Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 6:46

[1] Chimene ndikunena ndi chakuti, ngati mlowamʼmalo akali wamngʼono, sasiyana ndi kapolo, ngakhale kuti chuma chonse ndi chake.

[2] Mwanayo ayenera kumvera omulera ndiponso anthu oyangʼanira chuma mpaka nthawi imene abambo ake anakhazikitsa.

[3] Chomwechonso, ife pamene tinali ana, tinali akapolo a miyambo ya dziko lapansi.

[4] Koma nthawi itakwana, Mulungu anatumiza Mwana wake, wobadwa mwa mayi, wobadwa pansi pa lamulo,

[5] kudzawombola amene anali pansi pa lamulo, kuti tilandiridwe monga ana.

[6] Ndipo popeza ndinu ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake kuti alowe mʼmitima mwathu, Mzimu amene amafuwula kuti,“Abba, Atate.”

[7] Choncho sindiwenso kapolo, koma mwana wa Mulungu. Tsono popeza ndiwe mwana wake, Mulungu wakusandutsanso mlowamʼmalo.

[8] Koma poyamba pamene simunkamudziwa Mulungu, munali akapolo a zimene mwachilengedwe si milungu.

[9] Koma tsopano pakuti mukumudziwa Mulungu, kapena ndinene kuti Mulungu akukudziwani, nʼchifukwa chiyani mukubwereranso ku miyambo yofowoka ndi yomvetsa chisoni? Kodi mukufuna musandukenso akapolo?

[10] Mumasunga masiku, miyezi ndi nyengo ndi zaka.

[11] Ine ndikuopa kuti mwina ntchito zanga pa inu ndinagwira pachabe.

[12] Abale, ndikukudandaulirani, mukhale ngati ine, popeza ine ndinakhala ngati inu. Inu simunandilakwire.

[13] Monga inu mukudziwa ndinkakulalikirani Uthenga Wabwino ndili wofowoka.

[14] Ngakhale kuti matendawo anali ngati mayesero kwa inu, simunandinyoze kapena kunyansidwa nane. Komatu inu munandilandira ngati kuti ndinali mngelo wa Mulungu, ngati kuti ndinali Khristu Yesu mwini.

[15] Kodi chimwemwe chanu chonse chija chili kuti? Ine nditha kuchitira umboni kuti, ngati kukanatheka, inu mukanakolowola maso anu ndi kundipatsa.

[16] Kodi tsopano ine ndasanduka mdani wanu chifukwa ndakuwuzani choonadi?

[17] Anthu amenewo akuchita changu kuti akukopeni, koma changu chawocho sichabwino. Chimene iwo akufuna ndi chakuti akuchotseni inu kwa ife, kuti mukachite changu powathandiza iwowo.

[18] Nʼkwabwino kuchita changu, ngati cholingacho chili chabwino ndi kukhala otero nthawi zonse osati pokhapo pamene ine ndili ndi inu.

[19] Ana anga okondedwa, inu amene ine ndikukumveraninso zowawa za kubereka kufikira Khristu atawumbidwa mwa inu,

[20] ine ndikanakonda ndikanakhala nanu tsopano kuti ndisinthe mawu anga, chifukwa ndathedwa nanu nzeru.

[21] Tandiwuzani, inu, abale amene mukufuna kukhala pansi pa lamulo, kodi simukudziwa chimene lamulo limanena?

[22] Pakuti zinalembedwa kuti Abrahamu anali ndi ana aamuna awiri, wina mayi wake anali kapolo ndipo wina mayi wake anali mfulu.

[23] Mwana wake wobadwa mwa kapolo anabadwa mwathupi; koma mwana wake wobadwa mwa mfulu anabadwa monga mwa lonjezo.

[24] Zinthu izi zinali ngati fanizo, pakuti amayi awiriwa akuyimira mapangano awiri. Pangano limodzi ndi lochokera mʼPhiri la Sinai, ndiye Hagara, ndipo amabereka ana amene ndi akapolo.

[25] Tsono Hagara, akuyimira Phiri la Sinai ku Arabiya amene afanizidwa ndi mzinda wa Yerusalemu wa lero, chifukwa ali mu ukapolo pamodzi ndi ana ake.

[26] Koma Yerusalemu wakumwamba ndiye mfulu, ndipo ndiye mayi wathu.

[27] Pakuti kwalembedwa kuti, “Sangalala, iwe mayi wosabala, amene sunabalepo mwana; imba nthungululu ndi kufuwula mwachimwemwe, iwe amene sunamvepo ululu wa pobereka; chifukwa mkazi wosiyidwa adzakhala ndi ana ambiri kuposa mkazi wokwatiwa.”

[28] Tsono inu abale, ndinu ana alonjezo ngati Isake.

[29] Nthawi imeneyo mwana wobadwa mwathupi anazunza mwana wobadwa mwamphamvu za Mzimu. Zili chimodzimodzinso lero.

[30] Kodi Malemba akuti chiyani? “Muchotse kapoloyo pamodzi ndi mwana wake, chifukwa mwana wa kapolo sadzagawana chuma ndi mwana wamfulu.”

[31] Chifukwa chake, abale, ife sindife ana akapolo, koma ana a mfulu.

Kalata ya Paulo Yolembera Agalatiya — Chapters