[1] Kenaka Yosefe anadzigwetsa pa nkhope ya abambo ake, nawapsompsona kwinaku akulira.
[2] Ndipo Yosefe analamula antchito ake a chipatala kuti akonze thupi la Israeli ndi mankhwala kuti lisawole. Kotero antchitowo anakonzadi thupilo.
[3] Antchito aja zinawatengera masiku 40 kuti akonze mtembo uja popeza ntchito ngati imeneyi inafunikira masiku monga amenewa. Ndipo Aigupto anamulira Yakobo kwa masiku makumi asanu ndi awiri.
[4] Yosefe atatha kulira maliro a abambo ake, anayankhula kwa nduna za Farao nati, “Ngati mungandikomere mtima, chonde mundiyankhulire kwa Farao kumuwuza kuti,
[5] ‘Abambo anga anandilumbiritsa ndipo anati, ‘Ndatsala pangʼono kumwalira, ukandiyike mʼmanda amene ndinakumba ndekha mʼdziko la Kanaani.’ Tsono mundilole ndikayike abambo anga, ndipo ndikabweranso.’ ”
[6] Farao anati, “Pita ukayike abambo ako monga anakulumbiritsa kuti uchite.”
[7] Kotero Yosefe anapita kukayika abambo ake. Nduna zonse za Farao, akuluakulu a bwalo lake ndi akuluakulu a ku Igupto, anapita naye pamodzi.
[8] Anapitanso onse a pa banja la Yosefe ndi abale ake ndi onse amene anali a pa banja la abambo ake. Ana awo okha, nkhosa ndi ngʼombe zinatsala ku Goseni
[9] Asilikali okwera pa magaleta ndi asilikali a pa akavalo anapita nayenso pamodzi. Linali gulu lalikulu.
[10] Atafika pa Goreni ha-Atadi, pafupi ndi Yorodani, anachita mwambo waukulu wa maliro. Choncho Yosefe analira maliro a abambo ake masiku asanu ndi awiri.
[11] Akanaani amene ankakhala ku Goreni ha-Atadi ataona mwambo wa maliro anati, “Aigupto ali ndi mwambo wa maliro a akulu.” Ndi chifukwa chake malo amenewo a pafupi ndi Yorodani amatchedwa Abeli-Mizraimu.
[12] Choncho ana a Yakobo anachita monga momwe abambo awo anawalamula:
[13] Ndiye kuti ana a Yakobo anamunyamula kupita naye ku Kanaani kuti akamuyike mʼphanga limene lili mʼmunda wa Makipela pafupi ndi Mamre. Abrahamu anagula mundawo kwa Efroni Mhiti kuti pakhale manda.
[14] Atatha kuyika abambo ake, Yosefe anabwerera ku Igupto, pamodzi ndi abale ake ndi onse amene anapita nawo kukayika abambo ake.
[15] Abale ake a Yosefe ataona kuti abambo awo amwalira, anati, “Nanga tidzatani ngati Yosefe anatisungira mangawa nafuna kutibwezera pa zoyipa zonse zimene tinamuchitira?”
[16] Motero anatumiza mawu kwa Yosefe kuti, “Abambo anu anasiya malangizo asanafe nati:
[17] ‘Zimene mudzayenera kunena kwa Yosefe ndi izi: Ndikukupempha kuti uwakhululukire abale ako cholakwa chawo ndi machimo awo, popeza anakuchitira zoyipa.’ Ndiye tsopano chonde tikhululukireni zolakwa zimene ife akapolo a Mulungu wa abambo anu tinachita.” Yosefe atangomva mawu amenewa anayamba kulira.
[18] Kenaka abale ake anabwera nadzigwetsa pansi pamaso pake, nati, “Ife ndife akapolo anu.”
[19] Koma Yosefe anawawuza kuti, “Musachite mantha. Kodi ine ndalowa mʼmalo mwa Mulungu?
[20] Inu munafuna kundichitira zoyipa, koma Mulungu anasandutsa zoyipazo kuti zikhale zabwino kuti zikwaniritsidwe zimene zikuchitika panozi, zopulumutsa miyoyo yambiri.
[21] Kotero, musachite mantha. Ine ndidzasamalira inu pamodzi ndi ana anu omwe.” Tsono iye anawalimbitsa mtima powayankhula moleza mtima.
[22] Yosefe anakhala mu Igupto pamodzi ndi banja lonse la abambo ake. Anakhala ndi moyo zaka 110
[23] ndipo anaona mʼbado wachitatu wa ana a Efereimu. Yosefe anatenganso ana a Makiri, mwana wa Manase kukhala ngati ana a mʼbanja lake.
[24] Kenaka Yosefe anati kwa abale ake, “Ine ndatsala pangʼono kufa. Koma mosakayika Mulungu adzakuyangʼanirani nadzakutengani kukutulutsani mʼdziko lino kupita ku dziko limene Iye analonjeza kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo.”
[25] Ndipo Yosefe analumbiritsa ana a Israeli lumbiro nati, “Lonjezani kuti Mulungu akadzakusungani mudzanyamula mafupa anga kuwachotsa ku malo kuno.”
[26] Choncho Yosefe anafa ali ndi zaka 110. Motero iwo atakonza thupi lake ndi mankhwala kuti lisawole, analiyika mʼbokosi ku Igupto.