Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:29

[1] Yehova anayankhulanso nane kuti,

[2] “Iwe mwana wa munthu, kodi mtengo wamphesa umapambana bwanji mtengo wina uliwonse? Nthambi zake zimapambana bwanji nthambi ina iliyonse.

[3] Mtengo umene uja nʼkupangira chiyani? Kodi anthu angathe kupangira chikhomo chokolekapo zinthu zawo?

[4] Taonani, ndi nkhuni chabe zosonkhera moto. Ukaponyedwa pa moto monga nkhuni ndi kuyaka mbali zonse ndi kusanduka makala, kodi ungagwiritsidwe ntchito ina iliyonse?

[5] Ngati pamene unali wosapsa sukanatheka kuwugwiritsa ntchito, nanga bwanji utapserera ndi moto, adzawugwiritsa ntchito bwanji?

[6] “Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Mtengo wamphesa ndidzawuponya mʼmoto monga ndimachitira ndi mitengo ina ya ku nkhalango. Momwemonso ndidzachita ndi anthu a ku Yerusalemu.

[7] Ndidzawalanga pamenepo ngakhale iwo atuluka pa moto, motowo udzawatenthabe. Ndipo pamene ndidzatsutsana nawo, mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

[8] Ine ndidzasandutsa dziko kukhala chipululu chifukwa anthu akhala osakhulupirika, akutero Ambuye Yehova.’ ”

Ezekieli — Chapters