Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 8:40

[1] Mmamawa, akulu a ansembe pamodzi ndi akuluakulu, aphunzitsi amalamulo ndi olamulira onse anamanga fundo. Anamumanga Yesu, namutenga ndi kukamupereka kwa Pilato.

[2] Pilato anafunsa kuti, “Kodi Iwe ndi Mfumu ya Ayuda?” Yesu anayankha kuti,“Mwatero ndinu.”

[3] Akulu a ansembe anamunenera zinthu zambiri.

[4] Ndipo Pilato anamufunsanso Iye kuti, “Kodi Iwe suyankhapo kanthu? Tamva zinthu zambiri akukunenerazi.”

[5] Koma Yesu sanayankhebe, ndipo Pilato anadabwa.

[6] Pa nthawi ya Phwando, panali chizolowezi chomasula munthu wamʼndende amene anthu amupempha.

[7] Munthu wotchedwa Baraba anali mʼndende pamodzi ndi anthu owukira amene anapha anthu pa nthawi ya chipolowe.

[8] Gulu la anthu linabwera kwa Pilato ndi kumufunsa kuti awachitire zimene amachita nthawi zonse.

[9] “Kodi mukufuna kuti ndikumasulireni mfumu ya Ayuda?” Pilato anafunsa,

[10] podziwa kuti akulu a ansembe anamupereka Yesu kwa iye chifukwa cha nsanje.

[11] Koma akulu a ansembe anasonkhezera anthu kuti Pilato amasule Baraba mʼmalo mwa Yesu.

[12] Pilato anawafunsa kuti, “Kodi nanga ndichite chiyani ndi uyu amene mukumutcha mfumu ya Ayuda?”

[13] Anafuwula kuti, “Mpachikeni!”

[14] Pilato anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani? Wapalamula mlandu wotani?” Koma anafuwula kwambiri, “Mpachikeni!”

[15] Pilato pofuna kuwakondweretsa anthuwo, anawamasulira Baraba. Analamula kuti Yesu akwapulidwe mwankhanza, ndipo anamupereka kuti akapachikidwe.

[16] Asilikali anamutenga Yesu ndi kupita naye mʼkati mwa nyumba yaufumu (dera lokhalako asilikali a mfumu) ndipo anasonkhanitsa gulu lonse la asilikali.

[17] Anamuveka Iye mwinjiro wofiira, kenaka analuka chipewa cha minga ndi kuyika pa mutu pake.

[18] Ndipo anayamba kunena kwa lye kuti, “Ulemu kwa inu Mfumu ya Ayuda!”

[19] Ndipo anamugogoda pa mutu mobwerezabwereza ndi ndodo ndi kumulavulira. Anamugwadira ndi kumulambira Iye.

[20] Ndipo anamuchita chipongwe, anamuvula mwinjiro wofiira uja ndi kumuveka zovala zake. Kenaka anamutenga kuti akamupachike.

[21] Munthu wina ochokera ku Kurene, Simoni, abambo a Alekisanda ndi Rufasi amadutsa kuchokera ku dziko la kwawo, ndipo anamuwumiriza kuti anyamule mtanda.

[22] Anafika naye Yesu pa malo otchedwa Gologota (kutanthauza kuti, malo a bade)

[23] Kenaka anamupatsa Iye vinyo wosakaniza ndi mure, koma Iye sanamwe.

[24] Ndipo anamupachika Iye. Anachita maere ogawana zovala zake kuti aone chimene aliyense angatenge.

[25] Linali ora lachitatu mmawa pamene anamupachika Yesu.

[26] Chikwangwani cholembedwapo mlandu wake chinali choti: .

[27] Achifwamba awiri anapachikidwanso pamodzi ndi Iye, wina kumanja kwake ndi wina kumanzere kwake.

[28] (Ndipo malemba anakwaniritsidwa amene amati, “Iye anayikidwa mʼgulu la anthu oyipa).”

[29] Amene amadutsa pafupi anamunenera mawu amwano, akupukusa mitu yawo ndi kuti, “Haa! Iwe amene udzawononga Nyumba ya Mulungu ndi kuyimanganso masiku atatu,

[30] tsika kuchoka pa mtandapo ndipo udzipulumutse wekha!”

[31] Chimodzimodzinso akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo anamunyoza Iye pakati pawo. Iwo anati, “Anapulumutsa ena, koma sangathe kudzipulumutsa yekha!

[32] Musiyeni Khristu, Mfumu ya Aisraeli, atsike tsopano kuchoka pa mtanda, kuti ife tione ndi kukhulupirira.” Iwonso amene anapachikidwa naye pamodzi anamulalatira.

[33] Pa ora lachisanu ndi chimodzi masana mdima unabwera pa dziko lonse mpaka pa ora lachisanu ndi chinayi masana.

[34] Pa ora lachisanu ndi chinayi Yesu analira mofuwula kuti,“Eloi, Eloi, lama sabakitani?” Kutanthauza kuti,“Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?”

[35] Ena amene anali pafupi atamva izi anati, “Tamverani, akuyitana Eliya.”

[36] Munthu wina anathamanga, natenga chinkhupule atachiviyika mu vinyo wosasa, anachizika ku mtengo, ndi kumupatsa Yesu kuti amwe. Munthuyo anati, “Musiyeni yekha tsopano. Tiyeni tione ngati Eliya angabwere kudzamutsitsa.”

[37] Ndi mawu ofuwula, Yesu anapuma komaliza.

[38] Chinsalu chotchinga cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati kuyambira pamwamba mpaka pansi.

[39] Ndipo Kenturiyo, amene anayima patsogolo pa Yesu, atamva kulira kwake ndi kuona mmene anafera anati, “Zoonadi, uyu anali Mwana wa Mulungu.”

[40] Amayi ena anali patali kuonerera. Pakati pawo panali Mariya Magadalena, Mariya amayi a Yakobo wamngʼono ndi Yose ndi Salome.

[41] Amayi awa ankamutsatira Iye mu Galileya ndi kumutumikira Iye pa zosowa zake. Amayi enanso ambiri amene anabwera naye ku Yerusalemu analinso pomwepo.

[42] Linali Tsiku Lokonzekera (kunena kuti, tsiku lomwe limatsatizana ndi Sabata). Choncho madzulo atayandikira,

[43] Yosefe wa ku Arimateyu, mkulu wolamulira odziwika bwino, amene amadikirira ufumu wa Mulungu, anapita kwa Pilato molimba mtima ndi kukapempha mtembo wa Yesu.

[44] Pilato anadabwa pakumva kuti anali atamwalira kale. Anayitana Kenturiyo, namufunsa ngati Yesu anali atamwalira kale.

[45] Atawuzidwa ndi Kenturiyo kuti zinali motero, anapereka mtembowo kwa Yosefe.

[46] Choncho Yosefe anagula nsalu yabafuta, natsitsa thupi, ndipo analikulunga mʼnsalu, naliyika mʼmanda amene anawagoba pa mwala. Kenaka anagubuduza mwala umene anatseka nawo mandawo.

[47] Mariya Magadalena ndi Mariya amayi a Yose anaona kumene anamuyika Yesu.

Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu Wolembedwa ndi Marko — Chapters