Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 11:09

[1] Ndipo anawawuza kuti,“Zoonadi, ndikuwuzani kuti ena amene ayimirira pano sadzafa asanaone ufumu wa Mulungu ukubwera mwa mphamvu.”

[2] Patatha masiku asanu ndi limodzi Yesu anatenga Petro, Yakobo ndi Yohane nawatsogolera kupita ku phiri lalitali, kumene anali okhaokha. Kumeneko maonekedwe ake anasinthika pamaso pawo.

[3] Zovala zake zinawala monyezimira kwambiri, kotero kuti palibe sopo wina aliyense amene angaziyeretse monyezimira chotere pa dziko la pansi.

[4] Ndipo anaonekera Eliya ndi Mose pamaso pawo, amene ankayankhulana ndi Yesu.

[5] Petro anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, ndi kwabwino kuti ife tili pano. Tiyeni timange misasa itatu; umodzi wanu, wina wa Mose ndi wina wa Eliya.”

[6] (Iye sanadziwe choti anene, anali ndi mantha akulu).

[7] Pamenepo mtambo unaoneka ndi kuwaphimba, ndipo mawu anamveka kuchokera mu mtambo kuti, “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa. Mvereni Iye!”

[8] Mwadzidzidzi, atayangʼanayangʼana, sanaonenso wina aliyense ali ndi iwo kupatula Yesu.

[9] Pamene ankatsika kuchokera ku phiri, Yesu anawalamulira kuti asawuze aliyense zimene anaona mpaka Mwana wa Munthu atauka kwa akufa.

[10] Iwo anayisunga nkhaniyo nakambirana za tanthauzo lake la “Kuuka kwa akufa.”

[11] Ndipo anamufunsa Iye kuti, “Nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amati Eliya ayenera kuyamba wabwera?”

[12] Yesu anayankha kuti,“Kunena motsimikiza, Eliya ayeneradi kuyamba kubwera kudzakonzanso zinthu zonse. Nʼchifukwa chiyani tsono zinalembedwa, kuti Mwana wa Munthu ayenera kuvutika kwambiri ndi kukanidwa?

[13] Koma ndikuwuzani, kuti Eliya wabweradi, ndipo amuchitira iye zonse zimene iwo anafuna, monga momwe zalembedwera za iye.”

[14] Atafika kwa ophunzira ena aja, anaona gulu lalikulu la anthu litawazungulira ndi aphunzitsi amalamulo akutsutsana nawo.

[15] Nthawi yomweyo anthu onse atamuona, anadabwa kwambiri ndipo anathamanga kukamulonjera.

[16] Iye anafunsa kuti,“Mukukangana nawo chiyani iwowa?”

[17] Munthu wina mʼgululo anayankha kuti, “Aphunzitsi, ndinakubweretserani mwana wanga wamwamuna, amene ndi ogwidwa ndi mzimu umene umamulepheretsa kuyankhula.

[18] Nthawi iliyonse ukamugwira umamugwetsa pansi. Amatuluka thovu kukamwa, amakukuta mano ake ndipo amawuma. Ndinapempha ophunzira anu kuti awutulutse mzimuwo, koma sanathe.”

[19] Yesu anayankha kuti,“Haa! Mʼbado osakhulupirira, kodi ndidzakhala nanu mpaka liti? Mubweretseni kwa Ine mnyamatayo.”

[20] Ndipo anamubweretsa kwa Iye. Mzimu woyipawo utaona Yesu, nthawi yomweyo unamukomola mnyamatayo. Anagwa pansi ndi kumagubuduka, ndi kuchita thovu kukamwa.

[21] Yesu anafunsa abambo a mnyamatayo kuti,“Kodi wakhala chotere nthawi yayitali bwanji?” Iye anayankha kuti, “Kuyambira ali wamngʼono,

[22] wakhala ukumuponya pa moto kapena mʼmadzi kuti umuphe. Koma ngati mungathe kuchita kanthu, tichitireni chifundo ndipo mutithandize.”

[23] Yesu anati,“ ‘Ngati mungathe!’ Zinthu zonse ndi zotheka kwa iye amene akhulupirira.”

[24] Nthawi yomweyo abambo a mwanayo anafuwula kuti, “Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga!”

[25] Yesu ataona kuti gulu la anthu likuthamangira kumalowo, anadzudzula mzimu woyipawo kuti,“Iwe mzimu wolepheretsa kuyankhula ndi kumva, ndikulamulira tuluka mwa iye ndipo usadzalowenso.”

[26] Mzimuwo unafuwula ndi kumugubuduza kwambiri ndipo unatuluka. Mnyamatayo anaoneka ngati mtembo ndipo ambiri anati, “Wafa.”

[27] Koma Yesu anamugwira dzanja ndipo anamuyimiritsa, ndipo anayimirira.

[28] Yesu atalowa mʼnyumba, ophunzira ake anamufunsa ali pa okha kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani ife sitinathe kutulutsa chiwandacho?”

[29] Iye anayankha kuti,“Mtundu uwu umatuluka pokhapokha mwapemphera ndi kusala kudya.”

[30] Anachoka malo amenewo nadutsa ku Galileya. Yesu sanafune kuti wina aliyense adziwe kumene anali,

[31] chifukwa amaphunzitsa ophunzira ake. Anati kwa iwo,“Mwana wa Munthu adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu. Adzamupha, ndipo patatha masiku atatu adzauka.”

[32] Koma sanazindikire chimene amatanthauza, ndipo anachita mantha kuti amufunse.

[33] Anafika ku Kaperenawo. Pamene anali mʼnyumba, anawafunsa kuti,“Kodi mumatsutsana chiyani mʼnjira muja?”

[34] Koma anakhala chete chifukwa ali mʼnjira amatsutsana za kuti wamkulu kuposa onse ndani.

[35] Atakhala pansi, Yesu anayitana khumi ndi awiriwo nati,“Ngati wina aliyense afuna kukhala woyamba, ayenera kukhala wotsiriza ndi wotumikira onse.”

[36] Anatenga kamwana nakayimiritsa pakati pawo ndipo anawawuza kuti,

[37] “Aliyense wolandira mmodzi wa ana angʼono awa mʼdzina langa alandira Ine; ndipo aliyense wolandira Ine salandira Ine koma amene anandituma.”

[38] Yohane anati, “Aphunzitsi, tinaona munthu akutulutsa ziwanda mʼdzina lanu ndipo ife tinamuwuza kuti aleke, chifukwa sanali mmodzi wa ife.”

[39] Yesu anati,“Musamuletse, palibe amene amachita chodabwitsa mʼdzina langa ndipo kenaka nanena zoyipa za Ine,

[40] pakuti aliyense amene satsutsana nafe ali mbali yathu.

[41] Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti aliyense amene akupatsani chikho cha madzi mʼdzina langa chifukwa ndinu ake a Khristu, sadzataya konse mphotho yake.”

[42] “Ndipo ngati wina aliyense achimwitsa mmodzi wa ana angʼono awa amene akhulupirira Ine, kukanakhala bwino kwa iye kuti aponyedwe mʼnyanja atamangiriridwa mwala waukulu mʼkhosi mwake.

[43] Ngati dzanja lako likuchimwitsa, lidule. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa mʼmoyo ndi dzanja limodzi kusiyana ndi kukhala ndi manja awiri ndi kupita ku gehena, kumene moto wake suzima.

[44] (Kumene mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima).

[45] Ndipo ngati phazi lako likuchimwitsa, lidule. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa mʼmoyo olumala kusiyana ndi kukhala ndi mapazi awiri ndi kuponyedwa mu gehena.

[46] (Kumene mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima).

[47] Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi, kusiyana ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa mu gehena,

[48] kumene “ ‘mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima.’

[49] Aliyense adzayesedwa ndi moto.

[50] “Mchere ndi wabwino, koma ngati utasukuluka, mungawukoleretsenso bwanji? Mukhale nawo mchere mwa inu nokha, ndipo mukhale pa mtendere wina ndi mnzake.”

Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu Wolembedwa ndi Marko — Chapters