[1] Benjamini anabereka Bela mwana wake woyamba, wachiwiri Asibeli, wachitatu Ahara,
[2] wachinayi Noha ndipo wachisanu Rafa.
[3] Ana a Bela anali awa: Adari, Gera, Abihudi,
[4] Abisuwa, Naamani, Ahowa,
[5] Gera, Sefufani ndi Hiramu.
[6] Zidzukulu za Ehudi, zimene zinali atsogoleri a mabanja a amene amakhala ku Geba ndipo zinasamutsidwa kupita ku Manahati zinali izi:
[7] Naamani, Ahiya ndi Gera, amene anawasamutsa ndipo anabereka Uza ndi Ahihudi.
[8] Saharaimu anabereka ana ku Mowabu atalekana ndi akazi ake, Husimu ndi Baara.
[9] Mwa mkazi wake Hodesi anabereka Yobabu, Zibiya, Mesa, Malikamu,
[10] Yeusi, Sakiya ndi Mirima. Awa ndiye ana ake, atsogoleri a mabanja awo.
[11] Mwa mkazi wake Husimu anabereka Abitubi ndi Elipaala.
[12] Ana a Elipaala anali awa: Eberi, Misamu, Semedi (amene anamanga mizinda ya Ono ndi Lodi ndi midzi yake yozungulira)
[13] ndiponso Beriya ndi Sema, amene anali atsogoleri a mabanja a amene ankakhala ku Ayaloni ndipo anathamangitsa nzika za ku Gati.
[14] Ahiyo, Sasaki, Yeremoti,
[15] Zebadiya, Aradi, Ederi,
[16] Mikayeli, Isipa ndi Yoha anali ana a Beriya.
[17] Zebadiya, Mesulamu, Hiziki, Heberi,
[18] Isimerai, Iziliya ndi Yobabu anali ana a Elipaala.
[19] Yakimu, Zikiri, Zabidi,
[20] Elienai, Ziletai, Elieli,
[21] Adaya, Beraya ndi Simirati anali ana a Simei.
[22] Isipani, Eberi, Elieli,
[23] Abidoni, Zikiri, Hanani,
[24] Hananiya, Elamu, Anitotiya,
[25] Ifideya ndi Penueli anali ana a Sasaki.
[26] Samuserai, Sehariya, Ataliya,
[27] Yaaresiya, Eliya ndi Zikiri anali ana a Yerohamu.
[28] Onsewa anali atsogoleri a mabanja, anthu otchuka potsata mibado yawo, ndipo ankakhala mu Yerusalemu.
[29] Yeiyeli amene amabereka Gibiyoni ankakhala ku Gibiyoni. Dzina la mkazi wake linali Maaka,
[30] ndipo mwana wake woyamba anali Abidoni, motsatana ndi Zuri, Kisi, Baala, Neri, Nadabu,
[31] Gedori, Ahiyo, Zekeri
[32] ndi Mikiloti, amene anabereka Simea. Iwowa ankakhalanso ku Yerusalemu ndi abale awo.
[33] Neri anabereka Kisi. Kisi anabereka Sauli, ndipo Sauli anabereka Yonatani, Maliki-Suwa, Abinadabu ndi Esibaala.
[34] Mwana wa Yonatani anali Meri-Baala, amene anabereka Mika.
[35] Ana a Mika anali awa: Pitoni, Meleki, Tareya ndi Ahazi.
[36] Ahazi anabereka Yehoyada, Yehoyada anabereka Alemeti, Azimaveti ndi Zimuri, ndipo Zimuri anabereka Moza.
[37] Moza anabereka Bineya. Ana ake anali Rafa, Eleasa ndi Azeli.
[38] Azeli anali ndi ana asanu ndi mmodzi, ndipo mayina awo anali awa: Azirikamu, Bokeru, Ismaeli, Seariya, Obadiya ndi Hanani. Onsewa anali ana a Azeli.
[39] Ana a Eseki mʼbale wake anali awa: Mwana wake woyamba Ulamu, wachiwiri Yeusi ndipo wachitatu Elifeleti.
[40] Ana a Ulamu anali asilikali olimba mtima amene amadziwa kugwiritsa ntchito uta. Iwo anali ndi ana ndi adzukulu ambiri ndipo onse analipo 150. Onsewa anali adzukulu a Benjamini.