[1] “Tsiku limenelo Debora ndi Baraki mwana wa Abinoamu anayimba nyimbo iyi:
[2] “Popeza kuti atsogoleri anatsogoleradi mʼdziko la Israeli; ndipo anthu anadzipereka okha mwa ufulu, tamandani Yehova:
[3] “Imvani inu mafumu! Tcherani khutu, atsogoleri inu! Ndidzayimba nyimbo, ndidzayimbira Yehova, Mulungu wa Israeli nyimbo yokoma.
[4] “Inu Yehova, pamene munkatuluka mu Seiri, pamene mumayenda kuchokera mʼdziko la Edomu, dziko linagwedezeka, mitambo inasungunuka nigwetsa madzi.
[5] Mapiri anagwedezeka pamaso pa Yehova, Mulungu wa Israeli.
[6] “Pa nthawi ya Samugara mwana wa Anati, pa nthawi ya Yaeli, misewu inasiyidwa; alendo ankangoyenda mʼtinjira takumbali.
[7] Anthu a ku midzi anathawa; mu Israeli munalibe midzi mpaka pamene iwe Debora unafika; unafika ngati mayi ku Israeli.
[8] Pamene anasankha milungu ina, nkhondo inabwera ku zipata za mzinda, ndipo chishango kapena mkondo sizinapezeke pakati pa anthu 40,000 mu Israeli.
[9] Mtima wanga uli ndi atsogoleri a Israeli, uli ndi anthu amene anadzipereka okha mwaufulu pakati pa anthu. Tamandani Yehova!
[10] “Inu okwera pa abulu oyera, okhala pa zishalo, ndi inu oyenda pa msewu, yankhulani.
[11] Ku zitsime, kutali ndi phokoso la a mauta; kumeneko akusimba za kuti Yehova wapambana; akusimba kuti Yehova walipsira anthu ake mu Israeli. “Choncho anthu a Yehova anasonkhana ku zipata za mzinda.
[12] Anati, ‘Tsogolera ndiwe, Debora, tsogolera; tsogolera ndiwe, tsogolera, imba nyimbo. Iwe Baraki! nyamuka Tsogolera akapolo ako, iwe mwana wa Abinoamu.’
[13] “Kenaka anthu okhulupirika anatsatira atsogoleri awo; anthu a Yehova anapita kukamenyera Yehova nkhondo kulimbana ndi adani amphamvu.
[14] Anakalowa mʼchigwa kuchokera ku Efereimu; akutsatira iwe Benjamini ndi abale ako. Akulu a ankhondo anachokera ku Makiri, ndipo onyamula ndodo ya udindo anachokera ku Zebuloni.
[15] Olamulira a Isakara anali pamodzi ndi Debora; inde, anthu ochokera ku Isakara anatsatanso Baraki, ndipo anathamangira ku chigwa akumutsatira. Koma pakati pa mafuko a Rubeni panali kusinkhasinkha mtima kwambiri osadziwa chenicheni choyenera kuchita.
[16] Chifukwa chiyani munangokhala ku makola a nkhosa nʼkumangomvetsera zitoliro zoyitanira nkhosa? Pakati pa anthu a fuko la Rubeni panali kusinkhasinkha mtima kwambiri osadziwa chenicheni choyenera kuti achite.
[17] Agiliyadi anatsala pa tsidya la Yorodani. Ndipo nʼchifukwa chiyani anthu afuko la Dani anatsarira mʼsitima za pa madzi? Aseri anali pa gombe la Nyanja; anangokhala mʼmadooko mwawo.
[18] Azebuloni ndi anthu amene anayika moyo wawo mʼzoopsa. Nawonso anthu a fuko la Nafutali anayika miyoyo yawo pa chiswe pomenya nkhondo pamwamba pa mapiri.
[19] “Mafumu anabwera, anachita nkhondo; mafumu Akanaani anachita nkhondo ku Tanaki pafupi ndi madzi a ku Megido, koma sanatengeko zofunkha zasiliva.
[20] Ngakhalenso nyenyezi zakumwamba zinachita nkhondo, zinathira nkhondo Sisera, zikuyenda mʼnjira zake.
[21] Mtsinje wa Kisoni unawakokolola, chigumula cha mtsinje wa Kisoni chinawakokolola. Mtima wanga, yenda mwamphamvu, limbika!
[22] Ndipo ziboda za ngʼombe zazimuna zinachita phokoso lalikulu, akavalo ali pa liwiro, akuthamanga kwambiri.
[23] Mngelo wa Yehova anati ‘Tembererani Merozi.’ ‘Tembererani nzika zake mwaukali, chifukwa sanabwere kudzathandiza Yehova, kulimbana ndi adani ake amphamvu.’
[24] “Akhale wodala kupambana akazi onse, Yaeli mkazi wa Heberi Mkeni; inde mwa akazi onse okhala mʼdziko, akhale wodala iyeyu.
[25] Munthu uja anapempha madzi akumwa, koma iye anamupatsa mkaka; anamupatsa chambiko mʼchikho cha wolemekezeka.
[26] Anatenga chikhomo cha tenti mʼdzanja lake, anatenganso nyundo ndi dzanja lake lamanja. Ndipo anakhoma nacho Sisera, anamuphwanya mutu wake, ndi kumubowola mu litsipa mwake.
[27] Anathifukira ku mapazi a mkaziyo nagwa, anagwa; iye anagona pamenepo. Anagwera pa mapazi a mkaziyo, iye anagwa; pamene anagwera, pamenepo anaferapo.
[28] “Amayi ake a Sisera anasuzumira pa zenera; nafuwula mokweza kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani galeta lake lachedwa kufika? Nʼchifukwa chiyani phokoso la magaleta ake silikumveka?’
[29] Amayi ake anzeru kwambiri anamuyankha, ndithudi, mwiniwake anadziyankha yekha kuti,
[30] ‘Kodi iwo sakufunafuna zofunkha kuti agawane; akugawana wankhondo aliyense mtsikana mmodzi kapena awiri. Sisera akumupatsa zofunkha: zovala zonyikidwa mu utoto, zoti ndizivala mʼkhosi zovala zopeta zonyika mu utoto, ndi zopeta zomavala mʼkhosi?’
[31] “Choncho Yehova! adani anu onse awonongeke, koma iwo amene amakukondani inu akhale ngati dzuwa pamene lituluka ndi mphamvu zake.” Ndipo dziko linakhala pa mtendere zaka makumi anayi.