[1] Nazi zidzukulu za Esau amene ankatchedwanso Edomu:
[2] Esau anakwatira akazi atatu a ku Kanaani. Iwowa ndiwo Ada mwana wa Eloni Mhiti; Oholibama mwana wa Ana amene anali mwana wa Zibeoni Mhivi
[3] ndi Basemati mwana wa Ismaeli, amenenso anali mlongo wa Nabayoti.
[4] Ada anaberekera Esau, Elifazi; Basemati anabereka Reueli;
[5] ndipo Oholibama anabereka Yeusi, Yolamu ndi Kora. Amenewa anali ana a Esau amene anabadwira ku Kanaani.
[6] Esau anatenga akazi ake, ana ake aamuna ndi aakazi ndi ena onse a pa banja pake. Anatenganso ziweto zake ndi ziweto zake zonse pamodzi ndi katundu wake yense amene anamupata ku Kanaani, ndipo anachoka ku dziko la Kanaani kupatukana ndi mʼbale wake Yakobo.
[7] Iwo anatero chifukwa dziko limene ankakhalamo silikanakwanira awiriwo. Iwowa anali ndi ziweto zochuluka motero kuti sakanatha kukhala pamodzi.
[8] Choncho Esau (amene ndi Edomu) anakakhazikika ku dziko la mapiri ku Seiri.
[9] Nazi zidzukulu za Esau, kholo la Aedomu amene ankakhala ku Seiri.
[10] Awa ndi mayina a ana aamuna a Esau: Elifazi, mwana wa Ada, mkazi wa Esau, ndi Reueli, mwana wamwamuna wa Basemati, mkazi wa Esau.
[11] Awa ndi mayina a ana a Elifazi: Temani, Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi.
[12] Timna anali mzikazi wa Elifazi, mwana wa Esau. Iyeyo anaberekera Elifazi mwana dzina lake Amaleki. Amenewa ndiwo zidzukulu za Ada, mkazi wa Esau.
[13] Awa ndi ana a Reueli: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Amenewa ndi ana a Basemati, mkazi wa Esau.
[14] Ana aamuna a Oholibama, mkazi wa Esau, mwana wa Ana ndi mdzukulu wa Zebeoni ndi awa: Yeusi, Yolamu ndi Kora.
[15] Nawa mafumu a zidzukulu za Esau: Mwa ana a Elifazi, mwana woyamba wa Esau panali mafumu awa: Temani, Omari, Zefo, ndi Kenazi,
[16] Kora, Gatamu, ndi Amaleki. Awa anali mafumu mwa ana a Elifazi ku Edomu ndipo onsewa anali zidzukulu za Ada.
[17] Mwa ana a Reueli, mwana wa Esau munali mafumu awa: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Awa anali mafumu mwa ana a Reueli ku Edomu. Iwowa anali zidzukulu za Basemati mkazi wa Esau.
[18] Mwa ana a Oholibama, mkazi wa Esau munali mafumu awa: Yeusi, Yolamu, ndi Kora. Amenewa anali mafumu mwa ana a mkazi wa Esau, Oholibama, mwana wa Ana.
[19] Amenewa ndiwo zidzukulu za Esau (amene ndi Edomu) ndiponso mafumu awo.
[20] Awa ndi ana a Seiri Mhori, amene ankakhala mʼdzikomo: Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana,
[21] Disoni, Ezeri ndi Disani. Amenewa ndiwo ana a Seiri a ku Edomu ndipo analinso mafumu a Ahori.
[22] Ana aamuna a Lotani anali awa: Hori ndi Homamu. Timna anali mlongo wake wa Lotani.
[23] Ana aamuna a Sobala anali awa: Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu.
[24] Ana aamuna a Zibeoni anali awa: Ayiwa ndi Ana. Uyu ndi Ana amene anapeza akasupe a madzi amoto mʼchipululu pamene ankadyetsa abulu abambo wake Zibeoni.
[25] Ana a Ana anali: Disoni ndi Oholibama mwana wake wamkazi.
[26] Ana aamuna a Disoni anali awa: Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani.
[27] Ana aamuna a Ezeri anali awa: Bilihani, Zaavani ndi Akani.
[28] Ana aamuna a Disani anali awa: Uzi ndi Arani.
[29] Mafumu a Ahori anali awa: Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana,
[30] Disoni, Ezeri ndi Disani. Amenewa ndiwo mafumu a Ahori, monga mwa mafuko awo, mʼdziko la Seiri.
[31] Awa ndi mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mfumu iliyonse ya Israeli isanayambe kulamulira kumeneko:
[32] Bela mwana wa Beori anakhala mfumu ya ku Edomu. Mzinda wake ankawutcha Dinihaba.
[33] Bela atamwalira, Yobabu mwana wa Zera wochokera ku Bozira analowa ufumu mʼmalo mwake.
[34] Atafa Yobabu, Husamu wochokera ku dziko la Atemani, analowa mʼmalo mwake ngati mfumu.
[35] Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani mʼdziko la Mowabu, analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Aviti.
[36] Hadadi atamwalira, Samila wochokera ku Masireka, analowa ufumu mʼmalo mwake.
[37] Samila atamwalira, Sauli wochokera ku Rehoboti wa ku Mtsinje, analowa ufumu mʼmalo mwake.
[38] Sauli atamwalira, Baala-Hanani, mwana wa Akibori analowa ufumu mʼmalo mwake.
[39] Pamene Baala-Hanani mwana wa Akibori anamwalira, Hadari analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli, mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu.
[40] Mayina a mafumu ochokera mwa zidzukulu za Esau malingana ndi mafuko awo ndi malo a fuko lililonse anali awa: Timna, Aliva, Yeteti,
[41] Oholibama, Ela, Pinoni,
[42] Kenazi, Temani, Mibezari,
[43] Magidieli ndi Iramu. Awa anali mafumu a ku Edomu molingana ndi malo awo okhala mʼdzikomo. Umenewu ndi mndandanda wa mʼbado wa Esau, kholo la Aedomu.