[1] Agalatiya opusa inu, anakulodzani ndani? Tinamuonetsa poyera pamaso panu Yesu Khristu monga wopachikidwa pa mtanda.
[2] Ine ndikufuna ndiphunzire kuchokera kwa inu chinthu chimodzi ichi: Kodi munalandira Mzimu pochita ntchito za lamulo, kapena pokhulupirira zimene munamva?
[3] Kani ndinu opusa chotere? Inu mutayamba ndi Mzimu, kodi mukufuna kutsiriza ndi ntchito zathupi?
[4] Kodi munavutika kwambiri pachabe, ngati kunali kwachabedi?
[5] Kodi Mulungu amene anakupatsani Mzimu wake ndi kuchita zodabwitsa pakati panu, amachita zimenezi chifukwa mumachita ntchito za lamulo kapena chifukwa mumakhulupirira zimene munamva?
[6] Nʼchimodzimodzinso Abrahamu, “Iye anakhulupirira Mulungu, ndipo Mulungu anamutenga kukhala wolungama.”
[7] Tsono zindikirani kuti amene akhulupirira, ndi ana a Abrahamu.
[8] Malemba anaonetseratu kuti Mulungu adzalungamitsa anthu a mitundu ina mwachikhulupiriro, ndipo ananeneratu Uthenga Wabwino kwa Abrahamu kuti, “Mitundu yonse ya anthu idzadalitsika kudzera mwa iwe.”
[9] Choncho iwo amene ali ndi chikhulupiriro ndi odalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu, munthu wachikhulupiriro.
[10] Onse amene amadalira ntchito za lamulo ndi otembereredwa, pakuti zalembedwa mʼBuku la Malamulo kuti, “Ndi wotembereredwa aliyense amene sachita zonse zimene zalembedwa mʼBuku la Malamulo.”
[11] Chodziwikiratu nʼchakuti palibe amene amalungamitsidwa pamaso pa Mulungu ndi lamulo, chifukwa, “Wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.”
[12] Koma chikhulupiriro si Malamulo, chifukwa Malemba akuti, “Munthu amene achita zinthu izi adzakhala ndi moyo pozichita.”
[13] Khristu anatiwombola ku temberero la lamulo pokhala temberero mʼmalo mwathu, pakuti analemba kuti, “Aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa.”
[14] Iye anatiwombola ife ndi cholinga chakuti madalitso woperekedwa kwa Abrahamu abwere kwa anthu a mitundu ina kudzera mwa Khristu Yesu, kuti ndi chikhulupiriro tilandire lonjezo la Mzimu.
[15] Abale, ndiloleni ndipereke chitsanzo cha zochitika mʼmoyo wa tsiku ndi tsiku. Pangano likakhazikitsidwa palibe amene angachotsepo kapena kuwonjezerapo, choncho ndi chimodzimodzi pa nkhani iyi.
[16] Malonjezo awa anaperekedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake. Malemba sakunena kuti, “kwa mbewu zake,” kutanthauza anthu ambiri, koma, “kwa mbewu yako,” kutanthauza munthu mmodzi, amene ndi Khristu.
[17] Chimene ndikutanthauza ine ndi ichi: Malamulo amene anabwera patatha zaka 430, sangathetse pangano limene linakhazikitsidwa kale ndi Mulungu ndi kuliwononga lonjezolo.
[18] Ngati madalitso athu akudalira ntchito za lamulo ndiye kuti madalitsowo sakupatsidwa chifukwa cha lonjezo. Koma Mulungu mwachisomo chake anadalitsa Abrahamu kudzera mu lonjezo.
[19] Nanga tsono cholinga cha lamulo chinali chiyani? Linaperekedwa chifukwa cha zolakwa mpaka itafika mbewu imene lonjezo limanena. Malamulowo anaperekedwa ndi angelo kudzera mwa mʼkhalapakati.
[20] Ngakhale zili chomwecho, mʼkhalapakati sayimira mbali imodzi yokha, koma Mulungu ndi mmodzi.
[21] Kodi ndiye kuti lamulo limatsutsana ndi malonjezo a Mulungu? Ayi. Nʼkosatheka! Pakuti ngati tikanapatsidwa malamulo opatsa moyo ndiye kuti mwa lamulo tikanakhala olungama.
[22] Koma Malemba akunenetsa kuti dziko lonse lili mu ulamuliro wauchimo, kuti mwachikhulupiriro mwa Yesu Khristu, chimene chinalonjezedwa chiperekedwe kwa amene akhulupirira.
[23] Chikhulupiriro ichi chisanabwere, ife tinali mʼndende ya lamulo, otsekeredwa mpaka pamene chikhulupiriro chikanavumbulutsidwa.
[24] Choncho lamulo linayikidwa kukhala lotiyangʼanira kuti lititsogolere kwa Khristu kuti tilungamitsidwe mwachikhulupiriro.
[25] Tsopano pakuti chikhulupiriro chabwera, ife sitilinso mu ulamuliro wa lamulo.
[26] Nonse ndinu ana a Mulungu kudzera mʼchikhulupiriro mwa Khristu Yesu,
[27] pakuti nonse amene munalumikizana ndi Khristu mu ubatizo munavala Khristu.
[28] Palibe Myuda kapena Mgriki, kapolo kapena mfulu, mwamuna kapena mkazi, pakuti nonse ndinu amodzi mwa Khristu Yesu.
[29] Ngati inu muli ake a Khristu, ndiye kuti ndinu mbewu ya Abrahamu, ndi olowamʼmalo molingana ndi lonjezo.