[1] Nayi mbiri ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti. Ana atatuwa anabereka ana awo chitatha chigumula.
[2] Ana aamuna a Yafeti anali: Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi.
[3] Ana aamuna a Gomeri anali: Asikenazi, Rifati ndi Togarima.
[4] Ana aamuna a Yavani anali: Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu.
[5] (Amenewa ndiwo makolo a anthu okhala mʼmphepete mwa nyanja. Awa ndi ana a Yafeti monga mwa mafuko a mu mitundu yawo, uliwonse ndi chiyankhulo chake).
[6] Ana aamuna a Hamu anali: Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani.
[7] Ana aamuna a Kusi anali: Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka. Ana aamuna a Raama anali: Seba ndi Dedani.
[8] Kusi anabereka Nimurodi amene anali wankhondo wamphamvu kwambiri pa dziko lapansi.
[9] Iye anali mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova; nʼchifukwa chake anthu ali ndi chisudzo, chakuti, “Ndiwe mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova monga Nimurodi.”
[10] Malo oyambirira a ufumu wake anali Babeli, Ereki, Akadi ndi Kaline. Malo onsewa anali mʼdziko la Sinara.
[11] Atachoka mʼdziko limeneli anapita ku Asiriya kumene anakamanga Ninive, Rehoboti-Iri, Kala,
[12] ndi Reseni, mzinda waukulu umene uli pakati pa Ninive ndi Kala.
[13] Igupto ndiye kholo la Aludi, Aanami, Alehabu, Anafutu,
[14] Apaturusi, Akasilu ndi Akafitori (kumene kunachokera Afilisti).
[15] Kanaani anabereka mwana wake wachisamba, Sidoni, ndipo anaberekanso Ahiti;
[16] Ayebusi, Aamori, Agirigasi;
[17] Ahivi, Aariki, Asini,
[18] Aaravadi, Azemari ndi Ahamati. Pambuyo pake, mafuko a Akanaani anafalikira ponseponse,
[19] mpaka ku malire a Kanaani. Malirewo anachokera ku Sidoni kulowa cha ku Gerari mpaka ku Gaza, ndi kulowa ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa.
[20] Amenewa ndiwo ana aamuna a Hamu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe amakhala ndi mitundu yawo.
[21] Semu amene anali mkulu wake wa Yafeti nayenso anabereka nakhala kholo la Eberi.
[22] Ana aamuna a Semu anali: Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu.
[23] Ana aamuna a Aramu anali: Uzi, Huri, Geteri ndi Mesaki.
[24] Aripakisadi anabereka Sela, ndipo Selayo anabereka Eberi.
[25] A Eberi anabereka ana aamuna awiri: Wina anamutcha Pelegi chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani.
[26] Yokitani anabereka Alimodadi, Selefi, Hazari-Maveti, Yera,
[27] Hadoramu, Uzali, Dikila,
[28] Obali, Abimaeli, Seba,
[29] Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onsewa anali ana aamuna a Yokitani.
[30] Chigawo chimene ankakhala chinayambira ku Mesa mpaka ku Seferi, ku dera la mapiri chakummawa.
[31] Amenewa ndiwo ana a Semu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe ankakhala ndi mitundu yawo.
[32] Amenewa ndiwo mafuko a ana aamuna a Nowa monga mwa mibado ya mitundu yawo. Mitundu yonse ya anthu inatuluka mwa iwowa ndi kufalikira pa dziko lonse lapansi chitatha chigumula chija.