Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:48

[1] Yehosafati mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake ndipo anadzilimbitsa pofuna kulimbana ndi Israeli.

[2] Iye anayika magulu a asilikali mʼmizinda yonse yotetezedwa ya Yuda, ndipo anamanga maboma mu Yuda ndi mʼmizinda yonse ya Efereimu imene Asa abambo ake analanda.

[3] Yehova anali ndi Yehosafati chifukwa mʼzaka zoyambirira anatsatira makhalidwe a Davide abambo ake. Iye sanafunsire kwa Abaala.

[4] Koma anafunafuna Mulungu wa abambo ake ndipo anatsatira malamulo ake osati zochita za Israeli.

[5] Yehova anakhazikitsa kolimba ufumuwo mʼmanja mwake ndipo Ayuda onse anabweretsa mphatso kwa Yehosafati, kotero kuti anali ndi chuma ndi ulemu wambiri.

[6] Mtima wake anawupereka kutsatira Yehova, kuwonjezera apo, anachotsa malo onse achipembedzo ndi mafano a Asera mu Yuda.

[7] Mʼchaka chachitatu cha ufumu wake, iye anatuma akuluakulu ake Beni-Haili, Obadiya, Zekariya, Netaneli ndi Mikaya kukaphunzitsa mʼmizinda ya Yuda.

[8] Pamodzi ndi iwo panali Alevi ena: Semaya, Netaniya, Zebadiya, Asaheli, Semiramoti, Yonatani, Adoniya, Tobiya ndi Tobu-Adoniya ndiponso ansembe Elisama ndi Yehoramu.

[9] Iwo anaphunzitsa mu Yuda monse atatenga Buku la Malamulo a Yehova iwo anayenda mʼmizinda yonse ya ku Yuda ndipo anaphunzitsa anthu.

[10] Kuopsa kwa Yehova kunali pa maufumu onse a mayiko oyandikana ndi Yuda, kotero kuti sanachite nkhondo ndi Yehosafati.

[11] Afilisti ena anabweretsa kwa Yehosafati mphatso ndi siliva ngati msonkho, ndipo Aarabu anabweretsa ziweto: nkhosa zazimuna 7,700 ndi mbuzi 7,700.

[12] Mphamvu za Yehosafati zinkakulirakulira. Iye anamanga malo otetezedwa ndi mizinda yosungiramo chuma mu Yuda

[13] ndipo anali ndi katundu wambiri mʼmizinda ya Yuda. Iye anayikanso asilikali odziwa bwino nkhondo mu Yerusalemu.

[14] Chiwerengero chawo potsata mabanja awo chinali chotere: kuchokera ku Yuda, atsogoleri a magulu 1,000; mtsogoleri Adina, anali ndi anthu 300,000 odziwa nkhondo;

[15] otsatana naye, mtsogoleri Yehohanani, anali ndi anthu 280,000;

[16] otsatana naye, Amasiya mwana wa Zikiri amene anadzipereka yekha kutumikira Yehova, anali ndi anthu 200,000.

[17] Kuchokera ku Benjamini: Eliada, msilikali wolimba mtima, anali ndi anthu 200,000 amene anali ndi mauta ndi zishango;

[18] otsatana naye, Yehozabadi, anali ndi anthu 180,000 okonzekera nkhondo.

[19] Awa ndi anthu amene ankatumikira mfumu osawerengera amene anawayika mʼmizinda yotetezedwa mʼdziko lonse la Yuda.

2 Mbiri — Chapters