[1] Pa tsiku lakhumi la mwezi wakhumi chaka chachisanu ndi chinayi, Yehova anandiyankhula kuti:
[2] “Iwe mwana wa munthu lemba dzina la tsiku lalero, lero lomwe lino, chifukwa mfumu ya Babuloni yazungulira Yerusalemu lero lino.
[3] Uwaphere mwambi anthu owukirawa ndi kuwawuza kuti: ‘Ambuye Yehova akuti, “ ‘Ikani mʼphika pa moto, ndipo mu mʼphikamo muthiremo madzi.
[4] Mu mʼphikamo muyikemo nthuli za nyama, nthuli zonse zabwino kwambiri za mwendo wathako ndi mwendo wamwamba. Mudzadzemo mafupa abwino kwambiri.
[5] Pa gulu la nkhosa musankhepo nkhosa yabwino kwambiri. Muyike nkhuni pansi pa mʼphikawo. Madzi awire. Kenaka muphike nyamayo pamodzi ndi mafupa omwe.’
[6] “ ‘Nʼchifukwa chake, Ambuye Yehova akuti, “ ‘Tsoka kwa mzinda wokhetsa magazi, tsoka kwa mʼphika wadzimbiri; dzimbiri lake losachoka! Mutulutsemo nthuli imodzimodzi osasankhulapo.
[7] “ ‘Paja magazi amene anakhetsa akanali pakati pake mu mzindamo. Iye awakhuthulira pa thanthwe losalala. Sanawakhutulire pa dothi kuopa kuti fumbi lingawafotsere.
[8] Ndinasiya magaziwo pa mwala wosalala kuti asafotseredwe ndi fumbi chifukwa ndinafuna kuonetsa mkwiyo wanga ndi kulipsira.
[9] “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: “ ‘Tsoka kwa mzinda wokhetsa magazi! Inenso, ndidzawunjika mulu waukulu wa nkhuni.
[10] Choncho wonjeza nkhuni ndipo muyatse moto. Phikani nyamayo bwinobwino, muthiremo zokometsera, mutsanule msuzi, ndipo mupsereze mafupawo.
[11] Tsono muyike pa makala mʼphika wopanda kanthuwo mpaka utenthe kuchita kuti psuu kuti zonyansa zake zisungunuke ndi kuti dzimbiri lake lichoke.
[12] Koma mʼphikawo walephereka kuyeretsedwa. Dzimbiri lake linalowerera silingatheke kuchoka ngakhale ndi moto womwe.
[13] “ ‘Tsono dzimbiri limeneli ndi zilakolako za dama lako. Pakuti ine ndinayesa kukutsuka koma iwe sunayere, ndipo sudzayeranso mpaka ukali wanga utakwaniratu pa iwe.
[14] “ ‘Ine Yehova ndayankhula. Zimenezi zikubwera ndipo ndidzazichitadi. Sindidzabwerera mʼmbuyo. Sindidzakulekerera kapena kukuchitira chifundo. Ndidzakulanga molingana ndi makhalidwe ndi machitidwe ako, akutero Ambuye Yehova.’ ”
[15] Yehova anandiyankhula kuti:
[16] “Iwe mwana wa munthu, Ine ndikulanda mwadzidzidzi mkazi amene amakukomera mʼmaso kwambiri. Koma usadandaule, usalire kapena kukhetsa misozi.
[17] Ubuwule koma mwakachetechete. Usamulire wakufayo. Uvale nduwira yako ndithu, nsapato zakonso usavule. Usaphimbe nkhope kapena kudya chakudya cha anamfedwa.”
[18] Choncho ndinayankhula ndi anthu mmawa, ndipo madzulo mkazi wanga anamwalira. Mmawa mwake ndinachita monga momwe anandilamulira.
[19] Ndipo anthu anandifunsa kuti, “Kodi sutifotokozera tanthauzo la zimene ukuchitazi?”
[20] Ndinawayankha kuti, “Yehova anandipatsa uthenga wakuti,
[21] ‘Awuze Aisraeli kuti: Ine Ambuye Yehova ndikuti: ndidzayipitsa Nyumba yanga yopatulika, nyumba imene mwakhala mukuyinyadira. Mumakondwa kwambiri poyiona, ndipo mumayikonda ndi mtima onse. Ana aamuna ndi aakazi amene munawasiya mʼmbuyo adzaphedwa ndi lupanga.
[22] Ndipo mudzachita monga ndachitira inemu. Inu simudzaphimba nkhope zanu kapena kudya chakudya cha anamfedwa.
[23] Mudzavala nduwira zanu kumutu ndi nsapato zanu ku mapazi anu. Simudzabuma maliro kapena kukhetsa misozi koma mudzavutika kwambiri chifukwa cha machimo anu ndipo mudzabuwula pakati panu.
[24] Ine Ezekieli ndidzakhala chitsanzo chanu. Mudzachita monga momwe ndachitira. Izi zikadzachitika, akutero Yehova, ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Wamphamvuzonse.’
[25] “Ndipo Yehova anandiyankhula nati: Iwe mwana wa munthu, tsiku lina ndidzawachotsera anthuwa linga lawo limene ankakondwerera kukongola kwake, limene linkawakomera mʼmaso mwawo, limenenso anayikapo mtima wawo kwambiri. Ndidzawachotsera ana awo aamuna ndi aakazi.
[26] Pa tsiku limenelo wothawa nkhondo adzabwera kudzakuwuzani zimenezo.
[27] Pa tsiku limenelo pakamwa pako padzatsekuka. Udzatha kuyankhula naye ndipo sudzakhalanso chete. Motero udzakhala chizindikiro kwa iwo, ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”