Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:47

[1] Ndipo Yehova anayankhula ndi Yona kachiwiri kuti,

[2] “Nyamuka, pita ku mzinda waukulu wa Ninive ndipo ukalalikire uthenga umene ndikupatsa.”

[3] Yona anamvera mawu a Yehova ndipo anapita ku Ninive. Tsono Ninive unali mzinda waukulu kwambiri; wofunika masiku atatu kuwudutsa.

[4] Yona analowa mu mzindawo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi. Iye ankalalikira kuti, “Atsala masiku makumi anayi kuti Ninive awonongedwe.”

[5] Anthu a ku Ninive anakhulupirira Mulungu. Analengeza kuti aliyense, wamkulu ndi wamngʼono yemwe asale zakudya ndipo avale chiguduli.

[6] Mfumu ya ku Ninive itamva nkhaniyi, inatsika pa mpando wake waufumu, nivula mkanjo wake waufumu ndipo inavala chiguduli ndi kukhala pansi pa fumbi.

[7] Tsono mfumuyo inalengeza mu Ninive kuti, “Mwa lamulo lochokera kwa mfumu ndi akalonga ake: “Munthu aliyense kapenanso nyama, ngʼombe kapena nkhosa, zisadye kanthu kalikonse; musazilole kuti zidye kapena kumwa.

[8] Koma anthu avale ziguduli, ndipo nyamanso aziveke ziguduli. Munthu aliyense azifuwula kwa Mulungu ndi mphamvu zake zonse. Anthuwo asiye makhalidwe awo oyipa ndi machitidwe achiwawa.

[9] Angadziwe ndani? Mwina Mulungu nʼkutikhululukira ndipo mwa chifundo chake nʼkuleka kutikwiyira, ifeyo osawonongedwa.”

[10] Mulungu ataona zimene anthuwo anachita, ndi mmene anasiyira makhalidwe awo oyipa, anawachitira chifundo ndipo sanabweretse chiwonongeko chimene anawaopseza nacho.

Yona — Chapters