[1] Magulu a ana a Aaroni anali awa: Ana a Aaroni anali Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara.
[2] Koma Nadabu ndi Abihu anamwalira abambo awo asanamwalire, ndipo analibe ana aamuna. Kotero Eliezara ndi Itamara ankatumikira monga ansembe.
[3] Mothandizidwa ndi Zadoki chidzukulu cha Eliezara ndi Ahimeleki chidzukulu cha Itamara, Davide anawagawa mʼmagulu molingana ndi ntchito yawo yotumikira.
[4] Atsogoleri ambiri anapezeka pakati pa zidzukulu za Eliezara kusiyana ndi zidzukulu za Itamara ndipo anagawidwa moyenera: atsogoleri 16 a mabanja ochokera kwa Eliezara, ndipo atsogoleri asanu ndi atatu a mabanja ochokera kwa zidzukulu za Itamara.
[5] Anawagawa mosakondera pochita maere, pakuti iwo anali akuluakulu a ku malo opatulika ndi akuluakulu a Mulungu pakati pa zidzukulu za Eliezara ndi Itamara.
[6] Mlembi Semaya mwana wa Netaneli, Mlevi, analemba mayina awo pamaso pa mfumu ndi akuluakulu ake: wansembe Zadoki, Ahimeleki mwana wa Abiatara ndi atsogoleri a mabanja a ansembe ndiponso Alevi, banja limodzi kuchokera kwa Eliezara kenaka limodzi kuchokera kwa Itamara.
[7] Maere woyamba anagwera Yehoyaribu, achiwiri anagwera Yedaya,
[8] achitatu anagwera Harimu, achinayi anagwera Seorimu,
[9] achisanu anagwera Malikiya, achisanu ndi chimodzi anagwera Miyamini,
[10] achisanu ndi chiwiri anagwera Hakozi, achisanu ndi chitatu anagwera Abiya,
[11] achisanu ndi chinayi anagwera Yesuwa, a khumi anagwera Sekaniya,
[12] a 11 anagwera Eliyasibu, a 12 anagwera Yakimu,
[13] a 13 anagwera Hupa, a 14 anagwera Yesebeabu,
[14] a 15 anagwera Biliga, a 16 anagwera Imeri,
[15] a 17 anagwera Heziri, a 18 anagwera Hapizezi,
[16] a 19 anagwera Petahiya, a 20 anagwera Ezekieli,
[17] a 21 anagwera Yakini, a 22 anagwera Gamuli,
[18] a 23 anagwera Delaya, ndipo a 24 anagwera Maaziya.
[19] Umu ndi mmene anasankhidwira kuti azigwira ntchito yotumikira pamene alowa mʼNyumba ya Yehova, motsatira dongosolo limene anapatsidwa ndi kholo lawo Aaroni, monga momwe Yehova Mulungu wa Israeli anamulamulira.
[20] Za zidzukulu zina zonse za Levi: Kuchokera kwa ana a Amramu: Subaeli; kuchokera kwa ana a Subaeli: Yehideya.
[21] Kwa Rehabiya, kuchokera kwa ana ake: Mtsogoleri anali Isiya.
[22] Kuchokera ku banja la Izihari: Selomoti; kuchokera kwa ana a Selomoti: Yahati.
[23] Ana a Hebroni: woyamba anali Yeriya, wachiwiri anali Amariya, wachitatu anali Yahazieli ndipo Yekameamu anali wachinayi.
[24] Mwana wa Uzieli: Mika; kuchokera kwa ana a Mika: Samiri.
[25] Mʼbale wa Mika: Isiya; kuchokera kwa ana a Isiya: Zekariya.
[26] Ana a Merari: Mahili ndi Musi. Mwana wa Yaaziya: Beno.
[27] Ana a Merari: Kuchokera kwa Yaaziya: Beno, Sohamu, Zakuri ndi Ibiri.
[28] Kuchokera kwa Mahili: Eliezara, amene analibe ana aamuna.
[29] Kuchokera kwa Kisi: Mwana wa Kisi: Yerahimeeli.
[30] Ndipo ana a Musi: Mahili, Ederi ndi Yerimoti. Awa anali Alevi potsata mabanja a makolo awo.
[31] Iwonso anachita maere, monga anachitira abale awo, zidzukulu za Aaroni, pamaso pa mfumu Davide, ndi Zadoki ndi Ahimeleki, atsogoleri a mabanja a ansembe ndi Alevi. Mabanja a mwana wamkulu anachita nawo mofanana ndi a mwana wamngʼono.