[1] Davide anayimbira Yehova nyimbo iyi pamene Yehovayo anamupulumutsa mʼdzanja la adani ake onse ndiponso mʼdzanja la Sauli.
[2] Iye anati, “Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga.
[3] Mulungu wanga ndiye thanthwe langa, mʼmene ndimathawiramo, chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa. Iye ndi linga langa, pothawirapo panga ndi mpulumutsi wanga. Munandipulumutsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.
[4] “Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando, ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga.
[5] “Mafunde a imfa anandizinga; mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri.
[6] Anandimanga ndi zingwe za ku manda; misampha ya imfa inalimbana nane.
[7] “Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova; ndinapemphera kwa Mulungu wanga. Iye ali mʼnyumba yake, anamva mawu anga; kulira kwanga kunafika mʼmakutu ake.
[8] “Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi, maziko a miyamba anagwedezeka; ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya.
[9] Mʼmphuno mwake munatuluka utsi; moto wonyeketsa unatuluka mʼkamwa mwake, makala amoto anali lawilawi mʼkamwa mwake.
[10] Iye anangʼamba thambo natsika pansi; pansi pa mapazi ake panali mitambo yakuda.
[11] Iye anakwera pa Kerubi ndi kuwuluka; nawuluka ndi mphepo mwaliwiro.
[12] Iye anapanga mdima kukhala chofunda chake, mitambo yakuda ya mlengalenga.
[13] Mʼkuwala kumene kunali pamaso pake munkachokera makala amoto alawilawi.
[14] Yehova anabangula kumwamba ngati bingu, mawu a Wammwambamwamba anamveka ponseponse.
[15] Iye anaponya mivi yake, nabalalitsa adani ake, ndi zingʼaningʼani zake anawagonjetsa.
[16] Zigwa za mʼnyanja zinaonekera poyera, ndipo maziko a dziko lapansi anakhala poyera, Yehova atabangula mwaukali, pamene mpweya wamphamvu unatuluka mʼmphuno mwake.
[17] “Ali kumwamba, Iye anatambalitsa dzanja lake ndipo anandigwira; anandivuwula mʼmadzi ozama.
[18] Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu, adani anga amene anali amphamvu kuposa ine.
[19] Adaniwo analimbana nane pamene ndinali pa mavuto, koma Yehova anali thandizo langa.
[20] Iye anandipititsa kumalo otakasuka; anandipulumutsa chifukwa amakondwera nane.
[21] “Yehova wandithandiza molingana ndi chilungamo changa; molingana ndi makhalidwe anga abwino, Iye wandipulumutsa.
[22] Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova; ndilibe mlandu wochoka pamaso pa Mulungu wanga.
[23] Malamulo ake onse ali pamaso panga, sindinasiye malangizo ake.
[24] Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pake ndipo ndakhala ndi kupewa tchimo.
[25] Yehova wandipatsa mphotho molingana ndi chilungamo changa, molingana ndi makhalidwe anga abwino pamaso pake.
[26] “Kwa wokhulupirika, Inu mumaonetsa kukhulupirika kwanu, kwa anthu amakhalidwe abwino, Inu mumaonetsanso makhalidwe abwino,
[27] Kwa woyera mtima, Inu mumaonetsa kuyera mtima kwanu, koma kwa anthu achinyengo mumaonetsanso kunyansidwa nawo.
[28] Inu mumapulumutsa anthu odzichepetsa, koma maso anu amatsutsana ndi odzikuza ndipo mumawatsitsa.
[29] Inu Yehova, ndinu nyale yanga; Yehova wasandutsa mdima wanga kukhala kuwunika.
[30] Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo, ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu.
[31] “Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro; mawu a Yehova alibe cholakwika. Iye ndi chishango kwa onse amene amathawira kwa iye.
[32] Mulungu wina ndi uti wofanana nanu Yehova? Ndipo ndani amene ndi Thanthwe kupatula Mulungu wathu?
[33] Ndi Mulungu amene anandipatsa mphamvu ndi kulungamitsa njira yanga.
[34] Iye amasandutsa mapazi anga kukhala ngati ambawala yayikazi; Iye amandithandiza kuyimirira pamwamba pa mapiri.
[35] Iye amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo; manja anga amatha kuthyola uta wachitsulo.
[36] Inu mundipatsa ine chishango chanu cha chigonjetso; mumawerama kuti mundikweze.
[37] Inu mwalimbitsa njira yanga kuti ndiyende bwino, kuti mapazi anga asaterereke.
[38] “Ine ndinathamangitsa adani anga ndi kuwakantha; sindinabwerere mpaka iwo atawonongedwa.
[39] Ndinawakantha kotheratu, ndipo sanathe kudzukanso; Iwo anagwera pansi pa mapazi anga.
[40] Inu munandipatsa ine mphamvu yochitira nkhondo; munagwaditsa adani anga pa mapazi anga.
[41] Inu muchititsa kuti adani anga atembenuke ndi kuthawa; ndipo ndinawononga adani anga.
[42] Iwo anafuwula kupempha thandizo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe owapulumutsa. Analirira kwa Yehova, koma sanawayankhe.
[43] Ine ndinawaperesa ngati fumbi la pa dziko lapansi; ndinawasinja ndipo ndinawapondaponda ngati matope a mʼmisewu.
[44] “Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa mitundu ya anthu; Inu mwandisunga kuti ndikhale mtsogoleri wa anthu a mitundu ina. Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga.
[45] Alendo amadzipereka okha pamaso panga; akangomva za ine, amandigonjera.
[46] Iwo onse anataya mtima; anatuluka mʼmalinga awo akunjenjemera.
[47] “Yehova ndi wamoyo! Litamandidwe Thanthwe langa. Akuzike Mulungu, Thanthwe, Mpulumutsi wanga!
[48] Iye ndi Mulungu amene amabwezera chilango, amene amayika anthu a mitundu yonse pansi pa ulamuliro wanga,
[49] amene amandimasula mʼmanja mwa adani anga. Inu munandikuza kuposa adani anga; munandilanditsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.
[50] Choncho ine ndidzakutamandani Inu Yehova, pakati pa anthu a mitundu ina; ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu.
[51] “Iye amapereka chipambano chachikulu kwa mfumu yake, amaonetsa kukoma mtima kwa wodzozedwa wake, kwa Davide ndi zidzukulu zake kwamuyaya.”