Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 7:00

[1] Ine ndine munthu amene ndaona masautso ndi ndodo ya ukali wake.

[2] Wandipititsa kutali ndipo wandiyendetsa mu mdima osati mʼkuwala;

[3] zoonadi anandikantha ndi dzanja lake mobwerezabwereza tsiku lonse.

[4] Wakalambitsa khungu langa ndi mnofu wanga, ndipo waphwanya mafupa anga.

[5] Wandizinga ndi kundizungulira ndi zowawa ndi zolemetsa.

[6] Wandikhazika mu mdima ngati amene anafa kale.

[7] Wandimangira khoma kotero kuti sindingathawe, wandimanga ndi maunyolo.

[8] Ngakhale pamene ndifuwula kapena kupempha chithandizo, amakana pemphero langa.

[9] Wanditsekera njira yanga ndi miyala yosema; ndipo wakhotetsa tinjira tanga.

[10] Wandidikirira ngati chimbalangondo, wandibisalira ngati mkango.

[11] Wandikokera pambali ndi kundingʼambangʼamba, ndipo wandisiya wopanda thandizo.

[12] Wakoka uta wake ndipo walunjikitsa mivi yake pa ine.

[13] Walasa mtima wanga ndi mivi ya mʼphodo mwake.

[14] Ndinakhala choseketsa cha anthu anga onse; amandinyodola mʼnyimbo zawo tsiku lonse.

[15] Wandidyetsa zowawa ndipo wandimwetsa ndulu.

[16] Wathyola mano anga ndi miyala; wandiviviniza mʼfumbi;

[17] Wandichotsera mtendere; ndayiwala kuti kupeza bwino nʼchiyani.

[18] Choncho ndikuti, “Ulemerero wanga wachoka ndi zonse zimene ndimayembekeza kwa Yehova.”

[19] Kukumbukira masautso anga ndi kusowa pokhala, zili ngati zowawa ndi ndulu.

[20] Ine ndikuzikumbukira bwino izi, ndipo moyo wanga wathedwa mʼkati mwanga.

[21] Komabe ndimakumbukira zimenezi, nʼchifukwa chake ndili ndi chiyembekezo.

[22] Ife sitinawonongekeretu chifukwa chikondi cha Yehova ndi chachikulu, ndi chifundo chake ndi chosatha.

[23] Zimaoneka zatsopano mmawa uliwonse; kukhulupirika kwanu nʼkwakukulu.

[24] Mu mtima mwanga ndimati, “Yehova ndiye zanga zonse; motero ndimamuyembekezera.”

[25] Yehova ndi wabwino kwa amene amayembekezera Iye, kwa munthu amene amafunafuna Iyeyo;

[26] nʼkwabwino kudikira chipulumutso cha Yehova modekha.

[27] Nʼkwabwino kuti munthu asenze goli pamene ali wamngʼono.

[28] Akhale chete pa yekha, chifukwa Yehova wamusenzetsa golilo.

[29] Abise nkhope yake mʼfumbi mwina chiyembekezo nʼkukhalapobe.

[30] Apereke tsaya lake kwa iye amene angamumenye, ndipo amuchititse manyazi.

[31] Chifukwa Ambuye satayiratu anthu nthawi zonse.

[32] Ngakhale amabweretsa zowawa, Iye adzawachitira chifundo, chifukwa chikondi chake ndi chosatha.

[33] Pakuti sabweretsa masautso mwadala, kapena zowawa kwa ana a anthu.

[34] Kuphwanya ndi phazi a mʼndende onse a mʼdziko,

[35] kukaniza munthu ufulu wake pamaso pa Wammwambamwamba,

[36] kumana munthu chiweruzo cholungama— kodi Ambuye saona zonsezi?

[37] Kodi ndani angayankhule zinthu nʼkuchitika ngati Ambuye sanavomereze?

[38] Kodi zovuta ndi zabwino sizituluka mʼkamwa mwa Wammwambamwamba?

[39] Kodi nʼchifukwa chiyani munthu aliyense wamoyo amadandaula akalangidwa chifukwa cha machimo ake?

[40] Tiyeni tisanthule ndi kuyesa njira zathu, ndipo tiyeni tibwerere kwa Yehova.

[41] Tiyeni tikweze mitima yathu ndi manja athu kwa Mulungu kumwamba ndipo tinene kuti:

[42] “Ife tachimwa ndi kuwukira ndipo inu simunakhululuke.

[43] “Mwadzikuta ndi mkwiyo ndi kutilondola ndipo mwatitha mopanda chifundo.

[44] Mwadzikuta mu mtambo kotero mapemphero athu sakukufikani.

[45] Mwatisandutsa zinyatsi ndi zinyalala pakati pa mitundu ya anthu.

[46] “Adani anthu atitsekulira pakamwa.

[47] Ife tadzazidwa ndi mantha pakuti tagwa mʼdzenje, tapasuka ndi kuwonongedwa.”

[48] Misozi mʼmaso mwanga ikungoti mbwembwembwe chifukwa anthu anga akuwonongedwa.

[49] Misozi idzatsika kosalekeza, ndipo sidzasiya,

[50] mpaka Yehova ayangʼane pansi kuchokera kumwamba ndi kuona.

[51] Mtima wanga ukupweteka poona zimenezi chifukwa cha akazi onse a mu mzinda.

[52] Akundisaka ngati mbalame, amene anali adani anga, popanda chifukwa.

[53] Ayesa kundipha pondiponya mʼdzenje ndi kundiponya miyala;

[54] madzi anamiza mutu wanga ndipo ndinkaganiza kuti imfa yayandikira.

[55] Ndinayitana dzina lanu Inu Yehova, kuchokera mʼdzenje lozama.

[56] Inu munamva kudandaula kwanga. “Mundimvere kulira kwanga kopempha thandizo.”

[57] Munafika pafupi pamene ndinakuyitanani, ndipo munati, “Usaope.”

[58] Inu Ambuye munandiwombola ku mlandu wanga; munapulumutsa moyo wanga.

[59] Yehova, mwaona zoyipa zimene andichitira. Mundiweruzire ndinu!

[60] Mwaona kuzama kwa kubwezera kwawo, chiwembu chawo chonse pa ine.

[61] Inu Yehova mwamva kunyoza kwawo, chiwembu chawo chonse pa ine,

[62] manongʼonongʼo a adani anga ondiwukira ine tsiku lonse.

[63] Tawaonani! Kaya ali pansi kapena kuyimirira, akundinyoza mu nyimbo zawo.

[64] Inu Yehova, muwabwezere chowayenera, chifukwa cha zimene manja awo achita.

[65] Phimbani mitima yawo, ndipo matemberero anu akhale pa iwo!

[66] Muwalondole mwaukali ndipo muwawonongeretu pa dziko lapansi.

Maliro — Chapters