Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 5:05

[1] Ndinaona pamene Mwana Wankhosa anatsekula chomatira choyamba cha zomatira zisanu ndi ziwiri zija. Ndipo ndinamva chimodzi mwa zamoyo zinayi zija chikunena liwu lomveka ngati bingu kuti, “Bwera!”

[2] Nditayangʼana patsogolo pake ndinaona kavalo woyera! Wokwerapo wake anali ndi uta ndipo anapatsidwa chipewa chaufumu, ndipo anatuluka kupita kukagonjetsa anthu ena.

[3] Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachiwiri, ndinamva chamoyo chachiwiri chija chikuti, “Bwera!”

[4] Pamenepo kavalo wina wofiira anatulukira. Wokwerapo wake anapatsidwa mphamvu yochotsa mtendere pa dziko lapansi ndi kuchititsa anthu kuti aziphana wina ndi mnzake. Iyeyu anapatsidwa lupanga lalikulu.

[5] Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachitatu, ndinamva chamoyo chachitatu chikuti, “Bwera!” Nditayangʼana patsogolo panga ndinaona kavalo wakuda! Wokwerapo wake anali ndi masikelo awiri mʼmanja mwake.

[6] Ndinamva ngati liwu kuchokera pakati pa zamoyo zinayi zija likuti, “Kilogalamu imodzi ya tirigu mtengo ndi malipiro a tsiku limodzi ndipo makilogalamu atatu a barele mtengo wake ndi malipiro a tsiku limodzi koma usawononge mafuta ndi vinyo!”

[7] Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachinayi, ndinamva chamoyo chachinayi chija chikunena kuti, “Bwera!”

[8] Nditayangʼana patsogolo panga ndinaona kavalo wotuwa! Wokwerapo wake dzina lake linali Imfa ndipo Hade inali kumutsatira pambuyo pake. Anapatsidwa ulamuliro pa gawo limodzi la magawo anayi a dziko lapansi kuti aphe ndi lupanga, njala, mliri, ndi zirombo zakuthengo za mʼdziko lapansi.

[9] Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachisanu, ndinaona kunsi kwa guwa lansembe kunali mizimu ya anthu amene anaphedwa chifukwa cha Mawu a Mulungu ndi chifukwa chochitira umboni.

[10] Iwo anafuwula kuti, “Mudzawaleka mpaka liti, Inu Ambuye wamkulu, woyera ndi woona, osawaweruza anthu okhala mʼdziko lapansi ndi kulipsira magazi athu?”

[11] Pamenepo aliyense wa anthuwo anapatsidwa mwinjiro woyera ndipo anawuzidwa kuti adikire pangʼono kufikira chiwerengero cha anzawo ndi abale awo amene anayeneranso kuphedwa ngati iwo, chitakwanira.

[12] Ndinayangʼanitsitsa pamene ankatsekula chomatira chachisanu ndi chimodzi. Ndipo panachitika chivomerezi champhamvu. Dzuwa linada ngati chiguduli chopanga ndi bweya wambuzi wakuda. Mwezi wonse unafiira ngati magazi,

[13] ndipo nyenyezi zakuthambo zinagwa pa dziko lapansi ngati muja zimagwera nkhuyu zotsalira mu mtengo mphepo yamphamvu ikawomba.

[14] Thambo linachoka ngati amayalulira mphasa ndipo phiri lililonse ndi chilumba chilichonse zinachotsedwa pa malo pake.

[15] Kenaka, mafumu a pa dziko lapansi, ana a mafumu, atsogoleri a ankhondo, olemera, amphamvu, kapolo aliyense, ndi mfulu aliyense anakabisala kumapanga ndi pakati pa matanthwe a ku mapiri.

[16] Iwo anafuwulira mapiri ndi matanthwe kuti, “Tigwereni ndi kutivundikira kuti asatione wokhala pa mpando waufumuyo ndi kupulumuka ku mkwiyo wa Mwana Wankhosa!

[17] Pakuti tsiku lalikulu la mkwiyo wawo lafika ndipo ndi ndani angathe kulimbapo?”

Chivumbulutso cha Yesu Khristu kwa Yohane — Chapters