Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:27

[1] Yona ali mʼmimba mwa chinsomba chija anapemphera kwa Yehova Mulungu wake.

[2] Iye anati: “Pamene ndinali mʼmavuto anga ndinayitana Yehova, ndipo Iye anandiyankha. Ndili ku dziko la anthu akufa ndinapempha thandizo, ndipo Inu munamva kulira kwanga.

[3] Munandiponya mʼnyanja yozama, mʼkati mwenimweni mwa nyanja, ndipo madzi oyenda anandizungulira; mafunde anu onse ndi mkokomo wake zinandimiza.

[4] Ndinati, ‘Ine ndachotsedwa pamaso panu; komabe ndidzayangʼananso ku Nyumba yanu yopatulika.’

[5] Madzi wondimiza anandichititsa mantha, nyanja yozama inandizungulira; udzu wa mʼmadzi zinakuta mutu wanga.

[6] Ndinatsikira kunsi ndithu, mʼtsinde mwa mapiri; mipiringidzo ya dziko inanditsekereza kosatha. Koma Inu munatulutsa moyo wanga mʼmandamo, Inu Yehova Mulungu wanga.

[7] “Pamene moyo wanga umachoka mwa ine, ine ndinakumbukira Inu Yehova, ndipo pemphero langa linafika kwa inu, ku Nyumba yanu yopatulika.

[8] “Iwo amene amagwiritsitsa mafano achabechabe amataya chisomo chawo.

[9] Koma ine ndidzapereka kwa Inu nsembe ndikuyimba nyimbo yamayamiko. Chimene ndinalonjeza ndidzachikwaniritsa. Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.”

[10] Ndipo Yehova analamula chinsomba chija, ndipo chinakamusanza Yonayo mʼmbali mwa nyanja.

Yona — Chapters