Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:49

[1] Davide ndi atsogoleri a asilikali anapatula ena mwa ana a Asafu, Hemani ndi Yedutuni ku utumiki wa uneneri pogwiritsa ntchito apangwe, azeze ndi ziwaya zamalipenga. Tsopano nawu mndandanda wa anthu amene ankagwira ntchito imeneyi:

[2] Kuchokera kwa ana a Asafu: Zakuri, Yosefe, Netaniya ndi Asareli. Ana a Asafu amalamulidwa ndi Asafu ndipo amanenera moyangʼaniridwa ndi mfumu.

[3] Kwa Yedutuni, kuchokera kwa ana ake: Gedaliya, Zeri, Yesaya, Simei, Hasabiya ndi Matitiya. Onse analipo 9 ndipo amayangʼaniridwa ndi Yedutuni abambo awo, amene amanenera pogwiritsa ntchito apangwe poyamika ndi kutamanda Yehova.

[4] Kwa Hemani, kuchokera kwa ana ake: Bukiya, Mataniya, Uzieli, Subaeli ndi Yerimoti; Hananiya, Hanani, Eliata, Gidaliti ndi Romamiti-Ezeri; Yosibakasa, Maloti, Hotiri ndi Mahazioti.

[5] Onsewa anali ana a Hemani mlosi wa mfumu. Iye anapatsidwa anawa potsata mawu a Mulungu akuti adzamukweza. Mulungu anapatsa Hemani ana aamuna 14 ndi ana aakazi atatu.

[6] Anthu onsewa ankayangʼaniridwa ndi makolo awo pa mayimbidwe a mʼNyumba ya Yehova. Iwowatu ankayimba ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe potumikira mʼNyumba ya Mulungu. Koma Asafu, Yedutuni ndi Hemani amayangʼaniridwa ndi mfumu.

[7] Iwo pamodzi ndi abale awo onse ophunzitsidwa ndi aluso loyimbira Yehova chiwerengero chawo chinali 288.

[8] Angʼonoangʼono ndi akulu omwe, mphunzitsi ndi wophunzira yemwe anachita maere pa ntchito zawo.

[9] Maere woyamba amene anali a Asafu, anagwera Yosefe, ana ndi abale ake. 12 Maere achiwiri anagwera Gedaliya, ndi abale ake ndi ana ake. 12

[10] Maere achitatu anagwera Zakuri, ana ake ndi abale ake. 12

[11] Maere achinayi anagwera Iziri, ana ake ndi abale ake. 12

[12] Maere achisanu anagwera Netaniya, ana ake ndi abale ake. 12

[13] Maere achisanu ndi chimodzi anagwera Bukiya, ana ake ndi abale ake. 12

[14] Maere achisanu ndi chiwiri anagwera Yesarela, ana ake ndi abale ake. 12

[15] Maere achisanu ndi chitatu anagwera Yeshaya, ana ake ndi abale ake. 12

[16] Maere achisanu ndi chinayi anagwera Mataniya, ana ake ndi abale ake. 12

[17] Maere a khumi anagwera Simei, ana ake ndi abale ake. 12

[18] Maere a 11 anagwera Azareli, ana ake ndi abale ake. 12

[19] Maere a 12 anagwera Hasabiya, ana ake ndi abale ake. 12

[20] Maere a 13 anagwera Subaeli, ana ake ndi abale ake. 12

[21] Maere a 14 anagwera Matitiya, ana ake ndi abale ake. 12

[22] Maere a 15 anagwera Yeremoti, ana ake ndi abale ake. 12

[23] Maere a 16 anagwera Hananiya, ana ake ndi abale ake. 12

[24] Maere a 17 anagwera Yosibakasa, ana ake ndi abale ake. 12

[25] Maere a 18 anagwera Hanani, ana ake ndi abale ake. 12

[26] Maere a 19 anagwera Maloti, ana ake ndi abale ake. 12

[27] Maere a 20 anagwera Eliyata, ana ake ndi abale ake. 12

[28] Maere a 21 anagwera Hotiri, ana ake ndi abale ake. 12

[29] Maere a 22 anagwera Gidaliti, ana ake ndi abale ake. 12

[30] Maere a 23 anagwera Mahazioti, ana ake ndi abale ake. 12

[31] Maere a 24 anagwera Romamiti-Ezeri, ana ake ndi abale ake 12.

1 Mbiri — Chapters