Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:34

[1] Nʼchifukwa chake abale oyera mtima, amenenso munayitanidwa ndi kumwamba, lingalirani za Yesu amene ndi Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chikhulupiriro chimene timavomereza.

[2] Iye anali wokhulupirika kwa Mulungu amene anamupatsa udindowo, monga momwe Mose anali wokhulupirika mʼnyumba yonse ya Mulungu.

[3] Yesu anapezeka woyenera kulandira ulemu waukulu kuposa Mose, monga momwemonso womanga nyumba amalandira ulemu waukulu kuposa nyumbayo.

[4] Pakuti nyumba iliyonse imamangidwa ndi munthu wina, koma amene anapanga zonse ndi Mulungu.

[5] Mose anali wokhulupirika monga mtumiki mʼnyumba yonse ya Mulungu, kuchitira umboni zimene zidzayankhulidwe mʼtsogolo.

[6] Koma Khristu ndi wokhulupirika monga mwana pa nyumba ya Mulungu. Ndipo ndife nyumba yake ngati tipitirire kulimbika mtima ndi kunyadira zomwe tikuyembekerazo.

[7] Tsono monga Mzimu Woyera akuti, “Lero mukamva mawu ake,

[8] musawumitse mitima yanu ngati munachitira pamene munawukira, pa nthawi yoyesedwa mʼchipululu.

[9] Pamene makolo anu anandiputa ndi kundiyesa, ndipo kwa zaka makumi anayi anaona zimene Ine ndinachita.

[10] Nʼchifukwa chake ndinawukwiyira mʼbadowo, ndipo Ine ndinati, ‘Nthawi zonse mitima yawo imasochera, ndipo iwo sadziwa njira zanga.’

[11] Kotero Ine ndinalumbira nditakwiya kuti, ‘Iwo sadzalowa mu mpumulo wanga.’ ”

[12] Abale samalani, kuti pasapezeke wina aliyense mwa inu wokhala ndi mtima woyipa ndi wosakhulupirira, womulekanitsa ndi Mulungu wamoyo.

[13] Koma muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku, ikanalipo nthawi imene imatchedwa kuti “Lero” kuti aliyense wa inu mtima wake usawumitsidwe ndi chinyengo cha tchimo.

[14] Pakuti timakhala anzake a Khristu, ngati tigwiritsitsa mpaka potsiriza chitsimikizo chimene tinali nacho pachiyambi.

[15] Monga kunanenedwa kuti, “Lero ngati mumva mawu ake, musawumitse mitima yanu ngati momwe munachitira pamene munawukira.”

[16] Nanga amene anamva ndi kuwukira anali ndani? Kodi si onse amene Mose anawatulutsa mu Igupto?

[17] Nanga amene Mulungu anawakwiyira zaka makumi anayi anali ndani? Kodi si anthu amene anachimwa, amene mitembo yawo inatsala mʼchipululu muja?

[18] Nanga Mulungu ankanena za ndani kuti sadzalowa mu mpumulo wake? Pajatu ankanena za anthu amene sanamvere aja.

[19] Tsono ife tikuona kuti sanalowe chifukwa cha kusakhulupirika kwawo.

Kalata Yolembera Ahebri — Chapters