Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:23

[1] Tsono choyamba ndikukupemphani kuti mupempherere anthu onse. Mapemphero anu akhale opemba, opempha, opempherera ena ndi oyamika.

[2] Mupempherere mafumu ndi onse aulamuliro, kuti tikhale moyo wamtendere ndi bata, woopa Mulungu ndi oyera mtima.

[3] Izi ndi zabwino ndipo zimakondweretsa Mulungu Mpulumutsi wathu,

[4] amene amafuna kuti anthu onse apulumutsidwe ndipo kuti adziwe choonadi.

[5] Pakuti pali Mulungu mmodzi yekha ndi Mʼkhalapakati mmodzi yekha pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja Khristu Yesu.

[6] Iyeyu anadzipereka kukhala dipo lowombolera anthu onse. Umenewu ndi umboni umene waperekedwa mu nthawi yake yoyenera.

[7] Nʼchifukwa chake anandisankha kukhala mlaliki ndiponso mtumwi wophunzitsa anthu a mitundu ina mawu achikhulupiriro choona. Sindikunama ayi, ndikunena zoona.

[8] Choncho ndikufuna kuti paliponse popemphera, amuna azikweza manja awo kwa Mulungu mopanda mkwiyo kapena kukangana.

[9] Ndikufunanso kuti amayi azivala mwaulemu, modzilemekeza ndi moyenera. Adzikongoletse koma osati ndi tsitsi loluka mowonjeza muyeso kapena zokongoletsa zagolide kapena mikanda yamtengowapatali kapena ndi zovala zamtengowapatali.

[10] Koma adzikongoletse ndi ntchito zabwino zoyenera mayi wopembedza Mulungu.

[11] Amayi azikhala chete pophunzitsidwa ndi mtima ogonjera kwathunthu.

[12] Ine sindikulola kuti amayi aziphunzitsa kapena kulamulira amuna; koma akhale chete.

[13] Pakuti Adamu ndiye anayamba kupangidwa kenaka Hava.

[14] Ndipo Adamu si amene ananyengedwa koma mkazi ndiye amene ananyengedwa nachimwa.

[15] Ndipo mkazi adzapulumutsidwa pobereka mwana ngati apitiriza kukhala mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkuyera mtima pamodzi ndi kudzichepetsa konse.

Kalata Yoyamba ya Paulo Yolembera Timoteyo — Chapters