Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:04

[1] Pamenepo anandionetsa Yoswa, mkulu wa ansembe, atayima pamaso pa mngelo wa Yehova, ndipo Satana anayima ku dzanja lake lamanja kuti atsutsane naye.

[2] Yehova anawuza Satana kuti, “Yehova akukudzudzula iwe Satana! Yehova amene wasankha Yerusalemu akukudzudzula! Kodi munthu uyu sali ngati chikuni choyaka chofumula pa moto?”

[3] Tsono Yoswa anali atavala zovala zalitsiro pa nthawi imene anayima pamaso pa mngelo.

[4] Mngelo uja anawuza anzake amene anali naye kuti, “Muvuleni zovala zake zalitsirizo.” Kenaka anawuza Yoswa kuti, “Taona, ndachotsa tchimo lako, ndipo ndikuveka zovala zokongola.”

[5] Ndipo ine ndinati, “Muvekeni nduwira yopatulika pamutu pake.” Choncho anamuveka nduwira yopatulika pamutu pake, namuvekanso zovala zatsopano. Nthawiyi nʼkuti mngelo wa Yehova atayima pambali.

[6] Mngelo wa Yehova analimbikitsa Yoswa kuti,

[7] “Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ngati uyenda mʼnjira zanga ndi kusunga malamulo anga, pamenepo udzalamulira nyumba yanga ndi kuyangʼanira mabwalo anga, ndipo ndidzakulolani kuti mudzakhale pamodzi ndi amene ali panowa.

[8] “ ‘Mvera tsono, iwe Yoswa mkulu wa ansembe, pamodzi ndi anzako amene wakhala nawowa, amene ndi chizindikiro cha zinthu zimene zikubwera: Ine ndidzabweretsa mtumiki wanga, wotchedwa Nthambi.

[9] Taona, mwala wokongola umene ndayika patsogolo pa Yoswa! Pa mwala umenewu pali maso asanu ndi awiri, ndipo Ine ndidzalembapo mawu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse, ‘ndipo ndidzachotsa tchimo la dziko lino tsiku limodzi.

[10] “ ‘Tsiku limenelo aliyense adzayitana mnzake kuti akhale pansi pa mtengo wamphesa ndi wa mkuyu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.”

Zekariya — Chapters