Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:19

[1] Yehova anawuza Mose kuti,

[2] “Yankhula ndi Aisraeli ndipo akupatse ndodo khumi ndi ziwiri, imodzi kuchokera kwa mtsogoleri wa fuko lililonse. Ulembe dzina la munthu aliyense pa ndodo yake.

[3] Pa ndodo ya Levi ulembepo dzina la Aaroni, chifukwa pafunika ndodo imodzi ya mtsogoleri pa fuko lililonse.

[4] Uyike ndodozo mu tenti ya msonkhano, kutsogolo kwa Bokosi la Umboni, kumene ndimakumana nawe.

[5] Ndodo ya munthu amene ndamusankha idzachita maluwa potero ndidzaletsa madandawulo osatha a Aisraeli otsutsana nawe.”

[6] Choncho Mose anayankhula ndi Aisraeli, ndipo atsogoleri awo anapereka ndodo khumi ndi ziwiri, imodzi kuchokera kwa mtsogoleri wa fuko lililonse ndipo ndodo ya Aaroni inali pakati pa ndodo zawozo.

[7] Mose anayika ndodozo pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano.

[8] Pa tsiku lotsatira Mose analowa mu tenti ya msonkhanoyo ndipo anaona kuti ndodo ya Aaroni, yomwe inkayimira fuko la Levi, sinangophuka masamba chabe, komanso inachita maluwa nʼkubala zipatso za alimondi.

[9] Choncho Mose anatulutsa ndodo zonse pamaso pa Yehova napita nazo kwa Aisraeli onse. Iwowo anaziona ndipo munthu aliyense anatenga ndodo yake.

[10] Yehova anawuza Mose kuti, “Bwezera ndodo ya Aaroni patsogolo pa Bokosi la Umboni, kuti chikhale chizindikiro cha kuwukira kwawo. Zimenezi zidzathetsa kudandaula kwawo kotsutsana nane, kuopa kuti angafe.”

[11] Mose anachita monga Yehova anamulamulira.

[12] Aisraeli anati kwa Mose, “Tikufa! Tatayika, tonse tatayika!

[13] Aliyense woyandikira chihema adzafa. Kodi ndiye kuti tonse tikufa?”

Numeri — Chapters