[1] Choncho, monga ana okondedwa, tsatirani chitsanzo cha Mulungu.
[2] Muzikondana monga Khristu anakonda ife nadzipereka yekha chifukwa cha ife monga chopereka cha fungo lokoma ndi nsembe kwa Mulungu.
[3] Koma pakati panu pasamveke nʼpangʼono pomwe zadama, kapena za mtundu wina uliwonse wa chodetsa, kapena za umbombo, chifukwa izi ndi zosayenera kwa anthu oyera a Mulungu.
[4] Musamatukwane, kuyankhula zopusa kapena kunena nthabwala zopanda pake, zomwe ndi zosayenera, koma mʼmalo mwake muziyamika.
[5] Dziwani ichi, palibe wadama, wochita zonyansa kapena waumbombo, munthu wotero ali ngati wopembedza mafano, amenewa alibe malo mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu.
[6] Musalole wina akunamizeni ndi mawu opanda pake, pakuti chifukwa cha zinthu ngati izi mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa amene samvera.
[7] Nʼchifukwa chake musamayanjane nawo anthu otere.
[8] Pajatu inu nthawi ina munali mdima, koma tsopano ndinu kuwunika mwa Ambuye. Mukhale ngati ana akuwunika
[9] (pakuti pamene pali kuwunika pamapezekaponso zabwino zonse, chilungamo ndi choonadi).
[10] Inu mufufuze chimene chimakondweretsa Ambuye.
[11] Musayanjane nazo ntchito zosapindulitsa za mdima, koma mʼmalo mwake muzitsutse.
[12] Pakuti ndi zochititsa manyazi ngakhale kutchula zomwe zimachitika mseri.
[13] Koma kuwala kumawunikira zinthu, ndipo chilichonse chimaonekera poyera. Choncho chilichonse choonekera poyera chimasandukanso kuwala.
[14] Nʼchifukwa chake Malemba akuti, “Dzuka, wamtulo iwe, uka kwa akufa, ndipo Khristu adzakuwalira.”
[15] Samalani makhalidwe anu, musakhale ngati opanda nzeru koma ngati anzeru.
[16] Gwiritsani ntchito mpata uliwonse, chifukwa masiku ano ndi oyipa.
[17] Choncho musakhale opusa, koma mudziwe zimene Ambuye akufuna kuti muchite.
[18] Musaledzere ndi vinyo, chifukwa adzawononga moyo wanu. Mʼmalo mwake, mudzazidwe ndi Mzimu Woyera.
[19] Muziyankhulana wina ndi mnzake mawu a Masalimo, nyimbo za Mulungu ndi nyimbo za uzimu. Muziyimbira Ambuye movomerezana ndi mitima yanu.
[20] Muziyamika Mulungu Atate nthawi zonse chifukwa cha zonse, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu.
[21] Gonjeranani wina ndi mnzake, kuonetsa kuopa Khristu.
[22] Inu akazi, muzigonjera amuna anu, monga mumagonjera kwa Ambuye.
[23] Pakuti mwamuna ndi mutu wa mkazi monga momwe Khristu ali mutu wa mpingo, thupi lake, limene Iyeyo ndi Mpulumutsi wake.
[24] Tsono monga mpingo umagonjera Khristu, momwemonso akazi akuyenera kugonjera amuna awo mu zonse.
[25] Inu amuna, kondani akazi anu monga momwe Khristu anakondera mpingo nadzipereka yekha mʼmalo mwa mpingowo
[26] kuti awupatule ukhale oyera, atawuyeretsa powusambitsa ndi madzi omwe ndi mawu ake.
[27] Anachita zimenezi kuti awupereke mpingowo kwa Iye mwini, mpingo wowala ndi waulemerero, wopanda banga kapena makwinya kapena chilema chilichonse, koma oyera ndi wangwiro.
[28] Momwemonso, amuna akuyenera kukonda akazi awo monga matupi awo. Iye amene akonda mkazi wake adzikondanso yekha.
[29] Pakuti palibe amene amadana nalo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulisamalira bwino, monga momwe Khristu amachitira ndi mpingo wake
[30] pakuti ndife ziwalo za thupi lake.
[31] “Pa chifukwa ichi, mwamuna adzasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.”
[32] Ichi ndi chinsinsi chozama, koma ine ndikunena za Khristu ndi mpingo.
[33] Chomwecho, aliyense mwa inu akuyenera kukonda mkazi wake monga adzikondera iye mwini, ndipo mkazi akuyenera kulemekeza mwamuna wake.