[1] Patapita nthawi Yesu anakwera kupita ku Yerusalemu ku phwando la Ayuda.
[2] Ndipo ku Yerusalemuko pafupi ndi chipata cha Nkhosa kuli dziwe limene mʼChihebri limatchedwa Betisaida ndipo ndi lozunguliridwa ndi makumbi asanu.
[3] Mʼmenemo munkagonamo gulu lalikulu la anthu odwala, osaona, olumala ndi ofa ziwalo.
[4] Pakuti nthawi zina mngelo wa Ambuye ankatsikira mʼdziwemo nʼkuvundula madziwo. Woyamba kulowamo madzi atavundulidwa, ankachira ngakhale akhale ndi nthenda yanji.
[5] Mmodzi wa amene anali pamenepo anali atadwala zaka 38.
[6] Yesu atamuona ali chigonere, nadziwa kuti anakhala chotero kwa nthawi yayitali, anamufunsa iye kuti,“Kodi ukufuna kuchira?”
[7] Wodwalayo anayankha kuti, “Ambuye, ndilibe wina aliyense woti angandithandize kulowa mʼdziwe pamene madzi avundulidwa. Pamene ndikuyesera kuti ndilowemo, wina amalowamo ine ndisanalowemo.”
[8] Ndipo Yesu anati kwa iye,“Imirira! Nyamula mphasa yako yamba kuyenda.”
[9] Nthawi yomweyo munthuyo anachiritsidwa. Iye ananyamula mphasa yake nayamba kuyenda. Tsiku limene izi zinachitika linali la Sabata.
[10] Ndipo Ayuda anati kwa munthu amene anachiritsidwayo, “Lero ndi la Sabata; lamulo silikulola iwe kunyamula mphasa yako.”
[11] Koma iye anayankha kuti, “Munthu amene wandichiritsa anati kwa ine,‘Nyamula mphasa yako yamba kuyenda.’ ”
[12] Pamenepo anamufunsa iye kuti, “Kodi munthu ameneyo ndani amene wakuwuza kuti, ‘Nyamula mphasa yako ndipo yenda?’ ”
[13] Munthu amene anachiritsidwayo sanadziwe kuti anali ndani, pakuti Yesu anangolowera mʼgulu la anthu ndi kupita.
[14] Patapita nthawi Yesu anamupeza ku Nyumba ya Mulungu ndipo anati kwa iye,“Taona uli bwino tsopano. Usakachimwenso kuti choyipa choposa ichi chingakugwere.”
[15] Munthu uja anachoka ndi kukawawuza Ayuda kuti anali Yesu amene anamuchiritsa iye.
[16] Ndipo popeza Yesu amachita zinthu izi tsiku la Sabata, Ayuda anayamba kumulondalonda.
[17] Yesu anawawuza kuti,“Atate anga amagwira ntchito nthawi zonse mpaka lero lino, ndipo Inenso ndili pa ntchito.”
[18] Chifukwa cha ichi Ayuda anawirikiza kufuna kumupha; osati chifukwa chakuswa Sabata kokha komanso chifukwa ankanena kuti Mulungu ndi Atate ake, nadziyesa Iye wofanana ndi Mulungu.
[19] Yesu anawapatsa yankho ili:“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Mwana sangathe kuchita kanthu pa Iye yekha. Iye amachita zokhazo zimene amaona Atate ake akuchita, chifukwa chilichonse chimene Atate amachita Mwana amachitanso.
[20] Pakuti Atate amakonda Mwana, amamuonetsa zonse zimene Iwo amachita. Inde, Atate adzamuonetsa zinthu zazikulu kuposa zimenezi ndipo mudzadabwa.
[21] Pakuti monga Atate amaukitsa akufa nawapatsa moyo, momwemonso Mwana amapereka moyo kwa amene Iye akufuna.
[22] Komanso, Atate saweruza aliyense koma wapereka kwa Mwana ulamuliro woweruzawo,
[23] kuti aliyense alemekeze Mwanayo monga momwe amalemekezera Atate. Munthu amene salemekeza Mwana salemekezanso Atate amene anamutuma Mwanayo.
[24] “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene amamva mawu anga ndi kukhulupirira Iye amene ananditumiza Ine, ali ndi moyo wosatha ndipo sadzaweruzidwa. Iye wachoka mu imfa ndipo walowa mʼmoyo.
[25] Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano, pamene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu ndipo iwo amene amva adzakhala ndi moyo.
[26] Pakuti monga Atate ali gwero la moyo, momwemonso anapereka mphamvu zopereka moyo mwa Mwana.
[27] Ndipo wamupatsa Iye ulamuliro woweruza chifukwa ndi Mwana wa Munthu.
[28] “Musadabwe ndi zimenezi. Pakuti nthawi ikubwera pamene onse amene ali mʼmanda adzamva mawu ake
[29] ndi kutuluka. Iwo amene anachita zabwino adzauka ndi kupita ku moyo wosatha ndipo amene anachita zoyipa adzauka ndi kupita ku chilango chamuyaya.
[30] Pakuti sindingathe kuchita kena kalikonse pa ndekha. Ine ndimaweruza molingana ndi zomwe Mulungu wandiwuza ndipo kuweruza kwanga ndi kolungama. Ine sindifuna kudzikondweretsa ndekha koma Iye amene anandituma.
[31] “Ngati ndidzichitira umboni ndekha, umboni wanga si woona.
[32] Alipo wina amene amandichitira umboni wabwino. Ine ndikudziwa kuti umboni wake wonena za Ine ndi woona.
[33] “Inu munatumiza amithenga kwa Yohane ndipo iye anachitira umboni choona.
[34] Sikuti Ine ndikudalira umboni wa munthu; koma ndikunena zimenezi kuti mupulumutsidwe.
[35] Yohane anali ngati nyale imene imayaka ndi kuwala, ndipo inu kwa kanthawi munasankha kusangalala ndi kuwala kwakeko.
[36] “Koma Ine ndili ndi umboni woposa uja wa Yohane. Pakuti ntchito imene Atate andipatsa kuti ndiyikwaniritse ndi imene ndikugwira, ndipo ikundichitira umboni kuti Atate andituma Ine.
[37] Ndipo Atate amene anandituma Ine, Iye mwini wandichitira umboni. Inu simunamvepo mawu ake kapena kuona maonekedwe ake,
[38] kapena mawu ake kukhala mwa inu, pakuti simukhulupirira Iye amene anamutuma.
[39] Inu mumasanthula malemba chifukwa mumaganiza kuti mʼmalembamo muli moyo wosatha. Awa ndi malemba amene akundichitira umboni.
[40] Koma inu mukukana kubwera kwa Ine kuti mukhale ndi moyo.
[41] “Ine sindilandira ulemu kuchokera kwa anthu
[42] koma Ine ndikukudziwani. Ndikudziwa kuti mʼmitima mwanu mulibe chikondi cha Mulungu.
[43] Ine ndabwera mʼdzina la Atate anga, ndipo inu simukundirandira Ine; koma wina wake akabwera mʼdzina la iye mwini, inu mudzamulandira.
[44] Kodi inu mudzakhulupirira bwanji ngati mumapatsana ulemu wina ndi mnzake, ndipo simufuna kulandira ulemu kuchokera kwa Mulungu yekhayo?
[45] “Koma inu musaganize kuti Ine ndidzakunenezani kwa Atate. Wokunenezani ndi Mose, amene inu mwayikapo chiyembekezo chanu.
[46] Ngati mukanakhulupirira Mose, mukanakhulupiriranso Ine, pakuti iye analemba za Ine.
[47] Koma ngati simukhulupirira zimene iye analemba, mudzakhulupirira bwanji zimene Ine ndikunena?”