[1] Pamaso pa Mulungu ndi pamaso pa Khristu Yesu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa omwe pamene adzaonekera ndi ufumu wake, ndikukulamula kuti:
[2] Lalikira Mawu; khala wokonzeka pa nthawi yake, ngakhale pamene si pa nthawi yake. Konza zolakwa zawo, dzudzula ndipo limbikitsa moleza mtima kwambiri ndi malangizo osamalitsa.
[3] Pakuti idzafika nthawi imene anthu adzakana chiphunzitso choona. Mʼmalo mwake, chifukwa chokhumba kumva zowakomera zokha, adzasonkhanitsa aphunzitsi ambiri omawawuza zimene iwo akufuna kumva.
[4] Sadzafuna kumva choona koma adzafuna kumva nthano chabe.
[5] Koma iwe, khala tcheru nthawi zonse, pirira mʼzovuta, gwira ntchito ya mlaliki, gwira ntchito zonse za utumiki wako.
[6] Pakuti moyo wanga wayamba kale kuthiridwa ngati nsembe, ndipo nthawi yakwana yoti ndinyamuke ulendo wanga.
[7] Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liwiro ndipo ndasunga chikhulupiriro.
[8] Tsopano mphotho yanga ikundidikira imene ndi chipewa cha chilungamo, imene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa pa tsiku lijalo, osati ine ndekha komanso onse amene akufunitsitsa kubwera kwake.
[9] Uyesetse kubwera kuno msanga.
[10] Paja Dema anandisiya chifukwa chokonda dziko lapansi lino, ndipo anapita ku Tesalonika. Kresike anapita ku Galatiya ndipo Tito anapita ku Dalimatiya.
[11] Ndatsala ndi Luka yekha basi. Mutenge Marko ndipo ubwere naye kuno, chifukwa amandithandiza mu utumiki wanga.
[12] Ndatumiza Tukiko ku Efeso.
[13] Pobwera, unditengere chofunda pamwamba chimene ndinachisiya kwa Kupro ku Trowa. Unditengerenso mabuku anga, makamaka aja azikopawa.
[14] Alekisandro, mmisiri wa zitsulo anandichitira zoyipa kwambiri. Ambuye adzamubwezera pa zimene anachita.
[15] Iwenso ukhale naye tcheru chifukwa anatsutsa kwambiri uthenga wathu.
[16] Podziteteza koyamba pa mlandu wanga, panalibe ndi mmodzi yemwe amene anandithandiza, koma aliyense anandithawa. Mulungu awakhululukire.
[17] Koma Ambuye anayima nane limodzi, ndipo anandipatsa mphamvu, kuti kudzera mwa ine, uthenga ulalikidwe kwambiri, ndikuti anthu a mitundu ina amve. Ndipo ndinalanditsidwa mʼkamwa mwa mkango.
[18] Ambuye adzandilanditsa ku chilichonse chofuna kundichita choyipa ndipo adzandisamalira bwino mpaka kundilowetsa chonse mu ufumu wake wakumwamba. Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya.
[19] Pereka moni kwa Prisila ndi Akura pamodzi ndi banja lonse la Onesiforo.
[20] Erasto anatsalira ku Korinto. Trofimo ndinamusiya akudwala ku Mileto.
[21] Uyesetse kubwera kuno nthawi yozizira isanafike. Eubulo akupereka moni, ndiponso Pude, Lino, Klaudiya ndi abale onse nawonso akupereka moni.
[22] Ambuye akhale ndi mzimu wako. Chisomo chikhale ndi inu nonse.