Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 5:08

[1] Uthenga umene mneneri Habakuku analandira mʼmasomphenya.

[2] Kodi inu Yehova, ndidzakhala ndikukupemphani thandizo kwa nthawi yayitali motani, koma wosayankha? Kapena kufuwulira kwa inu kuti, “Chiwawa kuno!” koma wosatipulumutsa?

[3] Chifukwa chiyani mukundionetsa zinthu zoyipa? Chifukwa chiyani mukundionetsa mavutowa? Ndikuona chiwonongeko ndi chiwawa; pali ndewu ndi kukangana kwambiri.

[4] Kotero malamulo anu atha mphamvu, ndipo chilungamo sichikugwira ntchito. Anthu oyipa aposa olungama, kotero apotoza chilungamo.

[5] “Yangʼanani pakati pa mitundu ya anthu, ndipo penyetsetsani, ndipo muthedwe nazo nzeru. Pakuti ndidzachitadi zinthu pa nthawi yanu zimene inu simudzazikhulupirira, ngakhale wina atakufotokozerani.

[6] Pakuti taonani, Ine ndikuwutsa Ababuloni, anthu ankhanza ndiponso amphamvu, amene amapita pa dziko lonse lapansi kukalanda malo amene si awo.

[7] Iwowa ndi anthu ochititsa mantha, ndipo ndi owopsa; amadzipangira okha malamulo ndi kudzipezera okha ulemu.

[8] Akavalo awo ndi aliwiro kwambiri kupambana akambuku ndi owopsa kupambana mimbulu yolusa nthawi ya madzulo. Okwerapo awo akuthamanga molunjika; a pa akavalo awo ndi ochokera kutali, akuwuluka ngati chiwombankhanga chofuna kugwira nyama;

[9] onse akubwera atakonzekera zachiwawa. Gulu la ankhondo likubwera ngati mphepo ya mʼchipululu ndi kugwira akapolo ochuluka ngati mchenga.

[10] Akunyoza mafumu ndiponso kuchitira chipongwe olamulira. Akupeputsa mizinda yonse yotetezedwa; akumanga mitumbira ndi kulanda mizindayo.

[11] Kenaka amasesa mofulumira ngati mphepo nʼkumangopitirirabe, anthu ochimwa, amene mphamvu zawo ndiye mulungu wawo.”

[12] Inu Yehova, kodi sindinu wachikhalire? Mulungu wanga, Woyera wanga, ife sitidzafa. Inu Yehova, munawasankha anthuwo kuti abweretse chiweruzo; Inu Thanthwe, munawayika iwowo kuti atilange.

[13] Maso anu ndi oyera kwambiri safuna kuona choyipa; Inu simulekerera cholakwa. Chifukwa chiyani nanga mukulekerera anthu ochita zachinyengowa? Chifukwa chiyani muli chete pamene anthu oyipa akuwononga anthu olungama kupambana iwowo?

[14] Mwasandutsa anthu kukhala ngati nsomba zamʼnyanja, ngati zolengedwa zamʼnyanja zimene zilibe wolamulira.

[15] Mdani wawo woyipa amakoka anthu onse ndi mbedza, amawakola mu ukonde wake, amawasonkhanitsa mu khoka lake; kotero iyeyo amakondwa ndi kusangalala.

[16] Choncho iye amaperekera nsembe ukonde wake ndiponso kufukizira lubani khoka lake, popeza ukonde wakewo ndiye umamubweretsera moyo wapamwamba ndipo amadya chakudya chabwino kwambiri.

[17] Kodi iye azipitirabe kugwiritsa ntchito makoka akewo, kuwononga mitundu ya anthu mopanda chifundo?

Habakuku — Chapters