[1] “Tsoka kwa abusa amene akuwononga ndi kubalalitsa nkhosa za pabusa panga!” akutero Yehova.
[2] Nʼchifukwa chake Yehova, Mulungu wa Israeli, ponena za abusa amene akuweta anthu anga akuti, “Mwabalalitsa ndi kumwaza nkhosa zanga. Komanso simunazisamale bwino. Choncho ndidzakulangani chifukwa cha machimo anu,” akutero Yehova.
[3] “Pambuyo pake Ine mwini wakene ndidzasonkhanitsa nkhosa zanga zotsala, kuzichotsa ku mayiko onse kumene ndinazibalalitsira ndi kuzibweretsanso ku msipu wawo. Kumeneko zidzaswana ndi kuchulukana.
[4] Ndidzazipatsa abusa amene adzaziweta, ndipo sizidzaopanso kapena kuchita mantha, ndipo palibe imene idzasochera,” akutero Yehova.
[5] Yehova akuti, “Masiku akubwera, pamene ndidzaphukitsira Davide Nthambi yowongoka. Imeneyi ndiye mfumu imene idzalamulira mwanzeru, mwachilungamo ndi mosakondera mʼdziko.
[6] Pa masiku a ulamuliro wake Yuda adzapulumuka ndipo Israeli adzakhala pamtendere. Dzina limene adzamutcha ndi ili: Yehova ndiye Chilungamo Chathu.
[7] Choncho, masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene anthu sadzanenanso polumbira kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli ku Igupto,’
[8] koma adzanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa zidzukulu za Israeli ku dziko lakumpoto ndi ku mayiko konse kumene anawabalalitsira.’ Ndipo iwo adzawabweretsa ku dziko lawolawo.”
[9] Kunena za aneneri awa: Mtima wanga wasweka; mʼnkhongono mwati zii. Ndakhala ngati munthu woledzera, ngati munthu amene wasokonezeka ndi vinyo, chifukwa cha Yehova ndi mawu ake opatulika.
[10] Dziko ladzaza ndi anthu achigololo; lili pansi pa matemberero. Dziko lasanduka chipululu ndipo msipu wawuma. Aneneri akuchita zoyipa ndipo akugwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika.
[11] “Mneneri ngakhale wansembe onse sapembedza Yehova. Amachita zoyipa ngakhale mʼnyumba yanga,” q4 akutero Yehova.
[12] “Nʼchifukwa chake njira zawo zidzakhala zoterera; adzawapirikitsira ku mdima ndipo adzagwera kumeneko. Adzaona zosaona mʼnthawi ya chilango chawo,” q4 akutero Yehova.
[13] “Pakati pa aneneri a ku Samariya ndinaona chonyansa ichi: Ankanenera mʼdzina la Baala ndipo anasocheretsa anthu anga, Aisraeli.
[14] Ndipo pakati pa aneneri a ku Yerusalemu ndaonapo chinthu choopsa kwambiri: amachita chigololo, amanena bodza ndipo amalimbitsa mtima anthu ochita zoyipa. Choncho palibe amene amasiya zoyipa zake. Kwa Ine anthu onsewa ali ngati a ku Sodomu ndi Gomora.”
[15] Choncho ponena za aneneriwa Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ndidzawadyetsa zakudya zowawa ndi kuwamwetsa madzi a ndulu, chifukwa uchimo umene wafalikira mʼdziko lonse ndi wochokera kwa aneneri a ku Yerusalemuwa.”
[16] Koma Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Musamvere zimene aneneri amenewa akulosera kwa inu; zomwe aloserazo nʼzachabechabe. Iwo akungoyankhula za masomphenya a mʼmitima mwawo basi, osati zochokera kwa Yehova.
[17] Iwo amapita ndi kumakawuza amene amandinyoza Ine kuti, ‘zinthu zidzakuyenderani bwino.’ Kwa iwo amene amawumirira kutsata zofuna za mitima yawo amakawawuza kuti, ‘palibe choyipa chimene chidzakugwereni.’ ”
[18] Ine ndikuti, “Koma ndani wa iwo amene anakhalapo mu msonkhano wa Yehova? Ndani anaonapo kapena kumvapo mawu ake? Ndani mwa iwo analabadirako za mawu ake ndi kuwamvera?
[19] Taonani ukali wa Yehova uli ngati chimphepo chamkuntho, inde ngati namondwe. Ndipo adzakantha mitu ya anthu oyipa.
[20] Mkwiyo wa Yehova sudzaleka mpaka atachita zonse zimene anatsimikiza mu mtima mwake. Mudzazizindikira bwino zimenezi masiku akubwerawa.”
[21] Yehova anati, “Ine sindinatume aneneri amenewa, komabe iwo athamanga uku ndi uku kulalikira uthenga wawo; Ine sindinawayankhule, komabe iwo ananenera.
[22] Iwo akanakhala pa msonkhano wanga ndiye kuti akanamayankhula mawu anga kwa anthu anga. Komanso bwenzi atawachotsa anthu anga mʼnjira zawo zoyipa kuti aleke machimo awo.”
[23] Yehova akuti, “Kodi ndimakhala Mulungu pokhapokha ndikakhala pafupi, ndiye sindine Mulungu?
[24] Kodi wina angathe kubisala Ine osamuona?” “Kodi Ine sindili ponseponse kumwamba ndi dziko lapansi?” q4 Akutero Yehova.
[25] “Ndamva zimene aneneri akuyankhula. Iwo amalosera zabodza mʼdzina langa nʼkumati, ‘Ndalota! Ndalota!’
[26] Kodi zabodzazi zidzakhalabe mʼmitima ya aneneriwa mpaka liti? Iwotu amalosera zonyenga za mʼmitima yawo.
[27] Aneneriwa amakhulupirira kuti anthu anga adzayiwala mawu anga akamamva za maloto awo amene amayankhulana ngati mmene anachitira makolo awo popembedza Baala.
[28] Mneneri amene ali ndi maloto afotokoze malotowo. Koma iye amene ali ndi mawu anga alalikire mawuwo mokhulupirika. Kodi phesi lingafanane ndi chimanga?
[29] Kodi suja mawu anga amatentha ngati moto? Suja mawu anga amaphwanya monga ichitira nyundo kuphwanya miyala?” Akutero Yehova.
[30] Yehova akuti, “Nʼchifukwa chake, Ine ndikudana nawo aneneri amene amaberana okhaokha mawu nʼkumati mawuwo ndi a Yehova.”
[31] Yehova akuti, “Inde, Ine ndikudana ndi aneneri amene amakonda kuyankhula zabodza nʼkumanena kuti, ‘Amenewa ndi mawu a Yehova.’ ”
[32] Yehova akuti, “Ndithudi, Ine ndikudana ndi aneneri a maloto abodzawa. Iwo amafotokoza malotowo nʼkumasocheretsa anthu anga ndi bodza lawo losachita nalo manyazilo, chonsecho Ine sindinawatume kapena kuwalamula. Iwo sathandiza anthuwa ndi pangʼono pomwe,” akutero Yehova.
[33] Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Anthu awa, kapena mneneri, kapenanso wansembe, akakufunsa kuti, ‘Kodi uthenga wolemetsa wa Yehova ukuti chiyani?’ uwawuze kuti, ‘Inuyo ndinu katundu wolemetsa Yehova, ndipo adzakutayani.’
[34] Ngati mneneri kapena wansembe kapenanso munthu wina aliyense anena kuti, ‘Uthenga wolemetsa wa Yehova ndi uwu,’ Ine ndidzalanga munthu ameneyo pamodzi ndi banja lake.
[35] Koma chimene aliyense wa inu azifunsa kwa mnzake kapena mʼbale wake ndi ichi: ‘Kodi Yehova wayankha chiyani?’ kapena ‘Yehova wayankhula chiyani?’
[36] Koma musanenenso kuti ‘nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ chifukwa mawu a munthu aliyense ndiwo uthenga wa iye mwini, kotero kuti inu mumakhotetsa mawu a Mulungu wamoyo, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wathu.
[37] Tsono iwe Yeremiya udzamufunse mneneri kuti, ‘Kodi Yehova wakuyankha chiyani?’ kapena, ‘Kodi Yehova wayankhula chiyani?’
[38] Ngati mudzanena kuti, ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ ndiye tsono Yehova akuti, ‘Popeza mwagwiritsa ntchito mawu akuti: Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova, mawu amene ndinakuletsani kuti musawatchule,
[39] ndiye kuti Ine ndidzakunyamulani ngati katundu nʼkukuponyani kutali. Ndidzakuchotsani pamaso panga, inuyo pamodzi ndi mzinda umene ndinakupatsani inu ndi makolo anu.
[40] Ndidzakunyozani mpaka muyaya. Ndidzakuchititsani manyazi osayiwalika.’ ”