[1] Kenaka Yehova anati kwa Mose,
[2] “Uza Aisraeli abwerere ndi kukagona pafupi ndi Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja. Inu mumange zithando mʼmbali mwa nyanja moyangʼanana ndi Baala-Zefoni.
[3] Farao adzaganiza kuti ‘Aisraeli asokonezeka nʼkumangozungulirazungulira mu dzikomo, chipululu chitawazinga.’
[4] Ndidzawumitsa mtima wa Farao ndipo adzathamangira Aisraeliwo. Choncho ndikadzagonjetsa Farao ndi gulu lake lonse la nkhondo, Ine ndidzalemekezedwa.” Choncho Aisraeli aja anachita zimenezi.
[5] Farao, mfumu ya Igupto atamva kuti anthu aja athawa, iye pamodzi ndi nduna zake anasintha maganizo awo pa Israeli ndipo anati, “Ife tachita chiyani? Tawalola Aisraeli kuti apite ndi kuleka kutitumikira?”
[6] Choncho anakonzetsa galeta lake ndipo ananyamuka pamodzi ndi ankhondo ake.
[7] Iye anatenga magaleta 600 abwino kwambiri pamodzi ndi magaleta ena a dziko la Igupto. Anatenganso akuluakulu onse ankhondo.
[8] Yehova anawumitsa mtima wa Farao mfumu ya dziko la Igupto, kotero iye anawathamangira Aisraeli amene ankachoka mʼdzikomo mosavutika.
[9] Aigupto aja (kutanthauza akavalo ndi magaleta onse a Farao, okwera akavalowo pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo) analondola Aisraeli aja ndipo anakawapeza pamalo pamene anamanga zithando paja, mʼmbali mwa nyanja, pafupi ndi Pihahiroti, moyangʼanana ndi Baala-Zefoni.
[10] Tsono Farao anayandikira. Ndipo Aisraeli ataona kuti Aigupto akuwatsatira, anachita mantha aakulu ndipo anafuwula kwa Yehova.
[11] Iwo anafunsa Mose kuti, “Kodi nʼchifukwa chakuti kunalibe manda ku dziko la Igupto kuti iwe utibweretse muno mʼchipululu kuti tidzafe? Chimene watichitachi nʼchiyani, kutitulutsa mʼdziko la Igupto?
[12] Kodi sindizo zimene tinakuwuza mʼdziko la Igupto? Ife tinati, ‘Tileke titumikire Aigupto?’ Zikanatikomera kutumikira Aigupto kulekana ndi kufa mʼchipululu muno.”
[13] Mose anayankha anthu kuti, “Musachite mantha. Imani, ndipo muone chipulumutso chimene Yehova akuchitireni lero. Aigupto amene mukuwaona lerowa simudzawaonanso.
[14] Yehova adzakumenyerani nkhondo. Inu mungokhala chete.”
[15] Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Chifukwa chiyani ukufuwulira kwa ine? Uwuze Aisraeli aziyenda.
[16] Nyamula ndodo yako ndi kutambasula dzanja lako kuloza ku nyanja, kugawa madzi kuti Aisraeli awoloke powuma.
[17] Ine ndidzawumitsa mitima ya Aigupto kotero kuti adzatsatirabe Aisraeli. Ndipo ine ndikadzagonjetsa Farao ndi asilikali ake onse ankhondo, okwera magaleta ndi akavalo, ndidzapeza ulemerero.
[18] Aigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova akadzaona mmene ndipambanire Farao ndi magaleta ndi owayendetsa ake.”
[19] Ndipo mngelo wa Mulungu amene amayenda patsogolo pa gulu lankhondo la Israeli anachoka ndi kupita kumbuyo kwawo. Chipilala cha mtambo chinasunthanso kuchoka kutsogolo ndi kupita kumbuyo kwawo.
[20] Choncho mtambowo unakhala pakati pa asilikali ankhondo a dziko la Igupto ndi a dziko la Israeli. Choncho panali mdima motero kuti magulu awiri ankhondowa sanathe kuyandikizana usiku wonse.
[21] Kenaka Mose anatambalitsa dzanja lake pa nyanja, ndipo Yehova pogwiritsa ntchito mphepo yamphamvu ya kummawa imene inawomba usiku wonse anabweza madzi ndi kuwumitsa nyanja ija. Choncho nyanja ija inagawanika.
[22] Ndipo Aisraeli anawoloka pakati pa nyanja powuma, madzi atasanduka khoma kumanja ndi kumanzere kwawo.
[23] Aigupto onse, Farao, ndi onse okwera pa magaleta ndi akavalo anawalondola ndipo analowa mʼmadzi.
[24] Kutatsala pangʼono kucha, Yehova ali mu chipilala chamoto ndi chamtambo, anayangʼana asilikali ankhondo a Igupto ndipo anabweretsa chisokonezo pakati pawo.
[25] Yehova anamanga matayala a magaleta kotero kuti ankavutika kuyenda. Ndipo Aigupto anati, “Tiyeni tiwathawe Aisraeli! Yehova akuwamenyera nkhondo kulimbana nafe.”
[26] Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Tambasula dzanja lako pa nyanja kuti madzi amize Aigupto ndi magaleta awo ndi okwera pa akavalo.”
[27] Mose anatambasula dzanja lake pa nyanja, ndipo mmene kumacha nyanja inabwerera mʼmalo mwake. Aigupto pothawa anakumana nayo, ndipo Yehova anawakokera mʼnyanja momwemo.
[28] Madzi anabwerera ndi kumiza magaleta ndi okwera akavalo, asilikali ankhondo onse amene anatsatira Aisraeli mʼnyanja, palibe ndi mmodzi yemwe amene anapulumuka.
[29] Koma Aisraeli aja anawoloka nyanja pansi pali powuma, madzi atachita khoma kumanja ndi kumanzere kwawo.
[30] Tsiku limeneli Yehova anapulumutsa Israeli mʼmanja mwa Aigupto ndipo Israeli anaona Aigupto ali lambalamba mʼmbali mwa nyanja atafa
[31] Choncho Aisraeli anaona dzanja lamphamvu la Yehova limene linagonjetsa Aigupto aja, ndipo iwo anaopa Yehova ndi kumukhulupirira pamodzi ndi mtumiki wake Mose.