Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 8:09

[1] Iye atachoka mʼNyumba ya Mulungu, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, “Aphunzitsi taonani! Miyala ikuluikulu! Nyumba zikongolerenji!”

[2] Yesu anayankha kuti,“Kodi mukuziona nyumba zikuluzikuluzi? Palibe mwala ndi umodzi pano umene udzakhala pa unzake; uliwonse udzagwetsedwa pansi.”

[3] Yesu atakhala pansi pa phiri la Olivi moyangʼanana ndi Nyumba ya Mulungu, Petro, Yakobo, Yohane ndi Andreya anamufunsa Iye pambali kuti,

[4] “Tatiwuzani, izi zidzachitika liti? Nanga chizindikiro chakuti zatsala pangʼono kukwaniritsidwa chidzakhala chiyani?”

[5] Yesu anawawuza kuti,“Chenjerani kuti wina asakunyengeni.

[6] Anthu ambiri adzabwera mʼdzina langa, nadzati, ‘Ine ndi Iyeyo,’ ndipo adzanamiza anthu ambiri.

[7] Pamene mudzamva zankhondo ndi mbiri zankhondo, musadzadzidzimuke. Zinthu zotere ziyenera kuchitika, koma sikuti chimaliziro chafika kale ayi.

[8] Mtundu udzawukira mtundu unzake, ndi ufumu kuwukira ufumu unzake. Kudzakhala zivomerezi mʼmalo osiyanasiyana, ndi njala. Izi ndi chiyambi chabe cha zowawa monga mayi pobereka.

[9] “Muyenera kukhala tcheru. Mudzaperekedwa ku mabwalo oweruza ndi kukwapulidwa mwankhanza mʼmasunagoge. Mudzayima pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu monga mboni kwa iwo chifukwa cha Ine.

[10] Ndipo Uthenga Wabwino uyenera kuyamba walalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.

[11] Nthawi iliyonse pamene mwamangidwa ndi kuyimbidwa mlandu, musadandaule za zimene mudzanena. Zimene mudzapatsidwe pa nthawiyo yankhulani; pakuti sindinu amene mudzayankhula, koma Mzimu Woyera.

[12] “Mʼbale adzapereka mʼbale kuti aphedwe, ndipo abambo adzapereka mwana wawo. Ana adzawukira makolo awo ndi kuwapereka kuti aphedwe.

[13] Anthu onse adzakudani chifukwa cha Ine, koma amene adzalimbika mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.

[14] “Mukadzaona ‘chinthu chonyansa chosakaza’ chitayima pa malo amene si ake, owerenga azindikire. Pamenepo amene ali ku Yudeya athawire kumapiri.

[15] Aliyense amene ali pa denga la nyumba yake asatsike kapena kulowa mʼnyumba kukatenga kanthu kalikonse.

[16] Aliyense amene ali ku munda asabwerere kukatenga mkanjo wake.

[17] Kudzakhala koopsa mʼmasiku amenewo kwa amayi oyembekezera ndi amayi oyamwitsa!

[18] Pempherani kuti zimenezi zisadzachitike nthawi yozizira,

[19] chifukwa masiku amenewo adzakhala owawitsa osafanana ndi ena kuyambira pachiyambi, pamene Mulungu analenga dziko, kufikira lero ndipo sadzafanananso ndi ena.

[20] Ambuye akanapanda kufupikitsa masikuwo, palibe amene akanapulumuka. Koma chifukwa cha osankhidwiratu, amene anawasankha, Iye anawafupikitsa.

[21] Pa nthawi imeneyo, ngati wina adzati kwa inu, ‘Taonani, Khristu ali kuno, kapena, Taonani, uyo ali apoyo!’ musakhulupirire.

[22] Pakuti akhristu onama ndi aneneri onama adzaonekera ndipo adzachita zizindikiro ndi zodabwitsa kuti anyenge osankhidwiratu ngati kutakhala kotheka kutero.

[23] Choncho khalani tcheru; ndakuwuzani zonse nthawi isanafike.

[24] “Koma masiku amenewo, masautsowo atatha, “ ‘dzuwa lidzada, ndipo mwezi sudzawala;

[25] nyenyezi zidzagwa kuchokera ku thambo, ndipo mayiko mumlengalenga adzagwedezeka!’

[26] “Nthawi imeneyo anthu adzaona Mwana wa Munthu akubwera mʼmitambo ndi mphamvu yayikulu ndi ulemerero.

[27] Ndipo adzatuma angelo ake kukasonkhanitsa osankhidwiratu ake ku mphepo zinayi, kuyambira kumalekezero a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.

[28] “Tsopano phunzirani phunziro ili kuchokera ku mtengo wamkuyu. Pamene msonga za nthambi zake zikhala za nthete ndipo masamba ake ayamba kuphukira, mumadziwa kuti dzinja layandikira.

[29] Momwenso pamene muona zinthu izi zikuchitika, dziwani kuti wayandikira, ali pa khomo.

[30] Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti mʼbado uno sudzatha mpaka zinthu zonsezi zitachitika.

[31] Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”

[32] “Palibe amene akudziwa za tsikulo kapena nthawi, ngakhale angelo akumwamba, kapena Mwana, koma Atate wokha.

[33] Khalani maso! Khalani tcheru! Simudziwa pamene nthawi imeneyo idzafike.

[34] Zili ngati munthu amene akuchokapo. Amasiyira nyumba yake antchito ake, aliyense ndi ntchito yake; ndi kumuwuza wa pa khomo kuti azikhala maso.

[35] “Inunso muyenera kukhala maso chifukwa simukudziwa nthawi imene mwini nyumba adzabwere, kaya madzulo, kapena pakati pa usiku, kapena tambala akulira, kapena mʼbandakucha.

[36] Ngati atabwera mwadzidzidzi, asadzakupezeni inu muli mtulo.

[37] Zimene ndikunena kwa inu, ndikunena kwa aliyense: ‘Khalani tcheru!’ ”

Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu Wolembedwa ndi Marko — Chapters