[1] Israeli anali mpesa wotambalala; anabereka zipatso zambiri. Pamene zipatso zawo zinanka zichuluka, anawonjezera kumanga maguwa ansembe. Pamene dziko lake linkatukuka, anakongoletsa miyala yake yopatulika.
[2] Mtima wawo ndi wonyenga ndipo tsopano ayenera kulangidwa chifukwa cha kulakwa kwawo. Yehova adzagumula maguwa awo ansembe ndi kuwononga miyala yawo yopatulika.
[3] Pamenepo anthuwo adzanena kuti, “Ife tilibe mfumu chifukwa sitinaope Yehova. Koma ngakhale tikanakhala ndi mfumu, kodi mfumuyo ikanatichitira chiyani?”
[4] Mafumu amalonjeza zambiri, amalumbira zabodza pochita mapangano. Kotero maweruzo amaphuka ngati zitsamba zakupha mʼmunda umene walimidwa.
[5] Anthu amene amakhala mu Samariya akuchita mantha chifukwa cha fano la mwana wangʼombe ku Beti-Aveni. Anthu ake adzalirira fanolo, chimodzimodzinso ansembe ake adamawo, amene anakondwera ndi kukongola kwake, chifukwa lachotsedwa pakati pawo ndi kupita ku ukapolo.
[6] Fanolo lidzatengedwa kupita ku Asiriya ngati mphatso kwa mfumu yayikulu. Efereimu adzachititsidwa manyazi chifukwa cha mafano ake amitengo.
[7] Samariya ndi mfumu yake adzatengedwa kupita kutali ngati kanthambi koyenda pa madzi.
[8] Malo opembedzerako mafano a ku Aveni adzawonongedwa. Ili ndiye tchimo la Israeli. Minga ndi mitungwi zidzamera ndi kuphimba maguwa awo ansembe. Kenaka anthu adzawuza mapiri kuti, “Tiphimbeni!” ndipo adzawuza zitunda kuti, “Tigwereni!”
[9] “Iwe Israeli, wachimwa kuyambira mʼmasiku a Gibeya, ndipo wakhala uli pomwepo. Kodi nkhondo sinagonjetse anthu ochita zoyipa ku Gibeya?
[10] Pamene ndifunire, ndidzalanga anthuwo; mitundu ya anthu idzasonkhanitsidwa kudzalimbana nawo, kuwayika mʼndende chifukwa cha uchimo wawo waukulu.
[11] Efereimu ndi mwana wangʼombe wamkazi wophunzitsidwa amene amakonda kupuntha tirigu, choncho Ine ndidzayika goli mʼkhosi lake lokongolalo. Ndidzasenzetsa Efereimu goli, Yuda ayenera kulima, ndipo Yakobo ayenera kutipula.
[12] Mufese nokha chilungamo ndipo mudzakolola chipatso cha chikondi changa chosasinthika. Ndipo tipulani munda wanu wosalimidwawo; pakuti ino ndi nthawi yofunafuna Yehova, mpaka Iye atabwera kudzakugwetserani mivumbi ya chilungamo.
[13] Koma inu munadzala zolakwa, mwakolola zoyipa; mwadya chipatso cha chinyengo. Chifukwa mumadalira mphamvu zanu ndiponso ankhondo anu ochulukawo,
[14] phokoso lankhondo lidzamveka pakati pa anthu anga kotero kuti malinga anu onse adzawonongeka, monga momwe Salimani anawonongera Beti-Aribeli pa nthawi ya nkhondo; pamene anapha amayi pamodzi ndi ana awo omwe.
[15] Momwemonso zidzakuchitikira, iwe Beteli chifukwa kuyipa kwako ndi kwakukulu. Tsiku limeneli likadzafika, mfumu ya Israeli idzawonongedwa kwathunthu.