[1] “Masiku amenewo ndiponso nthawi imeneyo, nditadzabwezeretsanso Yerusalemu ndi Yuda mʼchimake,
[2] ndidzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse ndipo ndidzawabweretsa ku Chigwa cha Yehosafati. Kumeneko ndidzawaweruza chifukwa cha cholowa changa, anthu anga Aisraeli, pakuti anabalalitsa anthu anga pakati pa mitundu ya anthu ndikugawa dziko langa.
[3] Anagawana anthu anga pochita maere ndipo anyamata anawasinthanitsa ndi akazi achiwerewere; anagulitsa atsikana chifukwa cha vinyo kuti iwo amwe.
[4] “Kodi tsopano inu a ku Turo ndi Sidoni ndi madera onse a Filisitiya, muli ndi chiyani chotsutsana nane? Kodi mukundibwezera pa zinthu zimene ndakuchitirani? Ngati inu mukundibwezera, Ine ndidzabwezera zochita zanu mofulumira ndi mwachangu pa mitu yanu.
[5] Pakuti munatenga siliva ndi golide wanga ndi kupita nacho chuma changa chamtengowapatali ku nyumba zanu zopembedzera mafano.
[6] Inu munagulitsa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu kwa Agriki, kuti apite kutali ndi malire a dziko lawo.
[7] “Taonani, Ine ndidzawachotsa kumalo kumene munawagulitsako, ndipo ndidzabwezera zimene mwachita pa mitu yanu.
[8] Ndidzagulitsa ana anu aamuna ndi ana anu aakazi kwa anthu a ku Yuda, ndipo iwo adzawagulitsa kwa Aseba, mtundu wa anthu okhala kutali.” Yehova wayankhula.
[9] Lengezani izi pakati pa anthu a mitundu ina: Konzekerani nkhondo! Dzutsani ankhondo amphamvu! Asilikali onse afike pafupi ndipo ayambe nkhondo.
[10] Sulani makasu anu kuti akhale malupanga ndipo zikwanje zanu zikhale mikondo. Munthu wofowoka anene kuti, “Ndine wamphamvu!”
[11] Bwerani msanga, inu anthu a mitundu yonse kuchokera ku mbali zonse, ndipo musonkhane kumeneko. Tumizani ankhondo anu Yehova!
[12] “Mitundu ya anthu idzuke; ipite ku Chigwa cha Yehosafati, pakuti kumeneko Ine ndidzakhala ndikuweruza anthu a mitundu yonse yozungulira.
[13] Tengani chikwakwa chodulira tirigu, pakuti mbewu zakhwima. Bwerani dzapondeni mphesa, pakuti mopsinyira mphesa mwadzaza ndipo mitsuko ikusefukira; kuyipa kwa anthuwa nʼkwakukulu kwambiri!”
[14] Chigulu cha anthu, chigulu cha anthu, mʼchigwa cha chiweruzo! Pakuti tsiku la Yehova layandikira mʼchigwa cha chiweruzo.
[15] Dzuwa ndi mwezi zidzadetsedwa, ndipo nyenyezi sizidzawalanso.
[16] Yehova adzabangula kuchokera mu Ziyoni ndipo mawu ake adzamveka ngati bingu kuchokera mu Yerusalemu; dziko lapansi ndi thambo zidzagwedezeka. Koma Yehova adzakhala pothawira pa anthu ake, linga la anthu a ku Israeli.
[17] “Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wanu, ndimakhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika. Yerusalemu adzakhala wopatulika; alendo sadzamuthiranso nkhondo.
[18] “Tsiku limenelo mapiri adzachucha vinyo watsopano, ndipo zitunda zidzayenderera mkaka; mitsinje yonse ya ku Yuda idzadzaza ndi madzi. Kasupe adzatumphuka mʼnyumba ya Yehova ndipo adzathirira Chigwa cha Sitimu.
[19] Koma Igupto adzasanduka bwinja, Edomu adzasanduka chipululu, chifukwa cha nkhondo imene anathira anthu a ku Yuda mʼdziko limene anakhetsa magazi a anthu osalakwa.
[20] Koma Yuda adzakhala ndi anthu mpaka muyaya ndi Yerusalemu ku mibadomibado.
[21] Kukhetsa magazi kwawo kumene Ine sindinakhululuke ndidzakhululuka.” Yehova amakhala mu Ziyoni!