Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 7:35

[1] Pamene Petro ndi Yohane amayankhula ndi anthu, kunabwera ansembe, mkulu woyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndiponso Asaduki.

[2] Iwo anakhumudwa kwambiri chifukwa atumwiwo amaphunzitsa anthu ndi kumalalikira za kuuka kwa akufa mwa Yesu.

[3] Iwo anagwira Petro ndi Yohane, popeza kunali kutada, anawayika mʼndende mpaka mmawa mwake.

[4] Koma anthu ambiri amene anamva uthenga anakhulupirira, ndipo chiwerengero cha anthu chinakwana 5,000.

[5] Mmawa mwake olamulira, akulu ndi aphunzitsi a malamulo anasonkhana mu Yerusalemu.

[6] Panali Anasi, Mkulu wa ansembe, Kayafa, Yohane ndi Alekisandro ndi ana a banja la mkulu wa ansembe.

[7] Iwo anayimiritsa Petro ndi Yohane patsogolo pawo nayamba kuwafunsa kuti, “Kodi munachita zimenezi ndi mphamvu yanji kapena mʼdzina la yani?”

[8] Petro wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anawawuza kuti, “Inu olamulira ndi akulu!

[9] Ngati ife tikufunsidwa lero chifukwa cha ntchito yabwino imene yachitika pa munthu wolumala miyendo ndi mmene iye anachiritsidwira,

[10] tsono dziwani izi inu ndi aliyense mu Israeli: munthuyu akuyima pamaso panu, wochiritsidwa kwathunthu, ndi chifukwa cha dzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti amene munamupachika koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa.

[11] Iye ndi “ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana, umenewo wasanduka mwala wa pa ngodya!’

[12] Chipulumutso sichipezeka mwa wina aliyense; pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo limene lapatsidwa kwa anthu limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.”

[13] Ataona kulimba mtima kwa Petro ndi Yohane ndi kuzindikira kuti anali osaphunzira, anthu wamba, anadabwa kwambiri ndipo anazindikira kuti anthuwa anakhala pamodzi ndi Yesu.

[14] Koma popeza iwo amamuona munthu amene anachiritsidwa atayima pamodzi ndi iwo, palibe chimene akananena.

[15] Chifukwa chake anawalamula kuti atuluke mʼbwalo la milandu ndipo akulu abwalowo anayamba kukambirana.

[16] Iwo anafunsana kuti, “Kodi anthuwa tichite nawo chiyani? Pakuti aliyense okhala mu Yerusalemu akudziwa kuti achita chodabwitsachi, ndipo ife sitingathe kukana.

[17] Koma kuti mbiriyi isapitirire kuwanda pakati pa anthu, ife tiwachenjeze anthu amenewa kuti asayankhulenso kwa wina aliyense mʼdzina la Yesu.”

[18] Pamenepo anawayitananso ndipo anawalamula kuti asayankhule kapena kuphunzitsa konse mʼdzina la Yesu.

[19] Koma Petro ndi Yohane anayankha kuti, “Weruzani nokha ngati nʼkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu.

[20] Ife sitingaleke kuyankhula za zimene tinaziona ndi kuzimva.”

[21] Atawonjeza kuwaopseza anawamasula. Sanathe kugwirizana njira yowalangira, chifukwa anthu onse amayamika Mulungu chifukwa cha zimene zinachitika.

[22] Ndipo munthu amene anachiritsidwayo anali ndi zaka makumi anayi.

[23] Atamasulidwa Petro ndi Yohane anapita kwa anzawo ndipo anawafotokozera zonse zimene akulu a ansembe ndi akulu anawawuza.

[24] Anthu atamva zimenezi anafuwula ndi mtima umodzi napemphera kwa Mulungu. Iwo anati, “Ambuye wolamulira zonse, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndiponso zonse zili mʼmenemo.

[25] Inu munayankhula mwa Mzimu Woyera kudzera pakamwa pa Davide kholo lathu, mtumiki wanu kuti, “ ‘Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu, ndipo akonzekera kuchita zopandapake?

[26] Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo; ndipo olamulira asonkhana pamodzi kulimbana ndi Ambuye ndi wodzozedwa wakeyo.’

[27] Zoonadi, Herode ndi Pontiyo Pilato anasonkhana pamodzi ndi amitundu ndiponso Aisraeli, mu mzinda muno, kupanga zolimbana ndi mtumiki wanu woyera Yesu, amene Inu munamudzoza.

[28] Iwo anachita zimene munakonzeratu mwachifuniro chanu ndi mphamvu yanu kuti zichitike.

[29] Tsopano, Ambuye taonani kuti atiopseza, tithandizeni ife atumiki anu, kuti tiyankhule mawu anu molimba mtima.

[30] Tambasulani dzanja lanu kuchiritsa anthu ndipo kuti, zizindikiro zodabwitsa zichitike mʼdzina la mtumiki wanu woyera Yesu.”

[31] Iwo atatha kupemphera, malo amene anasonkhanapo anagwedezeka. Ndipo iwo onse anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo anayankhula Mawu a Mulungu molimba mtima.

[32] Okhulupirira onse anali a mtima umodzi, ndi maganizo amodzi. Palibe munthu amene amati zomwe anali nazo zinali zake zokha, koma amagawana chilichonse chimene anali nacho.

[33] Atumwi anapitirira kuchitira umboni mwa mphamvu zakuuka kwa Ambuye Yesu, ndipo pa iwo panali chisomo chochuluka.

[34] Panalibe anthu osowa kanthu pakati pawo. Pakuti amene anali ndi malo, kapena nyumba amagulitsa ndi kubweretsa ndalamazo

[35] ndi kuzipereka kwa atumwi, ndipo zimagawidwa kwa aliyense amene anali ndi chosowa.

[36] Yosefe, wa fuko la Levi, wochokera ku Kupro amene atumwi anamutcha Barnaba, kutanthauza kuti mwana wachilimbikitso,

[37] anagulitsa munda wake ndipo anadzapereka ndalamazo kwa atumwi.

Machitidwe a Atumwi — Chapters