Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:36

[1] Mabwana, antchito anu muzikhala nawo mwachilungamo ndi moyenera, podziwa kuti nanunso muli nawo Ambuye anu mmwamba.

[2] Pempherani modzipereka, mukhale atcheru ndiponso oyamika.

[3] Ndipo muzitipemphereranso ife kuti Mulungu atitsekulire khomo la uthenga wathu, kuti tilalikire chinsinsi cha Khristu, chimene ndine womangidwa nacho mʼndende.

[4] Pempherani kuti ndilalikire momveka bwino, monga ndikuyenera.

[5] Mayendedwe anu pakati pa akunja, akhale anzeru ndipo mugwiritse ntchito mpata uliwonse umene muli nawo.

[6] Mayankhulidwe anu nthawi zonse akhale odzaza ndi chisomo ndi okoma, kuti mudziwe kuyankha aliyense.

[7] Tukiko adzakuwuzani zonse za ine. Iye ndi mʼbale wokondedwa, mtumiki wokhulupirika ndiponso wantchito mnzanga mwa Ambuye.

[8] Ine ndikumutumiza kwa inu ndi cholinga choti mudziwe zimene tikukumana nazo ndiponso kuti alimbikitse mitima yanu.

[9] Iye akubwera ndi Onesimo, mʼbale wathu wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ndi mmodzi mwa inu. Iwo adzakuwuzani zonse zimene zikuchitika kuno.

[10] Aristariko, wamʼndende mnzanga akupereka moni, Marko akuperekanso moni, msuweni wa Barnaba. (Inu munawuzidwa kale za Iye. Iye akabwera kwanuko, mulandireni).

[11] Yesu wotchedwa Yusto, akuperekanso moni. Amenewa ndi Ayuda okhawo pakati pa atumiki anzanga mu ufumu wa Mulungu, ndipo aonetsa kuti ndi chitonthozo kwa ine.

[12] Epafra ndi mmodzi mwa inu ndiponso mtumiki wa Khristu Yesu, akupereka moni. Iyeyu nthawi zonse amakupemphererani mwamphamvu, kuti mukhazikike pa chifuniro chonse cha Mulungu, mukhale okhwima ndi otsimikiza kwathunthu.

[13] Ine ndikumuchitira umboni kuti amagwira ntchito mwamphamvu chifukwa cha inu ndiponso kwa amene ali ku Laodikaya ndi Herapoli.

[14] Luka, dotolo wathu wokondedwa ndi Dema, akupereka moni.

[15] Perekani moni kwa abale a ku Laodikaya, ndiponso kwa Numfa ndi mpingo wa mʼnyumba mwake.

[16] Kalata iyi ikawerengedwa pakati panu, muonetsetse kuti ikawerengedwenso ku mpingo wa ku Laodikaya ndipo inunso muwerenge kalata yochokera ku Laodikaya.

[17] Uzani Arkipo kuti, “Wonetsetsa kuti wamaliza ntchito imene unayilandira mwa Ambuye.”

[18] Ine Paulo, ndikulemba ndi dzanja langa moni uwu. Kumbukirani kuti ndili mu unyolo. Chisomo chikhale ndi inu.

Kalata ya Paulo Yolembera Akolose — Chapters