Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:31

[1] Koma dziwa izi: Mʼmasiku otsiriza kudzafika nthawi zoopsa kwambiri.

[2] Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, onyada, achipongwe, osamvera makolo awo, osayamika, wopanda chiyero.

[3] Adzakhala wopanda chikondi, osakhululuka, osinjirira, osadziletsa, ankhanza, osakonda zabwino,

[4] opereka anzawo kwa adani awo, osaopa zoyipa, odzitukumula, okonda zowasangalatsa mʼmalo mokonda Mulungu.

[5] Adzakhala ndi maonekedwe achipembedzo koma mphamvu yake ndi kumayikana. Anthu amenewa uziwapewa.

[6] Iwowa ndi anthu aja amene amayendayenda mʼmakomo a anthu nʼkumanyenga akazi ofowoka mʼmaganizo, olemedwa ndi machimo ndiponso otengeka ndi zilakolako zoyipa zamitundumitundu,

[7] amaphunzira nthawi zonse koma samatha kuzindikira choonadi.

[8] Monga momwe Yanesi ndi Yambere anawukira Mose, momwemonso anthu amenewa amawukira choonadi. Nzeru zawo ndi zowonongeka ndipo pa za chikhulupiriro, ndi okanidwa.

[9] Koma sadzapita nazo patali kwambiri zimenezi, pakuti anthu onse adzaona kupusa kwawo monga anachitira Yanesi ndi Yambere.

[10] Tsono iwe, umadziwa zonse zimene ndimaphunzitsa, makhalidwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, ndi kupirira kwanga,

[11] mazunzo anga, masautso anga, monga zinandichitikira ku Antiokeya, ku Ikoniya ndi ku Lusitra. Ndinazunzika kwambiri. Koma Ambuye anandipulumutsa pa zonsezi.

[12] Kunena zoona, munthu aliyense amene akufuna kukhala moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi,

[13] pomwe anthu oyipa ndi onyenga adzanka nayipirayipira, kunamiza ena, iwo nʼkumanamizidwanso.

[14] Koma iwe pitiriza zimene waziphunzira ndi kuzivomereza, chifukwa ukudziwa amene anakuphunzitsa zimenezi.

[15] Kuyambira uli wamngʼono wakhala ukudziwa Malemba Oyera, amene akhoza kukupatsa nzeru zokupulumutsa kudzera mʼchikhulupiriro cha mwa Yesu Khristu.

[16] Malemba onse anawalembetsa ndi Mulungu, ndipo othandiza pophunzitsa, podzudzula, pokonza cholakwika ndi polangiza za chilungamo

[17] kuti munthu wa Mulungu akonzekere bwino lomwe kugwira ntchito iliyonse yabwino.

Kalata Yachiwiri ya Paulo Yolembera Timoteyo — Chapters