[1] Abale anga, ambiri musakhale aphunzitsi chifukwa mumadziwa kuti aphunzitsife tidzaweruzidwa mowuma kuposa anthu ena onse.
[2] Tonsefe timapunthwa mʼnjira zambiri. Ngati wina salakwa poyankhula, ameneyo ndi munthu wangwiro, wodziwa kuyangʼanira bwino thupi lake lonse.
[3] Tikayika tizitsulo mʼkamwa mwa akavalo kuti atimvere, timatha kuwongolera thupi lake lonse.
[4] Taonani sitima zapamadzi. Ngakhale ndi zazikulu kwambiri ndipo zimakankhidwa ndi mphepo yamphamvu, zimawongoleredwa ndi tsigiro lalingʼono kulikonse kumene woyendetsayo akufuna kupita.
[5] Momwemonso, lilime ndi kachiwalo kakangʼono ka thupi koma limadzitama kuti nʼkuchita zikuluzikulu. Tangoganizirani za nkhalango yayikulu imene ingapse ndi kalawi kamoto koyamba mochepa.
[6] Lilime nalonso ndi moto, dziko la zoyipa pakati pa ziwalo za thupi. Limawononga munthu yense wathunthu. Limayika zonse za moyo wake pa moto, ndipo moto wake ndi wochokera ku gehena.
[7] Mitundu yonse ya nyama, ya mbalame, ya zokwawa ndi ya zolengedwa za mʼnyanja, zikuwetedwa ndipo munthu wakhala akuziweta,
[8] koma palibe munthu amene angaweta lilime. Lilime ndipo silitha kupuma, ndi lodzaza ndi ululu wakupha.
[9] Ndi lilime lomwelo timatamanda Ambuye ndi Atate athu, komanso ndi lilime lomwelo timalalatira anthu, amene anapangidwa mʼchifanizo cha Mulungu.
[10] Mʼkamwa momwemo mutuluka matamando ndi kulalata. Abale anga, zisamatero ayi.
[11] Kodi madzi abwino ndi a mchere angatuluke pa kasupe mmodzi?
[12] Abale anga, kodi mtengo wa mkuyu nʼkubala mphesa, kapena mtengo wampesa nʼkubala nkhuyu? Kasupe wa madzi a mchere sangatulutsenso madzi abwino.
[13] Ndani mwa inu amene ndi wanzeru ndi womvetsa zinthu? Mulekeni aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru ndiye zikutsogolera kudzichepetsa kwake ndi zochita zake
[14] Koma ngati muli ndi mtima wakaduka ndi odzikonda, musadzitamandire kapena kukana choonadi.
[15] “Nzeru” zotere sizochokera kumwamba koma ndi za mʼdziko lapansi, si zauzimu koma ndi za ziwanda.
[16] Pakuti pamene pali kaduka ndi kudzikonda pomweponso pamakhala chisokonezo ndi zochitika zoyipa zonse.
[17] Koma nzeru imene imachoka kumwamba, poyamba ndi yangwiro, ndi yokonda mtendere, yoganizira za ena, yogonjera, yodzaza ndi chifundo ndi chipatso chabwino, yosakondera ndi yoona mtima.
[18] Anthu amtendere amene amadzala mtendere amakolola chilungamo.