[1] Yehova anayankhula ndi Yoweli mwana wa Petueli.
[2] Inu akuluakulu, imvani izi; mvetserani, nonse amene mumakhala mʼdziko. Kodi zinthu zokhala ngati izi zinayamba zaonekapo mʼnthawi yanu, kapena mʼnthawi ya makolo anu?
[3] Muwafotokozere ana anu, ndipo ana anuwo afotokozere ana awo, ndipo ana awo adzafotokozere mʼbado winawo.
[4] Chimene dzombe losamera mapiko lasiya dzombe lowuluka ladya; chimene dzombe lowuluka lasiya dzombe lalingʼono ladya; chimene dzombe lalingʼono lasiya chilimamine wadya.
[5] Dzukani, inu zidakwa ndipo mulire! Lirani mofuwula, inu nonse amene mumamwa vinyo; lirani mofuwula chifukwa cha vinyo watsopano, pakuti wachotsedwa pakamwa panu.
[6] Mtundu wa anthu wathira nkhondo dziko langa, wamphamvu ndi wosawerengeka; uli ndi mano a mkango, zibwano za mkango waukazi.
[7] Wawononga mphesa zanga ndipo wathyola mitengo yanga ya mkuyu. Wakungunula makungwa ake ndi kuwataya, kusiya nthambi zake zili mbee.
[8] Lirani ngati namwali wovala chiguduli, chifukwa cha mwamuna wa utsikana wake.
[9] Chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa sizikuperekedwa ku nyumba ya Yehova. Ansembe akulira, amene amatumikira pamaso pa Yehova.
[10] Minda yaguga, nthaka yauma; tirigu wawonongeka, vinyo watsopano watha, mitengo ya mafuta yauma.
[11] Khalani ndi nkhawa, inu alimi, lirani mofuwula inu alimi a mphesa; imvani chisoni chifukwa cha tirigu ndi barele, pakuti zokolola za mʼmunda zawonongeka.
[12] Mpesa wauma ndipo mtengo wamkuyu wafota; makangadza, kanjedza ndi mitengo ya apulosi, mitengo yonse ya mʼmunda yauma. Ndithudi chimwemwe cha anthu chatheratu.
[13] Inu ansembe, valani ziguduli ndipo lirani; lirani mofuwula, inu amene mumatumikira pa guwa lansembe. Bwerani, fundani ziguduli usiku wonse, inu amene mumatumikira pamaso pa Mulungu wanga; pakuti chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa sizikupezekanso mʼnyumba ya Mulungu wanu.
[14] Lengezani tsiku lopatulika losala zakudya, itanani msonkhano wopatulika. Sonkhanitsani akuluakulu ndi anthu onse okhala mʼdziko ku nyumba ya Yehova Mulungu wanu ndipo alirire Yehova.
[15] Kalanga ine tsikulo! Pakuti tsiku la Yehova layandikira; lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuzonse.
[16] Kodi chakudya chathu sichachotsedwa ife tikuona? Kodi mʼnyumba ya Mulungu wathu simulibe chimwemwe ndi chisangalalo?
[17] Mbewu zikunyala poti pansi ndi powuma. Nyumba zosungiramo zinthu zawonongeka; nkhokwe zapasuka popeza tirigu wauma.
[18] Taonani mmene zikulirira ziweto; ngʼombe zikungoyenda uku ndi uku chifukwa zilibe msipu; ngakhalenso nkhosa zikusauka.
[19] Kwa Inu Yehova ndilirira, pakuti moto wapsereza msipu wakuthengo, malawi amoto apsereza mitengo yonse ya mʼtchire.
[20] Ngakhale nyama zakuthengo zikulirira Inu; timitsinje tonse taphwa ndipo moto wapsereza msipu wa kuthengo.