Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 6:59

[1] Uwu ndi mndandanda wa Aisraeli, atsogoleri a mabanja, olamulira asilikali 1,000, olamulira asilikali 100 ndi akuluakulu awo, amene ankatumikira mfumu mʼzonse zokhudza magulu a ankhondo, amene amagwira ntchito mwezi ndi mwezi chaka chonse. Gulu lililonse linali ndi anthu 24,000.

[2] Amene amalamulira gulu loyamba pa mwezi woyamba anali Yasobeamu mwana wa Zabidieli. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

[3] Iyeyu anali chidzukulu cha Perezi ndipo anali mkulu wa atsogoleri onse a ankhondo mwezi woyamba.

[4] Amene amalamulira gulu lachiwiri pa mwezi wachiwiri anali Dodai Mwahohi; Mikiloti ndiye anali mtsogoleri wa gulu lake. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

[5] Wolamulira ankhondo wachitatu, pa mwezi wachitatu anali Benaya, mwana wa wansembe Yehoyada. Iye anali mtsogoleri ndipo pa gulu lake panali ankhondo 24,000.

[6] Uyu ndi Benaya uja amene anali wamphamvu pa gulu la anthu makumi atatu ndipo ndiye amatsogolera anthu makumi atatu aja. Mwana wake Amizabadi ndiye amatsogolera gulu lake.

[7] Wachinayi pa mwezi wachinayi anali Asaheli mʼbale wake wa Yowabu; ndipo mwana wake Zebadiya ndiye analowa mʼmalo mwake. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

[8] Wachisanu pa mwezi wachisanu anali Samihuti, mdzukulu wa Izira. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

[9] Wa 6 pa mwezi wa 6 anali Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

[10] Wa 7 pa mwezi wa 7 anali Helezi Mpeloni wa fuko la Efereimu. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

[11] Wa 8 pa mwezi wa 8 anali Sibekai Mhusati, wa mbumba ya Zera. Pa gulu lake panali asilikali 24,000

[12] Wa 9 pa mwezi wa 9 anali Abiezeri wa banja la Anatoti, wa fuko la Benjamini. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

[13] Wa khumi pa mwezi wa khumi anali Mahazayi wa ku Netofa, wa mbumba ya Zera. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

[14] Mtsogoleri wa 11, pa mwezi wa 11 anali Benaya wa ku Piratoni, wa fuko la Efereimu. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

[15] Mtsogoleri wa 12, pa mwezi wa 12 anali Helidai Mnetofa, wa banja la Otanieli. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

[16] Akuluakulu amene amatsogolera mafuko a Israeli ndi awa: Mtsogoleri wa fuko la Rubeni: Eliezara mwana wa Zikiri; mtsogoleri wa fuko la Simeoni: Sefatiya mwana wa Maaka;

[17] mtsogoleri wa fuko la Levi: Hasabiya mwana wa Kemueli, mtsogoleri wa banja la Aaroni: Zadoki;

[18] mtsogoleri wa fuko la Yuda: Elihu, mʼbale wake wa Davide; mtsogoleri wa fuko la Isakara: Omuri mwana wa Mikayeli;

[19] mtsogoleri wa fuko la Zebuloni: Isimaiya mwana wa Obadiya; mtsogoleri wa fuko la Nafutali: Yerimoti mwana wa Azirieli;

[20] mtsogoleri wa fuko la Efereimu: Hoseya mwana wa Azaziya; mtsogoleri wa fuko la theka la Manase: Yoweli mwana wa Pedaya;

[21] mtsogoleri wa fuko la theka la Manase limene linali ku Giliyadi: Ido mwana wa Zekariya; mtsogoleri wa fuko la Benjamini: Yaasieli mwana wa Abineri;

[22] mtsogoleri wa fuko la Dani: Azareli mwana wa Yerohamu. Awa anali akuluakulu a mafuko a Israeli.

[23] Davide sanawerenge amuna amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kucheperapo, chifukwa Yehova analonjeza kuti adzachulukitsa Aisraeli ngati nyenyezi zamumlengalenga.

[24] Yowabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga amuna koma sanamalize. Mkwiyo unagwera Aisraeli chifukwa cha zimenezi ndipo chiwerengerochi sanachilowetse mʼbuku la mbiri ya mfumu Davide.

[25] Azimaveti mwana wa Adieli ankayangʼanira nyumba zosungiramo katundu wa mfumu. Yonatani mwana wa Uziya ankayangʼanira nyumba zosungiramo katundu wa maboma ozungulira, mizinda, midzi ndi malo olondera.

[26] Eziri mwana wa Kelubi ankayangʼanira anthu ogwira ntchito yolima ku munda.

[27] Simei wa ku Rama ankayangʼanira minda ya mpesa. Zabidi wa ku Sifamu ankayangʼanira mphesa ndi mosungiramo mwake.

[28] Baala-Hanani wa ku Gederi ankayangʼanira mitengo ya olivi ndi ya mikuyu ya ku Sefela. Yowasi ankayangʼanira mafuta a Olivi.

[29] Sitirayi wa ku Saroni ankayangʼanira ziweto zimene amaweta ku Saroni. Safati mwana wa Adilayi ankayangʼanira ngʼombe zakuzigwa.

[30] Obili Mwismaeli ankayangʼanira ngamira. Yehideya Mmerenoti ankayangʼanira abulu.

[31] Yazizi Mhagiri akayangʼanira nkhosa ndi mbuzi. Onsewa anali akuluakulu oyangʼanira chuma cha mfumu Davide.

[32] Yonatani, malume wake wa Davide, anali phungu wake ndipo anali munthu wanzeru komanso analinso mlembi. Yehieli mwana wa Hakimoni ankasamalira ana a mfumu.

[33] Ahitofele anali phungu wa mfumu. Husai Mwariki anali bwenzi la mfumu.

[34] Ahitofele atamwalira mʼmalo mwake munalowa Yehoyada mwana wa Benaya ndi Abiatara. Yowabu anali mtsogoleri wa gulu lankhondo la mfumu.

1 Mbiri — Chapters