Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:52

[1] Fundo yayikulu pa zimene tikunenazi ndi iyi: Tili naye ife Mkulu wa ansembe, amene anakhala ku dzanja lamanja la mpando waufumu wa Mulungu Waulemerero kumwamba.

[2] Ndipo akutumikira mʼmalo opatulika, mu Tenti yeniyeni yoyikidwa ndi Ambuye, osati ndi munthu.

[3] Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa kuti azipereka mphatso ndi nsembe kwa Mulungu, ndipo kunali koyenera kuti wansembe wathunso akhale nʼkanthu kopereka.

[4] Ngati iye akanakhala pa dziko lapansi, sakanakhala wansembe pakuti alipo kale anthu amene amapereka mphatso zolembedwa mʼMalamulo.

[5] Iwo amatumikira pamalo opatulika amene ndi chithunzi ndi chifanizo cha zimene zili kumwamba. Ichi ndi chifukwa chake Mose anachenjezedwa pamene anali pafupi kumanga Tenti: “Uwonetsetse kuti wapanga zonse monga momwe ndikukuonetsera pa phiri pano.”

[6] Koma Yesu analandira utumiki wopambana kuposa wawo monga Iyenso ali Nkhoswe ya pangano lopambana kuposa lakale lija, chifukwa pangano latsopano lakhazikika pa malonjezano opambana kwambiri.

[7] Ngati pangano loyamba lija likanakhala langwiro, sipakanafunikanso lina mʼmalo mwake.

[8] Koma Mulungu anapeza zolakwika pakati pa anthu ndipo anati, “Masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzachita pangano latsopano ndi Aisraeli ndiponso nyumba ya Yuda.

[9] Silidzakhala ngati pangano limene ndinachita ndi makolo awo, pamene ndinawagwira padzanja nʼkuwatulutsa ku Igupto chifukwa iwo sanasunge pangano langa lija ndipo Ine sindinawasamalire, q4 akutero Ambuye.

[10] Tsono ili ndi pangano ndidzapangane ndi nyumba ya Israeli: Atapita masiku amenewa, akutero Ambuye, Ine ndidzayika malamulo anga mʼmaganizo mwawo, ndi kulemba mʼmitima mwawo. Ine ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo iwo adzakhala anthu anga.

[11] Sipadzafunikanso wina kuti aphunzitse mnzake, kapena munthu kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, udziwe Ambuye chifukwa onse adzandidziwa, kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu.

[12] Pakuti Ine ndidzawakhululukira zoyipa zawo, ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.”

[13] Ponena kuti, pangano “latsopano” Mulungu wapanga pangano loyamba lija kukhala lotha ntchito, ndipo chilichonse chimene chayamba kutha ntchito ndi kukalamba, chili pafupi kuchokeratu.

Kalata Yolembera Ahebri — Chapters