Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 7:53

[1] Ine ndikunena zoona mwa Khristu. Sindikunama ndipo chikumbumtima changa kudzera mwa Mzimu Woyera chikundichitira umboni.

[2] Ndili ndi chisoni chachikulu ndipo ndikumva kupwetekeka kosalekeza mu mtima mwanga.

[3] Pakuti ndikanafuna ine mwini nditatembereredwa ndi kuchotsedwa mwa Khristu chifukwa cha abale anga, amene ndi a mtundu wanga,

[4] anthu Aisraeli. Iwo anasankhidwa kukhala ana. Mulungu anawapatsa ulemerero, anachita nawo mapangano, kuwapatsa Malamulo, Nyumba yopembedzeramo ndi malonjezano ake.

[5] Awo ndi makolo athu. Kuchokera kwa iwo mʼthupi ndi kumene kunachokera makolo a Khristu Yesu amene ndi Mulungu wolamulira zinthu zonse, alemekezeke mpaka muyaya! Ameni.

[6] Sikuti mawu a Mulungu analephera. Pakuti si onse obadwa mwa Israeli amene ndi Israeli.

[7] Kapena kuti ana ake chifukwa anachokera mwa Abrahamu. Koma zidzukulu zako zidzachokera mwa Isake.

[8] Kutanthauza kuti, si ana obadwa mʼthupi amene ndi ana a Mulungu koma ndi ana a lonjezano amene amatengedwa kukhala zidzukulu za Abrahamu.

[9] Pakuti Mulungu analonjeza ponena kuti, “Pa nthawi yake ngati yomwe ino chaka chamawa ndidzabweranso, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”

[10] Ndipo si pokhapo ayi. Ana awiri a Rebeka aja abambo awo anali mmodzi, kholo lathu Isake.

[11] Komabe, ana amapasawa asanabadwe kapena asanachite chilichonse chabwino kapena choyipa, nʼcholinga choti chifuniro cha Mulungu chosankhiratu munthu aliyense chipitirire,

[12] osati chifukwa cha ntchito za munthu koma chifuniro cha Iye mwini, anawuza Rebeka kuti, “Wamkulu adzatumikira wamʼngʼono.”

[13] Monga momwe kwalembedwa kuti, “Ine ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau.”

[14] Nanga tsono tidzanena chiyani? Kodi Mulungu ndi osalungama? Ayi, ndi pangʼono pomwe!

[15] Pakuti Mulungu anawuza Mose kuti, “Ine ndidzachitira chifundo amene ndikufuna kumuchitira chifundo, ndipo ndidzakomera mtima amene ndikufuna kumukomera mtima.”

[16] Nʼchifukwa chake, izi sizitengera zokhumba za munthu kapena kuyesetsa koma chifundo cha Mulungu.

[17] Malemba akuti Mulungu anamuwuza Farao kuti, “Ine ndakuyika kukhala mfumu ndi cholinga choti ndionetse mphamvu zanga, kuti mwa iwe dzina langa litchuke pa dziko lonse lapansi.”

[18] Choncho Mulungu amachitira chifundo munthu amene akufuna kumuchitira chifundo ndipo amawumitsa mtima munthu amene Iye akufuna kumuwumitsa mtima.

[19] Tsono mmodzi wa inu nʼkundifunsa kuti, “Nanga nʼchifukwa chiyani Mulungu amatipeza olakwa? Nanga ndani amene amakana chifuniro chake?”

[20] Koma ndiwe yani, munthu wamba, woti nʼkutsutsana ndi Mulungu? “Kodi chimene chinawumbidwa nʼkufunsa amene anachiwumba kuti, ‘Kodi unandiwumbiranji motere?’ ”

[21] Kodi wowumba alibe ufulu wowumba kuchokera ku dothi lomwelo mbiya yamtengowapatali ndi ina yamtengo wotsika?

[22] Koma Mulungu, anafuna kuonetsa mkwiyo wake ndi kuti mphamvu yake idziwike. Iye anapirira modekha mtima kwambiri zochita za anthu omwe anawakwiyirawo amene anayeneradi chiwonongeko.

[23] Iye anachita izi kufuna kuonetsa kulemera kwa ulemerero wake ndi kuti udziwike kwa amene analandira chifundo chake. Iye anawakonzeratu kuti alandire ulemerero wake

[24] ngakhale ifenso amene anatiyitana osati kuchokera kwa Ayuda okha komanso kwa a mitundu ina.

[25] Monga momwe Mulungu akunenera mʼbuku la Hoseya kuti, “Amene sanali anthu anga ndidzawatcha ‘anthu anga;’ ndipo Ine ndidzatcha ‘wokondedwa wanga’ amene sali wokondedwa wanga,”

[26] ndipo, “Pamalo omwewo pamene ananena kuti, ‘Sindinu anthu anga,’ pomweponso adzawatchula kuti, ‘Ana a Mulungu wamoyo.’ ”

[27] Yesaya anafuwula za Aisraeli kuti, “Ngakhale chiwerengero cha Aisraeli chingakhale ngati mchenga wa ku nyanja, otsala okha ndiye adzapulumuke.

[28] Pakuti Ambuye adzagamula milandu ya anthu pa dziko lapansi mofulumira ndi kumaliziratu.”

[29] Monga momwe Yesaya ananena malo ena kuti, “Ngati Yehova Wamphamvuzonse akanapanda kutisiyira zidzukulu, ife tikanawonongeka ngati anthu a ku Sodomu, tikanakhala ngati anthu a ku Gomora.”

[30] Kodi nanga tidzati chiyani? Tidzati a mitundu ina amene sanafune chilungamo analandira chilungamo chachikhulupiriro

[31] koma Aisraeli, amene anafuna chilungamo cha lamulo sanachilandire.

[32] Chifukwa chiyani? Chifukwa iwo sanachifune ndi chikhulupiriro koma ngati mwa ntchito. Iwo anapunthwa pa “Mwala wopunthwitsa.”

[33] Monga momwe kwalembedwa kuti, “Taonani, Ine ndikuyika mwala mu Ziyoni wopunthwitsa anthu, thanthwe limene limagwetsa anthu. Koma amene akhulupirira Iye sadzachititsidwa manyazi.”

Kalata ya Paulo Yolembera Aroma — Chapters