Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:03

[1] Tsoka kwa amene amakonzekera chiwembu, kwa amene amakonzekera kuchita zoyipa usiku pa mabedi awo! Kukacha mmawa amakachitadi chifukwa ali ndi mphamvu zochitira zimenezo.

[2] Amasirira minda ndi kuyilanda, amasirira nyumba ndi kuzilanda. Amatenga nyumba ya munthu mwachinyengo, munthu mnzawo kumulanda cholowa chake.

[3] Nʼchifukwa chake Yehova akuti, “Ine ndikukonzekera kubweretsa tsoka pa anthu awa, tsoka limene simudzatha kudzipulumutsa nokha. Inu simudzayendanso monyada, pakuti idzakhala nthawi ya masautso.

[4] Tsiku limenelo anthu adzakuchitani chipongwe; adzakunyogodolani ndi nyimbo iyi yamaliro: ‘Tawonongeka kotheratu; dziko la anthu anga lagawidwa. Iye wandilanda! Wapereka minda yathu kwa anthu otiwukira.’ ”

[5] Nʼchifukwa chake simudzakhala ndi munthu mu msonkhano wa Yehova kuti agawe dziko pochita maere.

[6] Aneneri awo amanena kuti, “Usanenere! Usanenere ndi pangʼono pomwe zimenezi; ife sitidzachititsidwa manyazi.”

[7] Inu nyumba ya Yakobo, monga zimenezi ndi zoyenera kuzinena: “Kodi Mzimu wa Yehova wakwiya? Kodi Iye amachita zinthu zotere?” “Kodi mawu ake sabweretsa zabwino kwa amene amayenda molungama?

[8] Posachedwapa anthu anga andiwukira ngati mdani. Mumawavula mkanjo wamtengowapatali anthu amene amadutsa mosaopa kanthu, monga anthu amene akubwera ku nkhondo.

[9] Mumatulutsa akazi a anthu anga mʼnyumba zawo zabwino. Mumalanda ana awo madalitso anga kosatha.

[10] Nyamukani, chokani! Pakuti ano si malo anu opumulirapo, chifukwa ayipitsidwa, awonongedwa, sangatheke kuwakonzanso.

[11] Ngati munthu wabodza ndi wachinyengo abwera nʼkunena kuti, ‘Ine ndidzanenera ndipo mudzakhala ndi vinyo ndi mowa wambiri, woteroyo adzakhala mneneri amene anthu awa angamukonde!’

[12] “Inu banja la Yakobo, ndidzakusonkhanitsani nonse; ndidzawasonkhanitsa pamodzi otsala a ku Israeli. Ndidzawabweretsa pamodzi ngati nkhosa mʼkhola, ngati ziweto pa msipu wake; malowo adzadzaza ndi chinamtindi cha anthu.

[13] Amene adzawapulumutse adzayenda patsogolo pawo; iwo adzathyola chipata ndipo adzatuluka. Mfumu yawo idzawatsogolera, Yehova adzakhala patsogolo pawo.”

Mika — Chapters