Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 5:45

[1] Tsono abale anga, ndimakukondani ndipo ndikukulakalakani. Ndinu chimwemwe changa ndi chipewa cha ulemerero wanga. Abwenzi okondedwa, chilimikani choncho mwa Ambuye.

[2] Ndikudandaulira Euodiya ndi Suntuke kuti akhale ndi mtima umodzi mwa Ambuye.

[3] Inde, ndikupempha iwe mnzanga pa ntchitoyi, thandiza amayiwa amene ndagwira nawo ntchito ya Uthenga Wabwino pamodzi ndi Klementonso ndi ena onse antchito anzanga amene mayina awo ali mʼbuku lamoyo.

[4] Nthawi zonse muzikondwa mwa Ambuye. Ndikubwerezanso; muzikondwa!

[5] Kufatsa kwanu kuzioneka pamaso pa anthu onse. Ambuye anu ali pafupi.

[6] Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu.

[7] Ndipo mtendere wa Mulungu, umene upambana nzeru zonse udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

[8] Potsiriza, abale, muziyika mtima wanu pa zinthu zilizonse zabwino ndi zotamandika monga, zinthu zoona, zinthu zolemekezeka, zinthu zolungama, zinthu zoyera, zinthu zokongola ndi zinthu zosiririka.

[9] Muzichita chilichonse chimene mwaphunzira kapena kulandira kapena kumva kuchokera kwa ine kapena mwaona mwa ine. Ndipo Mulungu wamtendere adzakhala nanu.

[10] Ndikukondwa kwambiri mwa Ambuye kuti patapita nthawi tsopano mwayambanso kuonetsa kuti mumandiganizira. Zoonadi, mwakhala mukundikumbukira, koma munalibe mpata woti muonetsere zimenezi.

[11] Sindikunena izi chifukwa choti ndikusowa thandizo, poti ine ndaphunzira kukhala wokwaniritsidwa ndi zimene ndili nazo.

[12] Ndimadziwa kusauka nʼkutani, ndipo ndimadziwa kulemera nʼkutani. Ndaphunzira chinsinsi chokhala wokhutitsidwa mwa njira ina iliyonse, kaya nʼkudya bwino kapena kukhala ndi njala, kaya kukhala ndi chuma kapena umphawi.

[13] Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu.

[14] Komatu munachita bwino kundithandiza mʼmavuto anga.

[15] Ndipo inu Afilipi mukudziwa kuti masiku oyambirira olalikira Uthenga Wabwino, nditachoka ku Makedoniya, panalibe mpingo ndi umodzi omwe umene unagwirizana nane pa nkhani yopereka ndi kulandira, kupatula inu.

[16] Pakuti ngakhale pamene ndinali ku Tesalonika, munanditumizira kangapo zondithandiza pa zosowa zanga.

[17] Osati ndikufuna mphatso zanu, koma ndikufuna kuti pa zimene muli nazo pawonjezerekepo phindu.

[18] Ndalandira zonse ndipo ndili nazo zokwanira zoposa zosowa zanga popeza ndalandira kwa Epafrodito mphatso zochuluka zimene munatumiza. Ndizo zopereka za fungo labwino, nsembe zolandiridwa zokondweretsa Mulungu.

[19] Ndipo Mulungu wanga adzakwaniritsa zosowa zanu monga mwa chuma chake chaulemerero mwa Khristu Yesu.

[20] Kwa Mulungu ndi Atate athu, kukhale ulemerero mpaka muyaya. Ameni.

[21] Perekani moni kwa oyera mtima onse mwa Khristu Yesu. Abale amene ali ndi ine akupereka moni wawo.

[22] Oyera mtima onse akupereka moni, makamaka iwo a ku nyumba ya Kaisara.

[23] Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu. Ameni.

Kalata ya Paulo Yolembera Afilipi — Chapters