Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 7:15

[1] Israeli, imva mawu awa, nyimbo ya maliro imene ndikuyimba za iweyo:

[2] “Namwali Israeli wagwa, moti sadzadzukanso, wasiyidwa mʼdziko lake lomwe, popanda woti ndi kumudzutsa.”

[3] Ambuye Yehova akuti, “Mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 1,000 amphamvu udzatsala ndi anthu 100 okha; mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 100 amphamvu udzatsala ndi anthu khumi okha basi.”

[4] Zimene Yehova akunena kwa nyumba ya Israeli ndi izi: “Mundifunefune kuti mukhale ndi moyo;

[5] musafunefune Beteli, musapite ku Giligala, musapite ku Beeriseba. Pakuti Giligala adzatengedwa ndithu kupita ku ukapolo, ndipo Beteli adzawonongekeratu.”

[6] Funani Yehova kuti mukhale ndi moyo, mukapanda kutero Iye adzatentha nyumba ya Yosefe ngati moto; motowo udzawononga, ndipo sipadzakhala wina wozimitsa motowo ku Beteli.

[7] Inu amene mumasandutsa chiweruzo cholungama kukhala chowawa ndi kunyoza chilungamo.

[8] (Iye amene analenga nyenyezi za Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, amene amasandutsa mdima kuti ukhale mmawa ndi kudetsa usana kuti ukhale usiku, amene amayitana madzi a mʼnyanja ndi kuwathira pa dziko lapansi, Yehova ndiye dzina lake.

[9] Iyeyo amabweretsa chiwonongeko modzidzimutsa pa anthu amphamvu ndi kuwononga mizinda yotetezedwa),

[10] inu mumadana ndi amene amadzudzula mʼbwalo la milandu ndi kunyoza amene amanena zoona.

[11] Mumapondereza munthu wosauka ndi kumukakamiza kuti akupatseni tirigu. Nʼchifukwa chake, ngakhale mwamanga nyumba zamiyala yosema, inuyo simudzakhalamo. Ngakhale mwalima minda yabwino ya mphesa, inu simudzamwa vinyo wake.

[12] Pakuti Ine ndikudziwa kuchuluka kwa zolakwa zanu ndi kukula kwa machimo anu. Inu mumapondereza anthu olungama ndi kulandira ziphuphu ndipo anthu osauka simuwaweruza mwachilungamo mʼmabwalo anu amilandu.

[13] Nʼchifukwa chake pa nthawi yotere munthu wanzeru sayankhulapo kanthu, popeza ndi nthawi yoyipa.

[14] Muyike mtima wanu pa zabwino osati pa zoyipa, kuti mukhale ndi moyo. Mukatero Yehova Mulungu Wamphamvuzonse adzakhala nanu, monga mmene mumanenera kuti ali nanu.

[15] Mudane ndi zoyipa, mukonde zabwino; mukhazikitse chiweruzo cholungama mʼmabwalo anu amilandu. Mwina mwake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse adzachitira chifundo anthu otsala a mʼbanja la Yosefe.

[16] Choncho izi ndi zimene Ambuye, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, akunena: “Mʼmisewu monse mudzakhala kulira mofuwula, ndi kulira chifukwa cha kuwawa kwa masautso kudzakhala paliponse. Adzayitana alimi kuti adzalire, ndipo anthu odziwa maliridwe anthetemya adzalira mofuwula.

[17] Mʼminda yonse ya mpesa mudzakhala kulira kokhakokha, pakuti Ine ndidzadutsa pakati panu,” q4 akutero Yehova.

[18] Tsoka kwa inu amene mumalakalaka tsiku la Yehova! Chifukwa chiyani mumalakalaka tsiku la Yehova? Tsikulo kudzakhala mdima osati kuwala.

[19] Lidzakhala ngati tsiku limene munthu pothawa mkango amakumana ndi chimbalangondo, ngati pamene munthu walowa mʼnyumba, natsamira dzanja lake pa khoma ndipo njoka nʼkuluma.

[20] Kodi tsiku la Yehova silidzakhala mdima osati kuwala, mdima wandiweyani, popanda powala pena paliponse?

[21] “Ndimadana nawo masiku anu achikondwerero ndipo ndimawanyoza; sindikondwera nayo misonkhano yanu.

[22] Ngakhale mupereke nsembe zopsereza ndi nsembe zachakudya, Ine sindidzazilandira. Ngakhale mupereke nsembe zabwino zachiyanjano, Ine sindidzaziyangʼana nʼkomwe.

[23] Musandisokose nazo nyimbo zanu! Sindidzamvetsera kulira kwa azeze anu.

[24] Koma chiweruzo cholungama chiyende ngati madzi, chilungamo ngati mtsinje wosaphwa!

[25] “Kodi pa zaka makumi anayi zimene munakhala mʼchipululu muja munkandibweretsera nsembe ndi zopereka, inu nyumba ya Israeli?

[26] Inu mwanyamula kachisi wa mfumu yanu, ndi nyenyezi ija Kaiwani, mulungu wanu, mafano amene munadzipangira.

[27] Nʼchifukwa chake Ine ndidzakupititsani ku ukapolo, kutali kupitirira ku Damasiko,” akutero Yehova, amene dzina lake ndi Mulungu Wamphamvuzonse.

Amosi — Chapters