Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:59

[1] “Imba nyimbo ya madandawulo, kuyimbira akalonga a ku Israeli.

[2] Uzinena kuti, “ ‘Amayi ako anali ndani? Anali ngati mkango waukazi! Iwo unabwatama pakati pa mikango yayimuna; unkalera ana ake pakati pa misona.

[3] Unalera mmodzi mwa ana ake, ndipo mwanayo anasanduka mkango wamphamvu. Unaphunzira kugwira nyama, ndipo unayamba kudya anthu.

[4] Anthu amitundu anamva za mkangowo, ndipo tsiku lina unagwa mʼmbuna mwawo. Iwo anawukoka ndi ngowe kupita nawo ku dziko la Igupto.

[5] “ ‘Amayi aja ataona kuti mwana ankamukhulupirira uja wagwidwa ndi kuti chiyembekezo chake chapita padera, amayiwo anatenganso mwana wina namusandutsa mkango wamphamvu.

[6] Unkayendayenda pakati pa mikango inzake, pakuti tsopano unali mkango wamphamvu. Unaphunzira kugwira nyama ndipo unayamba kudya anthu.

[7] Unagwetsa malinga awo, ndikuwononga mizinda yawo. Onse a mʼdzikomo anachita mantha chifukwa cha kubangula kwake.

[8] Pamenepo mitundu ya anthu, makamaka ochokera madera ozungulira, inabwera kudzalimbana nawo. Anawutchera ukonde wawo, ndipo tsiku lina unagwera mʼmbuna mwawo.

[9] Anawukoka ndi ngowe nawuponya mʼchitatanga. Anabwera nawo kwa mfumu ya ku Babuloni ndipo mfumuyo inawuponya mʼndende ndi cholinga choti liwu lake lisamamvekenso ku mapiri a Israeli.

[10] “ ‘Amayi ako anali ngati mpesa mʼmunda wamphesa wodzalidwa mʼmbali mwa madzi. Unabereka bwino ndipo unali ndi nthambi zambiri chifukwa cha kuchuluka kwa madzi.

[11] Nthambi zake zinali zolimba, zoyenera kupangira ndodo yaufumu. Unatalika nusomphoka pakati pa zomera zina. Unkaoneka bwino chifukwa cha kutalika kwake, ndi nthambi zake zambiri.

[12] Koma unazulidwa mwaukali ndipo unagwetsedwa pansi. Unawuma ndi mphepo ya kummawa, zipatso zake zinayoyoka; nthambi zake zolimba zinafota ndipo moto unapsereza mtengo wonse.

[13] Ndipo tsopano anawuwokeranso ku chipululu, dziko lowuma ndi lopanda madzi.

[14] Moto unatulukanso mu mtengomo ndi kupsereza nthambi ndi zipatso zake. Palibe nthambi yolimba inatsala pa mtengowo yoyenera kupangira ndodo yaufumu. Imeneyi ndi nyimbo yachisoni ndipo yasanduka nyimbo ya pa maliro.’ ”

Ezekieli — Chapters