Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:56

[1] Inu Yehova, kumbukirani zimene zinatichitikira; yangʼanani ndipo muone kunyozeka kwathu.

[2] Apereka cholowa chathu kwa obwera, nyumba zathu kwa alendo.

[3] Takhala amasiye ndi wopanda abambo, amayi athu ali ngati akazi amasiye.

[4] Tiyenera kugula madzi amene timamwa, nkhuni zathunso nʼzogula.

[5] Otilondola atigwira pakhosi; tafowoka ndipo sakutilola kupumula.

[6] Tinadzipereka kwa Aigupto ndi kwa Asiriya kuti tipeze chakudya.

[7] Makolo athu anachimwa ndipo anafa kale, koma chilango chawo chili pa ife.

[8] Akapolo akutilamulira, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe angatimasule mʼdzanja lawo.

[9] Timapeza chakudya chathu poyika miyoyo yathu pa chiswe chifukwa cha lupanga mʼchipululu.

[10] Khungu lathu latentha ngati uvuni mʼngʼanjo, chifukwa cha kuwawa kwa njala.

[11] Amayi agwiriridwa mu Ziyoni, ndi anamwali mʼmizinda ya Yuda.

[12] Akalonga athu akuwapachika pomangirira manja awo, akuluakulu sakuwalemekeza.

[13] Achinyamata akukakamizidwa kupera tirigu; anyamata akudzandira ndi mitolo ya nkhuni.

[14] Akuluakulu anachokapo pa chipata cha mzinda; achinyamata aleka nyimbo zawo.

[15] Chimwemwe chachoka mʼmitima yathu; kuvina kwathu kwasanduka maliro.

[16] Chipewa chathu chaufumu chagwa pamutu pathu. Tsoka kwa ife, chifukwa tachimwa!

[17] Mitima yathu yakomoka chifukwa cha zimenezi, chifukwa cha zinthu zimenezi maso athu sakuona bwino,

[18] pakuti phiri la Ziyoni, limene lasanduka bwinja, nkhandwe zikungoyendayendapo.

[19] Inu Yehova, lamulirani kwamuyaya; mpando wanu waufumu udzakhalabe ku mibadomibado.

[20] Chifukwa chiyani mumatiyiwala nthawi zonse? Chifukwa chiyani mwatitaya nthawi yayitali chotere?

[21] Yehova mutitembenuzire kwa Inu, kuti tibwerere; mukonzenso masiku athu akhale monga akale,

[22] pokhapokha ngati mwatitaya kotheratu, ndi kuti mwatikwiyira kobzola muyeso.

Maliro — Chapters