Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:33

[1] Potsiriza, abale, mutipempherere kuti uthenga wa Ambuye ufalikire msanga ndi kulemekezedwa monga momwe munachitira inu.

[2] Ndipo pempherani kuti tilanditsidwe mʼmanja mwa anthu ovuta ndi oyipa, pakuti si onse amene ali nacho chikhulupiriro.

[3] Koma Ambuye ndi wokhulupirika, ndipo adzakulimbikitsani ndi kukutetezani kwa woyipayo.

[4] Tili ndi chikhulupiriro mwa Ambuye kuti mukuchita zonse ndipo mudzapitirira kuchita zimene tinakulamulirani.

[5] Ambuye atsogolere mitima yanu kuti mudziwe chikondi cha Mulungu ndiponso kupirira kumene Khristu amapereka.

[6] Abale, tikukulamulani mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, kuti mupewe mʼbale aliyense amene ndi waulesi ndi wachisokonezo, wosafuna kutsata zimene tinakuphunzitsani.

[7] Pakuti inu mukudziwa zimene muyenera kuchita pofuna kutitsatira. Ife sitinali alesi pamene tinali nanu

[8] ndipo sitinadye chakudya cha aliyense osalipira. Komatu tinkagwira ntchito mwamphamvu usiku ndi usana kuti tisakhale cholemetsa kwa aliyense.

[9] Sitinachite zimenezi chifukwa choti tinalibe mphamvu zolamula kuti mutithandize koma kuti tikhale chitsanzo choti mutsatire.

[10] Pakuti ngakhale pamene tinali nanu, tinakupatsani lamulo lakuti, “Munthu wosafuna kugwira ntchito, asadye.”

[11] Ife tikumva kuti pakati panu pali ena amene ndi alesi. Iwo safuna kugwira ntchito, koma amangolowerera pa za eni.

[12] Mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, tikuwalamula ndi kuwakakamiza kuti azigwira ntchito mwabata ndi kumadya chakudya chodzigwirira ntchito okha.

[13] Koma inu abale, musatope nʼkuchita zabwino.

[14] Ngati wina aliyense akana kumvera malangizo athu a mʼkalatayi, mumuonetsetse ameneyo ndipo musayanjane naye kuti achite manyazi.

[15] Komatu musamutenge kukhala mdani, koma muchenjezeni ngati mʼbale.

[16] Tsopano Ambuye mwini mtendere akupatseni mtendere nthawi zonse mwa njira iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse.

[17] Ine Paulo, ndikulemba malonje awa ndi dzanja langa, chimene ndi chizindikiro chodziwika mʼmakalata anga onse. Umo ndi mmene ndimalembera.

[18] Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.

Kalata Yachiwiri ya Paulo Yolembera Atesalonika — Chapters