Listen to this chapter • 1:10
[1] Uwu ndi uthenga umene mneneri Yeremiya anawuza Baruki mwana wa Neriya mʼchaka cha chinayi cha Yehoyakimu mwana wa mwana ya Yosiya kuti alembe mʼbuku.
[2] “Yehova Mulungu wa Israeli, akunena kwa iwe Baruki kuti:
[3] Iwe unati, ‘Kalanga ine! Yehova wawonjezera chisoni pa mavuto anga. Ine ndatopa ndi kubuwula ndipo sindikupeza mpumulo.’ ”
[4] Koma Yehova akukuwuza kuti, “Ndidzagwetsa chimene ndinamanga ndipo ndidzazula chimene ndinadzala. Ndidzachita zimenezi mʼdziko lonse.
[5] Kodi tsono ukudzifunira wekha zinthu zazikulu? Usadzifunire. Pakuti ndidzagwetsa mavuto pa anthu onse, koma ndidzasunga moyo wako kulikonse kumene ungadzapite.”
Yeremiya — Chapters
13:5328:3936:4146:5657:3167:2977:2785:3796:27105:29115:20124:33136:24146:06155:49165:33177:25185:24194:16204:52214:09227:42239:51242:29258:29265:58275:30284:01297:57305:45319:223210:06335:37346:14355:02367:58374:52386:45394:16405:09415:01425:21433:28448:49451:10467:32471:554811:094910:575012:475114:38528:15