova anawapulumutsira.

[9] Yetero anakondwa kwambiri atamva zabwino zonse zimene Yehova anachitira Aisraeli powapulumutsa mʼdzanja la Aigupto.

[10] Iye anati, “Alemekezeke Yehova amene wakupulumutsani mʼdzanja la Aigupto ndi Farao. Wapulumutsanso anthuwa mʼdzanja la Aigupto.

[11] Tsopano ndikudziwa kuti Yehova ndi wopambana milungu ina yonse, pakuti anachita izi kwa amene ananyoza Israeli.”

[12] Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Mulungu. Aaroni ndi akuluakulu onse a Israeli anabwera kudzadya chakudya pamodzi ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu.

[13] Mmawa mwake, Mose anakhala pa mpando kuti aweruze milandu ya anthu. Anthu anayima momuzungulira kuyambira mmawa mpaka madzulo.

[14] Mpongozi wa Mose ataona zonse zimene iye amawachitira anthu anati, “Nʼchiyani chimene mukuwachitira anthuwa? Nʼchifukwa chiyani mulipo nokha woweruza, pamene anthu onsewa ayimirira kuyambira mmawa mpaka madzulo?”

[15] Mose anamuyankha kuti, “Chifukwa anthuwa anabwera kwa ine kudzafunsa zimene Mulungu akufuna.

[16] Ngati munthu akangana ndi mʼbale wake, onse awiri amabwera kwa ine, ndipo ine ndimawaweruza. Ndimawawuzanso malamulo a Mulungu ndi malangizo ake.”

[17] Mpongozi wa Mose anayankha kuti, “Zimene mukuchitazi si zabwino.

[18] Ntchitoyi ndi yayikulu kuposa mphamvu zanu. Inu simungathe kuyigwira nokha. Inu pamodzi ndi anthuwa amene amabwera kwa inu mudzatopa.

[19] Tsono tamverani ndikulangizeni, ndipo Mulungu akhale nanu. Inu muziwayimirira anthuwa pamaso pa Mulungu, ndipo mikangano yawo muzibwera nayo kwa Iye.

[20] Aphunzitseni mawu ndi malangizo a Mulungu. Aphunzitseni mmene ayenera kukhalira ndi zimene ayenera kuchita.

[21] Koma sankhani amuna odziwa ntchito yawo, anthu owopa Mulungu, anthu odalirika amene amadana ndi kupeza phindu mwachinyengo. Tsono muwayike kuti akhale oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50 ndi ena a anthu khumi.

[22] Tsono amenewa aziweruza anthu nthawi zonse. Mlandu uliwonse waukulu azibwera nawo kwa inu, koma mlandu waungʼono aziweruza okha. Izi zidzachititsa kuti ntchito yanu ipepuke, popeza mudzagwira ntchito mothandizana.

[23] Ngati mutsatira malangizowa monga mmene Mulungu wakulamulirani ndiye kuti simudzafowoka ndipo anthu onsewa adzapita kwawo mu mtendere.”

[24] Mose anamvera mpongozi wake ndi kuchita zonse zimene iye ananena.

[25] Iye anasankha amuna odziwa bwino ntchito zawo ndipo anawayika kuti akhale atsogoleri, oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 500, ena a anthu makumi asanu ndi ena a anthu khumi.

[26] Iwowa ankaweruza anthu nthawi zonse. Milandu yovuta ankabwera nayo kwa Mose, koma yosavuta ankayiweruza okha.

[27] Kenaka Mose analola kuti mpongozi wake, Yetero anyamuke kubwerera ku dziko la kwawo.

Eksodo — Chapters